1Nthawi yomweyo ophunzira anadza kwa Yesu, nanena, Ndani kodi ali wopambana mu Ufumu wa Kumwamba?
2Ndipo pamene Yesu anaitana kamwana, anakaimitsa pakati pao,
3
12Luk. 15.4-7Nanga muyesa bwanji? Ngati munthu ali nazo nkhosa makumi khumi, ndipo ikasokera imodzi ya izo, kodi saleka zija makumi asanu ndi anai mphambu zisanu ndi zinai, napita kumapiri, kukafuna yosokerayo?
13Ndimo akaipeza, indedi ndinena kwa inu, akondwera nayo koposa ndi makumi asanu ndi anai mphambu zisanu ndi zinai zosasokera.
14Chomwecho sichili chifuniro cha Atate wanu wa Kumwamba kuti mmodzi wa ang'ono awa atayike.
Makhululukidwe15 Lev. 19.27; Luk. 17.3; Yak. 5.20 Ndipo ngati mbale wako akuchimwira iwe, pita, numlangize pa nokha iwe ndi iye; ngati akumvera iwe, wambweza mbale wako.
16Yoh. 8.17Koma ngati samvera, onjeza kutenga ndi iwe wina mmodzi kapena awiri, kuti atsimikizidwe mau onse pakamwa pa mboni ziwiri kapena zitatu.
17Aro. 16.17Ndipo ngati iye samvera iwo, uuze Mpingo; ndipo ngati iye samveranso Mpingowo, akhale kwa iwe monga wakunja ndi wamsonkho.
18Mat. 16.19Indetu ndinena kwa inu, Zilizonse mukazimanga pa dziko lapansi zidzakhala zomangidwa Kumwamba: ndipo zilizonse mukazimasula pa dziko lapansi, zidzakhala zomasulidwa Kumwamba.
191Yoh. 3.22Ndiponso ndinena kwa inu kuti ngati awiri a inu avomerezana pansi pano chinthu chilichonse akachipempha, Atate wanga wa Kumwamba adzawachitira.
20Pakuti kumene kuli awiri kapena atatu asonkhanira m'dzina langa, ndili komweko pakati pao.
Fanizo la wamangawa wopanda chifundo21Pamenepo Petro anadza, nati kwa Iye, Ambuye, mbale wanga adzandilakwira kangati, ndipo ine ndidzamkhululukira iye? Kufikira kasanu ndi kawiri kodi?
22Mrk. 11.25; Akol. 3.13Yesu ananena kwa iye, Sindinena kwa iwe kufikira kasanu ndi kawiri, koma kufikira makumi asanu ndi awiri kubwerezedwa kasanu ndi kawiri.
23Chifukwa chake Ufumu wa Kumwamba ufanizidwa ndi munthu, mfumu, amene anafuna kuwerengera nao akapolo ake.
24Ndipo pamene anayamba kuwerengera, anadza kwa iye ndi wina wamangawa wa ndalama za matalente zikwi khumi.
252Maf. 4.1Koma popeza iye anasowa kanthu kombwezera, mbuye wake analamulira kuti iye agulitsidwe, ndi mkazi wake ndi ana ake omwe, ndi zonse ali nazo, kuti akabwezedwe mangawawo.
26Chifukwa chake kapoloyo anagwada pansi, nampembedzera, nati, Mbuye, bakandiyembekezani ine, ndipo zonse ndidzazibwezera kwa inu.
27Ndipo mbuye wa kapoloyo anagwidwa ndi chisoni mumtima, nammasula iye, namkhululukira ngongole.
28Koma kapolo uyu, potuluka anapeza wina wa akapolo anzake yemwe anamkongola iye marupiya atheka makumi khumi, namgwira, namkanyanga pakhosi, nati, Bwezera chija unachikongola.
29Pamenepo kapolo mnzakeyu anagwada pansi, nampempha iye, nati, Bakandiyembekeza ine, ndipo ndidzakubwezera.
30Ndipo iye sanafune; koma anamuka, namponya iye m'nyumba yandende, kufikira abwezere ngongole.
31Chifukwa chake m'mene akapolo anzake anaona zochitidwazo, anagwidwa chisoni chachikulu, nadza, nalongosolera mbuye wao zonse zimene zinachitidwa.
32Pomwepo mbuye wake anamuitana iye, nanena naye, Kapolo iwe woipa, ndinakukhululukira iwe mangawa onse aja momwe muja unandipempha ine;
33kodi iwenso sukadamchitira kapolo mnzako chisoni, monga inenso ndinakuchitira iwe chisoni?
34Ndipo mbuye wake anakwiya, nampereka kwa azunzi, kufikira akambwezere iye mangawa onse.
35Miy. 21.13; Yak. 2.13Chomwechonso Atate wanga a Kumwamba adzachitira inu, ngati inu simukhululukira yense mbale wake ndi mitima yanu.
Who We AreWhat We EelieveWhat We Do
2025 by iamachristian.org,Inc All rights reserved.