MASALIMO 79 - Buku Lopatulika Bible 2014

Yerusalemu apasuka, apempha Mulungu awathandizeSalimo la Asafu.

1 2Maf. 25.9-10 Mulungu, akunja alowa m'cholandira chanu;

anaipsa Kachisi wanu woyera;

anachititsa Yerusalemu bwinja.

2 Deut. 28.26 Anapereka mitembo ya atumiki anu ikhale

chakudya cha mbalame za mlengalenga,

nyama ya okondedwa anu anaipereka kwa zilombo za m'dziko.

3 Yer. 14.16 Anakhetsa mwazi wao ngati madzi pozungulira Yerusalemu;

ndipo panalibe wakuwaika.

4Takhala chotonza cha anansi athu,

ndi choseketsa ndi cholalatitsa iwo akutizinga.

5 Mas. 74.1 Yehova, mudzakwiya nthawi zonse kufikira liti?

Nidzatentha nsanje yanu ngati moto?

6 Yer. 10.25; Chiv. 16.1 Thirirani mkwiyo wanu pa akunja osadziwa Inu,

ndi pa maufumu osaitana pa dzina lanu.

7Pakuti anathera Yakobo,

napasula pokhalira iye.

8 Yes. 64.9 Musakumbukire motitsutsa mphulupulu za makolo athu;

nsoni zokoma zanu zitipeze msanga,

pakuti tafooka kwambiri.

9 2Mbi. 14.11 Tithandizeni Mulungu wa chipulumutso chathu,

chifukwa cha ulemerero wa dzina lanu;

ndipo tilanditseni, ndi kutifafanizira zoipa zathu,

chifukwa cha dzina lanu.

10 Mas. 42.10 Anenerenji amitundu, Ali kuti Mulungu wao?

Kubwezera chilango cha mwazi wa atumiki anu umene anaukhetsa

kudziwike pakati pa amitundu pamaso pathu.

11 Eks. 3.7; Mas. 102.20 Kubuula kwa wandende kufike kuli Inu;

monga mwa mphamvu yanu yaikulu lolani ana a imfa atsale.

12 Yes. 65.6-7 Ndipo anansi athu amene anatonza Inu

muwabwezere chotonza chao,

kasanu ndi kawiri kumtima kwao, Ambuye.

13 Mas. 95.7 Potero ife anthu anu ndi nkhosa zapabusa panu

tidzakuyamikani kosatha;

tidzafotokozera chilemekezo chanu ku mibadwomibadwo.

Blog
About Us
Message
Site Map

Who We AreWhat We EelieveWhat We Do

Terms of UsePrivacy Notice

2025 by iamachristian.org,Inc All rights reserved.

Home
Gospel
Question
Blog
Help