1Ndipo Yehova ananena ndi Mose, ndi kuti,
2Nena ndi Aroni ndi ana ake amuna, kuti azikhala padera ndi zinthu zopatulika za ana a Israele, zimene amandipatulira Ine, ndipo asaipse dzina langa loyera; Ine ndine Yehova.
3Nena nao, Aliyense wa mbeu zanu zonse mwa mibadwo yanu, akayandikiza zinthu zopatulika, zimene ana a Israele azipatulira Yehova, pokhala ali nacho chomdetsa chake, azimsadza munthuyo pankhope panga; Ine ndine Yehova.
4Munthu aliyense wa mbeu za Aroni wokhala ndi khate, kapena kukha, asadyeko zinthu zopatulika, kufikira atayera. Ndipo aliyense wokhudza chinthu chodetsedwa ndi wakufa, kapena mwamuna wogona uipa;
5ndi aliyense wokhudza chinthu chokwawa chakudetsedwa nacho, kapenanso munthu amene akamdetsa nacho, chodetsa chake chilichonse;
6munthu wokhudza chilichonse chotere adzakhala wodetsedwa kufikira madzulo, ndipo asadye zinthu zopatulika, akapanda kusamba thupi lake ndi madzi.
7Koma litalowa dzuwa, adzakhala woyera, ndi pambuyo pake adyeko zoyerazo, popeza ndizo chakudya chake.
8Lev. 17.15Asamadya zakufa zokha, kapena zojiwa, kudzidetsa nazo; Ine ndine Yehova.
9Potero asunge chilangizo changa, angasenzepo uchimo, ndi kufera m'mwemo, pakuchiipsa; Ine ndine Yehova wakuwapatula iwo.
10Mlendo asadyeko chopatulikacho; wakungokhala, ndi wansembe, kapena wolembedwa ntchito, asadyeko chopatulikacho.
11Koma wansembe atakagula munthu ndi ndalama zake, iyeyu adyeko; ndi iwo amene anabadwa m'nyumba yake, adyeko mkate wake.
12Ndipo mwana wamkazi wa wansembe akakwatibwa ndi mlendo, asadyeko nsembe yokweza ya zinthu zopatulika.
13Koma mwana wamkazi wa wansembe akakhala wamasiye kapena wochotsedwa, ndipo alibe mwana, nabwerera kunyumba ya atate wake, monga muja anali mwana, adyeko mkate wa atate wake; koma mlendo asamadyako.
14Ndipo munthu akadyako chinthu chopatulika mosadziwa, azionjezapo limodzi la magawo asanu, nalipereke kwa wansembe, pamodzi ndi chopatulikacho.
15Potero asaipse zinthu zopatulika za ana a Israele, zopereka iwo kwa Yehova;
16ndi kuwasenzetsa mphulupulu yakuwapalamulitsa, pakudya iwo zopatulika zao; pakuti Ine ndine Yehova wakuwapatula.
Za nsembe zaufulu17Ndipo Yehova ananena ndi Mose, ndi kuti,
18Nena ndi Aroni, ndi ana ake amuna, ndi ana onse a Israele, nuti nao, Aliyense wa mbumba ya Israele, kapena wa alendo ali m'Israele, akabwera nacho chopereka chake, monga mwa zowinda zao zonse, kapena monga mwa zopereka zaufulu zao, zimene abwera nazo kwa Yehova zikhale nsembe zopsereza;
19kuti mulandiridwe, azibwera nayo yaimuna yopanda chilema, ya ng'ombe, kapena nkhosa kapena mbuzi.
20Deut. 15.21Musamabwera nayo yokhala ndi chilema; popeza siidzalandirikira inu.
21Lev. 21.17; 22.2Ndipo munthu akabwera nayo nsembe yoyamika kwa Yehova, ya pa chowinda chachikulu, kapena ya pa chopereka chaufulu, ya ng'ombe kapena nkhosa, ikhale yangwiro kuti ilandirike; ikhale yopanda chilema.
22Musamabwera nazo kwa Yehova yakhungu, kapena yoduka mwendo, kapena yopunduka, kapena yafundo, kapena yausemwe, kapena ya usemwe waukulu, musamazipereka kwa Yehova nsembe zamoto pa guwa la nsembe.
23Ng'ombe kapena nkhosa yokula kapena yochepa chiwalo, ikhale nsembe yaufulu; koma pa chowinda siidzalandirika.
24Nyama yofula, kapena chopwanya kapena chosansantha, kapena chotudzula, kapena chodula, musamabwera nazo kwa Yehova; inde musamachita ichi m'dziko mwanu.
25Ndipo musamazilandira izi ku dzanja la mlendo ndi kubwera nazo zikhale chakudya cha Mulungu wanu; popeza zili nako kuvunda kwao; zili ndi chilema; sizidzalandirikira inu.
26Ndipo Yehova ananena ndi Mose, ndi kuti,
27Zikamabadwa ng'ombe kapena nkhosa, kapena mbuzi, zikhale ndi make masiku asanu ndi awiri; kuyambira tsiku lachisanu ndi chitatu ndi m'tsogolo mwake, idzalandirika ngati chopereka nsembe yamoto ya Yehova.
28Koma musamaipha ng'ombe kapena nkhosa pamodzi ndi mwana wake tsiku limodzimodzi.
29Ndipo mukamaphera Yehova nsembe yoyamika, muiphere kuti mulandirike.
30Idyedwe tsiku lomwelo; musamasiyako kufikira m'mawa; Ine ndine Yehova.
31Potero muwasunge malamulo anga, ndi kuwachita; Ine ndine Yehova.
32Musamaipsa dzina langa loyera; koma ndikhale woyera pakati pa ana a Israele; Ine ndine Yehova wakukupatulani,
33amene ndinakutulutsani m'dziko la Ejipito, kuti ndikhale Mulungu wanu; Ine ndine Yehova.
Who We AreWhat We EelieveWhat We Do
2025 by iamachristian.org,Inc All rights reserved.