1 Akol. 2.17; Aheb. 9.9 Pakuti chilamulo, pokhala nao mthunzi wa zokoma zilinkudza, osati chifaniziro chenicheni cha zinthuzo, sichikhozatu, ndi nsembe zomwezi chaka ndi chaka, zimene azipereka kosalekeza, kuwayesera angwiro iwo akuyandikira.
2Pakadapanda kutero, kodi sakadaleka kuzipereka, chifukwa otumikirawo sakadakhala nacho chikumbu mtima cha machimo, popeza adayeretsedwa kamodzi?
3Komatu mu izizo muli chikumbukiro cha machimo chaka ndi chaka.
4Mik. 6.6-7; Aheb. 9.13Pakuti sikutheka kuti mwazi wa ng'ombe zamphongo, ndi mbuzi ukachotsera machimo.
5Mas. 40.6-8Mwa ichi polowa m'dziko lapansi, anena,
Nsembe ndi chopereka simunazifuna,
koma thupi munandikonzera Ine.
6Nsembe zopsereza zamphumphu ndi za kwa machimo
simunakondwera nazo;
7pamenepo ndinati, Taonani, ndafika,
(Pamutu pake pa buku palembedwa za Ine)
kudzachita chifuniro chanu, Mulungu.
8Pakunena pamwamba apa, kuti, Nsembe ndi zopereka ndi nsembe zopsereza zamphumphu ndi za kwa machimo simunazifuna, kapena kukondwera nazo (zimene ziperekedwa monga mwa lamulo),
9pamenepo anati, Taonani, ndafika kudzachita chifuniro chanu. Achotsa choyambacho, kuti akaike chachiwiricho.
10Yoh. 17.19; Aheb. 9.12Ndi chifuniro chimenecho tayeretsedwa mwa chopereka cha thupi la Yesu Khristu, kamodzi, kwatha.
11Aheb. 7.27; 10.4Ndipotu wansembe aliyense amaima tsiku ndi tsiku, natumikira, napereka nsembe zomwezi kawirikawiri, zimene sizikhoza konse kuchotsa machimo;
12Aheb. 1.3koma Iye, m'mene adapereka nsembe imodzi chifukwa cha machimo, anakhala pa dzanja lamanja la Mulungu chikhalire;
13Mas. 110.1kuyambira pomwepo alindirira, kufikira adani ake aikidwa akhale mpando kumapazi ake.
14Aheb. 10.1Pakuti ndi chipereko chimodzi anawayesera angwiro chikhalire iwo oyeretsedwa.
15Koma Mzimu Woyeranso atichitira umboni; pakuti adatha kunena,
16 Yer. 31.33-34 Ichi ndi chipangano ndidzapangana nao,
atapita masiku ajawo, anena Ambuye:
Ndidzapereka malamulo anga akhale pamtima pao;
ndipo pa nzeru zao ndidzawalemba;
17ndipo machimo ao ndi masaweruziko ao
sindidzawakumbukiranso.
18Koma pomwe pali chikhululukiro cha machimo palibenso chopereka cha kwa uchimo.
Awachenjeza alimbike m'chikhulupiriro19 Aheb. 9.8, 12 Ndipo pokhala nacho, abale, chilimbikitso chakulowa m'malo opatulika, ndi mwazi wa Yesu,
20Yoh. 14.6pa njira yatsopano ndi yamoyo, imene adatikonzera, mwa chotchinga, ndicho thupi lake;
21Aheb. 4.14; 1Tim. 3.15ndipo popeza tili naye wansembe wamkulu wosunga nyumba ya Mulungu;
22Aef. 3.12tiyandikire ndi mtima woona, m'chikhulupiriro chokwanira, ndi mitima yathu yowazidwa kuichotsera chikumbu mtima choipa, ndi matupi athu osambitsidwa ndi madzi oyera;
23Aheb. 4.14; 1Ate. 5.24tigwiritse chivomerezo chosagwedera cha chiyembekezo chathu, pakuti wolonjezayo ali wokhulupirika;
24ndipo tiganizirane wina ndi mnzake kuti tifulumizane ku chikondano ndi ntchito zabwino,
25Mac. 2.42osaleka kusonkhana kwathu pamodzi, monga amachita ena, komatu tidandaulirane, ndiko koposa monga momwe muona tsiku lilikuyandika.
26 2Pet. 2.20-21 Pakuti tikachimwa ife eni ake, titatha kulandira chidziwitso cha choonadi, siitsalanso nsembe ya kwa machimo,
272Pet. 2.20-21koma kulindira kwina koopsa kwa chiweruziro, ndi kutentha kwake kwa moto wakuononga otsutsana nao.
28Deut. 17.2, 6Munthu wopeputsa chilamulo cha Mose angofa opanda chifundo pa mboni ziwiri kapena zitatu:
29Aheb. 2.3; 12.25; 1Ako. 11.29; Mat. 12.31-32ndipo mutani, kulanga koposa kotani nanga adzayesedwa woyenera iye amene anapondereza Mwana wa Mulungu, nayesa mwazi wa chipangano umene anayeretsedwa nao chinthu wamba, nachitira chipongwe Mzimu wa chisomo;
30Aro. 12.19; Deut. 32.36pakuti timdziwa Iye amene anati, Kubwezera chilango nkwanga, Ine ndidzabwezera. Ndiponso, Ambuye adzaweruza anthu ake.
31Luk. 12.5Kugwa m'manja a Mulungu wamoyo nkoopsa.
32 Afi. 1.29-30 Koma tadzikumbutsani masiku akale, m'menemo mutaunikidwa mudapirira chitsutsano chachikulu cha zowawa;
331Ako. 4.9pena pochitidwa chinthu chooneredwa mwa matonzo ndi zisautso; penanso polawana nao iwo ochitidwa zotere.
34Afi. 1.7; 1Pet. 1.4Pakuti munamva chifundo ndi iwo a m'ndende, ndiponso mudalola mokondwera kulandidwa kwa chuma chanu, pozindikira kuti muli nacho nokha chuma choposa chachikhalire.
35Potero musataye kulimbika kwanu, kumene kuli nacho chobwezera mphotho chachikulu.
361Yoh. 2.17Pakuti chikusowani chipiriro, kuti pamene mwachita chifuniro cha Mulungu, mukalandire lonjezano.
37 Hab. 2.3-4 Pakuti katsala kanthawi kakang'onong'ono,
ndipo wakudzayo adzafika, wosachedwa.
38 Hab. 2.3-4 Koma wolungama wangayo adzakhala ndi moyo wochokera m'chikhulupiriro:
Ndipo ngati abwerera, moyo wanga ulibe kukondwera mwa iye.
39 2Pet. 2.20-21; Mac. 16.30-31 Koma ife si ndife a iwo akubwerera kulowa chitayiko; koma a iwo a chikhulupiriro cha ku chipulumutso cha moyo.
Who We AreWhat We EelieveWhat We Do
2025 by iamachristian.org,Inc All rights reserved.