1Ndipo Elihu anabwereza kunena, nati,
2Kodi muchiyesa choyenera,
umo mukuti, Chilungamo changa chiposa cha Mulungu,
3pakuti munena, Upindulanji nacho?
Posachimwa ndinapindula chiyani
chimene sindikadapindula pochimwa?
4Ndidzakuyankhani,
ndi anzanu pamodzi ndi inu.
5Yang'anani kumwamba, nimuone,
tapenyani mitambo yokwera yakuposa inu.
6 Miy. 8.36; Yer. 7.19 Ngati mwachimwa, mumchitira Iye chiyani?
Zikachuluka zolakwa zanu, mumchitira Iye chiyani?
7 Aro. 11.35 Mukakhala wolungama, mumninkhapo chiyani?
Kapena alandira chiyani pa dzanja lanu?
8Choipa chanu chikhoza kuipira munthu wonga inu,
ndi chilungamo chanu chikhoza kukomera wobadwa ndi munthu.
9 Eks. 2.23 Chifukwa cha kuchuluka masautso anthu anafuula,
afuula chifukwa cha dzanja la amphamvu.
10 Mas. 42.8 Koma palibe anganene, Ali kuti Mulungu Mlengi wanga,
wakupatsa nyimbo usiku;
11wakutilangiza ife koposa nyama za padziko,
wakutipatsa nzeru zoposa mbalame za m'mlengalenga?
12Apo afuula, koma Iye sawayankha;
chifukwa cha kudzikuza kwa anthu oipa.
13 Yer. 11.11 Zedi Mulungu samvera zachabe,
ndi Wamphamvuyonse sazisamalira.
14 Mas. 37.5-6 Inde mungakhale munena, Sindimpenya,
mlanduwo uli pamaso pake, ndipo mumlindira.
15Ndipo tsopano popeza analibe kumzonda m'kukwiya kwake,
ndi kusamalitsa cholakwa,
16chifukwa chake Yobu anatsegula pakamwa pake mwachabe,
nachulukitsa mau opanda nzeru.
Who We AreWhat We EelieveWhat We Do
2025 by iamachristian.org,Inc All rights reserved.