1 Gen. 12.7 Ndipo Yehova anati kwa Mose, Muka, kwera kuchokera kuno, iwe ndi anthu amene unawakweza kuchokera m'dziko la Ejipito, kunka ku dzikolo ndinalumbirira nalo Abrahamu, ndi Isaki, ndi Yakobo, ndi kuti, Ndidzapatsa mbeu zako ilo;
2Eks. 32.34ndipo ndidzatuma mthenga akutsogolere; ndipo ndidzapirikitsa Akanani, ndi Aamori, ndi Ahiti, ndi Aperizi, Ahivi, ndi Ayebusi;
3Eks. 32.9kudziko koyenda mkaka ndi uchi ngati madzi, pakuti sindidzakwera pakati pa inu; popeza inu ndinu anthu opulupudza; ndingathe inu panjira.
4Ndipo pamene anthu anamva mau awa oipa anachita chisoni; ndipo panalibe mmodzi anavala zokometsera zake.
5Ndipo Yehova anati kwa Mose, Nena ndi ana a Israele, Inu ndinu anthu opulupudza; ndikakwera kulowa pakati pa inu kamphindi kamodzi, ndidzakuthani; koma tsopano, vulani zokometsera zanu, kuti ndidziwe chomwe ndikuchitireni.
6Ndipo ana a Israele anazichotsera zokometsera zao kuyambira pa phiri la Horebu.
7Ndipo Mose akatenga chihemacho nachimanga kunja kwa chigono, kutali kwa chigono; nachitcha, Chihema chokomanako. Ndipo kunakhala kuti yense wakufuna Yehova anatuluka kunka ku chihema chokomanako kunja kwa chigono.
8Ndipo kunali, pakutuluka Mose kunka ku chihemacho kuti anthu onse anaimirira, nakhala chilili, munthu yense pakhomo pa hema wake, nachita chidwi pa Mose, kufikira atalowa m'chihemacho.
9Ndipo kunali, pakulowa Mose m'chihemacho, mtambo njo udafutsika, nuima pakhomo pa chihemacho; ndipo Yehova analankhula ndi Mose.
10Ndipo anthu onse anaona mtambo njo ulikuima pakhomo pa chihema; ndi anthu onse anaimirira, nalambira, yense pakhomo pa hema wake.
11Gen. 32.30; Deut. 34.10Ndipo Yehova ananena ndi Mose kopenyana maso, monga munthu alankhula ndi bwenzi lake. Ndipo anabwerera kunka kuchigono; koma mtumiki wake Yoswa mwana wa Nuni, ndiye mnyamata msinkhu wake, sanachoke m'chihemamo.
Mose apeza ufulu pamaso pa Mulungu12Ndipo Mose anati kwa Yehova, Taonani, Inu munena ndi ine, Kwera nao anthu awa; koma simunandidziwitsa amene mudzamtuma amuke nane. Koma munati, Ndikudziwa dzina lako, wapezanso ufulu pamaso panga.
13Ndipo tsopano, ngati ndapeza ufulu pamaso panu, mundidziwitsetu njira zanu, kuti ndikudziweni, ndi kuti ndipeze ufulu pamaso panu; ndipo penyani kuti mtundu uwu ndi anthu anu.
14Yos. 1.5Ndipo anati, Nkhope yanga idzamuka nawe, ndipo ndidzakupumuza.
15Ndipo ananena ndi Iye, Ikapanda kumuka nane nkhope yanu, musatikweze kuchokera kuno.
16Pakuti chidziwika ndi chiyani tsopano kuti ndapeza ufulu pamaso panu, ine ndi anthu anu? Si pakumuka nafe Inu, kuti ine ndi anthu anu tisiyane ndi anthu onse akukhala pa nkhope ya dziko lapansi?
17Ndipo Yehova anati kwa Mose, Ichi chomwe wanenachi ndidzachita; pakuti wapeza ufulu pamaso panga, ndipo ndikudziwa dzina lako.
18Ndipo anati, Ndionetsenitu ulemerero wanu.
19Aro. 9.15Ndipo Iye anati, Ndidzapititsa ukoma wanga wonse pamaso pako, ndipo ndidzatchula dzina la Yehova pamaso pako; ndipo ndidzachitira ufulu amene ndidzamchitira ufulu; ndi kuchitira chifundo amene ndidzamchitira chifundo.
20Ower. 6.22; Chiv. 1.16-17Ananenanso, Sungathe kuona nkhope yanga; pakuti palibe munthu adzandiona Ine ndi kukhala ndi moyo.
21Ndipo Yehova anati, Taona pali Inepo pali malo, ndipo uime pathanthwe;
22ndipo kudzakhala, pakupitira ulemerero wanga, ndidzakuika mu mpata wa thanthwe, ndi kukuphimba ndi dzanja langa, mpaka nditapitirira;
23ndipo pamene ndichotsa dzanja langa udzaona m'mbuyo mwanga; koma nkhope yanga siidzaoneka.
Who We AreWhat We EelieveWhat We Do
2025 by iamachristian.org,Inc All rights reserved.