1Ndipo Yehova ananena ndi Mose, ndi kuti,
2Lev. 13Uza ana a Israele kuti azitulutsa m'chigono akhate onse, ndi onse akukhala nako kukha, ndi odetsedwa chifukwa cha akufa;
3muwatulutse amuna ndi akazi muwatulutsire kunja kwa chigono, kuti angadetse chigono chao, chimene ndikhala m'kati mwakemo.
4Ndipo ana a Israele anachita chotero, nawatulutsira kunja kwa chigono; monga Yehova adanena ndi Mose momwemo ana a Israele anachita.
Za kubwezera5Ndipo Yehova ananena ndi Mose, nati,
6Nena ndi ana a Israele, ndi kuti Mwamuna kapena mkazi akachita tchimo lililonse amachita anthu, kuchita mosakhulupirika pa Yehova, nakapalamuladi;
7Lev. 6.5; Yos. 7.19azivomereza tchimo lake adalichita; nabwezere chopalamulacho monsemo, naonjezeko limodzi la magawo asanu, ndi kuchipereka kwa iye adampalamulayo.
8Koma munthuyo akapanda kukhala nayo nkhoswe imene akaibwezere chopalamulacho, chopalamula achibwezera Yehovacho chikhale cha wansembe; pamodzi ndi nkhosa yamphongo ya chotetezerapo, imene amchitire nayo chomtetezera.
9Ndipo nsembe zokweza zonse za zinthu zopatulika za ana a Israele, zimene abwera nazo kwa wansembe zisanduka zake.
10Zopatulika za munthu aliyense ndi zake: zilizonse munthu aliyense akapatsa wansembe, zasanduka zake.
Za mlandu wa nsanje11Ndipo Yehova ananena ndi Mose, nati,
12Nena ndi ana a Israele, nuti nao, Mkazi wa mwini akapatukira mwamuna wake, nakamchitira mosakhulupirika,
13ndi munthu akagona naye, koma kumbisikira maso a mwamuna wake, ndi kumng'unira; nadetsedwa mkaziyo, koma palibe mboni yomtsutsa, kapena sanamgwire alimkuchita;
14ndipo ukamgwira mwamuna mtima wansanje, kuti achitire nsanje mkazi wake, popeza wadetsedwa; kapena ukamgwira mtima wansanje, kuti amchitire mkazi wake nsanje angakhale sanadetsedwe;
151Maf. 17.18pamenepo mwamunayo azidza naye mkazi wake kwa wansembe, nadze nacho chopereka chake, limodzi la magawo khumi la efa wa ufa wabarele; asathirepo mafuta, kapena kuikapo lubani; popeza ndiyo nsembe yaufa yansanje, nsembe yaufa yachikumbutso, yakukumbutsa mphulupulu.
16Ndipo wansembe abwere naye, namuike pamaso pa Yehova;
17natenge madzi opatulika m'mbale yadothi wansembeyo, natengeko fumbi lili pansi m'Kachisi, wansembeyo nalithire m'madzimo.
18Pamenepo wansembeyo aike mkaziyo pamaso pa Yehova, navula mutu wa mkaziyo, naike nsembe yaufa yachikumbutso m'manja mwake, ndiyo nsembe yaufa yansanje; ndipo m'manja mwake mwa wansembe muzikhala madzi owawa akudzetsa temberero.
19Ndipo wansembe amlumbiritse, nanene kwa mkazi, Ngati sanagone nawe munthu mmodzi yense, ngati sunapatukira kuchidetso, pokhala ndiwe wa mwamuna wako, upulumuke ku madzi owawa awa akudzetsa temberero.
20Koma iwe, ngati wapatukira mwamuna wako, ngati wadetsedwa, kuti wagona nawe munthu, wosati mwamuna wako;
21pamenepo wansembe alumbiritse mkazi lumbiro lakutemberera, ndi wansembe anene kwa mkazi, Yehova akuike ukhale temberero ndi lumbiro pakati pa anthu a mtundu wako, pakuondetsa Yehova m'chuuno mwako, ndi kukutupitsa thupi lako;
22ndipo madzi awa akudzetsa temberero adzalowa m'matumbo mwako, nadzakutupitsa thupi lako ndi kuondetsa m'chuuno mwako; ndipo mkaziyo aziti, Amen, Amen.
23Ndipo wansembe alembere matemberero awa m'buku, ndi kuwafafaniza ndi madzi owawawa.
24Ndipo amwetse mkaziyo madzi owawa akudzetsa temberero; ndi madzi odzetsa temberero adzalowa mwa iye nadzamwawira.
25Ndipo wansembe atenge nsembe yaufa yansanje m'manja mwa mkazi, naweyule nsembe yaufa pamaso pa Yehova, nabwere nayo ku guwa la nsembe.
26Wansembe atengekonso nsembe yaufa wodzala manja, chikumbutso chake, nachitenthe pa guwa la nsembe; ndipo atatero amwetse mkazi madziwo.
27Ndipo atammwetsa madziwo, kudzatero, ngati wadetsedwa, nachita mosakhulupirika pa mwamuna wake, madzi odzetsa tembererowo adzalowa mwa iye nadzamwawira, nadzamtupitsa thupi lake, ndi m'chuuno mwake mudzaonda; ndi mkaziyo adzakhala temberero pakati pa anthu a mtundu wake.
28Koma ngati mkazi sanadetsedwe, nakhala woyera, pamenepo adzapulumuka, nadzaima.
29Ichi ndi chilamulo cha nsanje, pamene mkazi, pokhala naye mwamuna wake, ampatukira nadetsedwa;
30kapena pamene mtima wansanje umgwira mwamuna, ndipo achitira mkazi wake nsanje; pamenepo aziika mkazi pamaso pa Yehova, ndipo wansembe amchitire chilamulo ichi chonse.
31Mwamunayo ndiye wosachita mphulupulu, koma mkazi uyo asenze mphulupulu yake.
Who We AreWhat We EelieveWhat We Do
2025 by iamachristian.org,Inc All rights reserved.