1Mau a Yehova amene anadza kwa Zefaniya mwana wa Kusi, mwana wa Gedaliya, mwana wa Amariya, mwana wa Hezekiya, masiku a Yosiya, mwana wa Amoni mfumu ya Yuda.
2Kuzitha ndidzazitha zonse kuzichotsa panthaka, ati Yehova.
3Ndidzatha munthu ndi nyama; ndidzatha mbalame za m'mlengalenga, ndi nsomba za m'nyanja, ndi zokhumudwitsa pamodzi ndi oipa; ndipo ndidzaononga anthu kuwachotsa panthaka, ati Yehova.
42Maf. 23.4-5Ndipo ndidzatambasulira dzanja langa pa Yuda, ndi pa onse okhala m'Yerusalemu; ndipo ndidzaononga otsala a Baala kuwachotsa m'malo muno, ndi dzina la Akemari pamodzi ndi ansembe;
5ndi iwo akulambira khamu la kumwamba pamwamba pa matsindwi; ndi iwo akulambira, akulumbira pali Yehova, nalumbiranso pali mfumu;
6Yes. 1.4ndi iwo akubwerera osamtsata Yehova; ndi osamfuna Yehova, kapena kufunsira kwa Iye.
7Yes. 13.6; 34.6; Hab. 2.20Khala chete pamaso pa Ambuye Yehova; pakuti tsiku la Yehova liyandikira; pakuti Yehova wakonzeratu nsembe, anapatula oitanidwa ake.
8Ndipo kudzachitika tsiku la nsembe ya Yehova, kuti ndidzalanga akalonga ndi ana a mfumu, ndi onse akuvala chovala chachilendo.
9Ndipo tsiku ilo ndidzalanga olumpha chiundo, nadzaza nyumba ya mbuye wao ndi chiwawa ndi chinyengo.
10Ndipo tsiku ilo, ati Yehova, kudzakhala phokoso lakulira lochokera kuchipata chansomba, ndi kuchema kochokera kudera lachiwiri, ndi kugamuka kwakukulu kochokera kuzitunda.
11Chemani okhala m'chigwa, pakuti amalonda onse atayika, onsewo osenza siliva aonongeka.
12Ndipo kudzachitika nthawi yomweyi kuti ndidzasanthula Yerusalemu ndi nyali, ndipo ndidzalanga amunawo okhala ndi nsenga, onena m'mtima mwao, Yehova sachita chokoma, kapena kuchita choipa.
13Amo. 5.11Ndipo zolemera zao zidzakhala zakufunkhidwa; ndi nyumba zao zabwinja; adzamangadi nyumba, koma sadzagonamo; adzaoka minda yampesa koma sadzamwa vinyo wake.
14Yow. 2.1, 11Tsiku lalikulu la Yehova lili pafupi, lili pafupi lifulumira kudza, mau a tsiku la Yehova; munthu wamphamvu adzalirapo mowawa mtima.
15Yes. 22.5Tsikulo ndi tsiku la mkwiyo, tsiku la msauko ndi lopsinja tsiku la bwinja, ndi chipasuko, tsiku la mdima ndi la chisisira, tsiku la mitambo ndi lakuda bii;
16tsiku la lipenga ndi lakufuulira midzi yamlinga, ndi nsanja zazitali za kungodya.
17Deut. 28.29Ndipo ndidzatengera anthu zowapsinja, kuti adzayenda ngati anthu akhungu, popeza anachimwira Yehova; ndi mwazi wao udzatsanulidwa ngati fumbi, ndi nyama yao idzanga ndowe.
18Miy. 11.4; Ezk. 7.19Ngakhale siliva wao, ngakhale golide wao sizidzakhoza kuwalanditsa tsiku la mkwiyo wa Yehova; koma dziko lonse lidzatha ndi moto wa nsanje yake; pakuti adzachita chakutsiriza, mofulumira, onse okhala m'dziko.
Who We AreWhat We EelieveWhat We Do
2025 by iamachristian.org,Inc All rights reserved.