1Ndipo zitatha izi, kunachitika kuti ana a Mowabu, ndi ana a Amoni, ndi ena pamodzi ndi Aamoni, anadza kuyambana nkhondo ndi Yehosafati.
2Pamenepo anadza anthu akuuza Yehosafati, kuti, Ukudzerani unyinji waukulu wa anthu ochokera tsidya la nyanja ku Aramu; ndipo taonani, ali ku Hazazoni-Tamara, ndiwo Engedi.
3Ezr. 8.21; Yon. 3.5Ndipo Yehosafati anachita mantha, nalunjikitsa nkhope yake kufuna Yehova, nalalikira kusala mwa Ayuda onse.
4Namemezedwa Yuda afunsire kwa Yehova, inde anachokera kumidzi yonse ya Yuda kufuna Yehova.
5Ndipo Yehosafati anaima mu msonkhano wa Ayuda, ndi a ku Yerusalemu, kunyumba ya Yehova, pakati pa bwalo latsopano;
6Mas. 47.2; Dan. 4.17, 25, 32nati, Yehova Mulungu wa makolo athu, Inu sindinu Mulungu wa m'Mwamba kodi? Sindinu woweruza maufumu onse a amitundu kodi? Ndi m'dzanja mwanu muli mphamvu yolimba; palibe wina wakulimbana ndi Inu.
7Mas. 44.2; Yak. 2.23Sindinu Mulungu wathu, amene munainga nzika za m'dziko muno pa maso pa ana anu Israele, ndi kulininkha kwa mbeu ya Abrahamu bwenzi lanu kosatha?
8Nakhala m'mwemo iwowa, nakumangirani m'mwemo malo opatulika a dzina lanu, ndi kuti,
91Maf. 8.33, 37Chikatigwera choipa, lupanga, chiweruzo, kapena mliri, kapena njala, tidzakhala chilili pakhomo pa nyumba iyi, ndi pamaso panu, (pakuti m'nyumba muno muli dzina lanu), ndi kufuulira kwa Inu m'kusauka kwathu; ndipo mudzamvera ndi kulanditsa.
10Deut. 2.5, 9, 19Ndipo tsopano, taonani ana a Amoni, ndi Mowabu, ndi a kuphiri la Seiri, amene simunalola Israele awalowere, pakutuluka iwo m'dziko la Ejipito, koma anawapatukira osawaononga;
11tapenyani, m'mene atibwezera, kudzatiinga m'cholowa chanu, chimene munatipatsa chikhale cholowa chathu.
12Mulungu wathu, simudzawaweruza? Pakuti mwa ife mulibe mphamvu yakulimbana nao aunyinji ambiri awa akutidzera; ndipo sitidziwa ngati tidzatani, koma maso athu ali kwa Inu.
13Ndipo Ayuda onse anakhala chilili pamaso pa Yehova, pamodzi ndi makanda ao, akazi ao, ndi ana ao.
14Pamenepo mzimu wa Yehova unagwera Yahaziele mwana wa Zekariya, mwana wa Benaya, mwana wa Yeiyele, mwana wa Mataniya, Mlevi, wa ana a Asafu, pakati pa msonkhano;
15Eks. 14.13-14nati iye, Tamverani Ayuda inu nonse, ndi inu okhala m'Yerusalemu, ndi inu mfumu Yehosafati, atero nanu Yehova, Musaope musatenge nkhawa chifukwa cha aunyinji ambiri awa; pakuti nkhondoyi si yanu, koma ya Mulungu.
16Mawa muwatsikire; taonani, akwera pokwerera pa Zizi, mudzakomana nao polekezera chigwa chakuno cha chipululu cha Yeruwele.
17Eks. 14.13-14Si kwanu kuchita nkhondo kuno ai; chilimikani, imani, nimupenye chipulumutso cha Yehova pa inu Yuda ndi Yerusalemu; musaope, kapena kutenga nkhawa; mawa muwatulukire, popeza Yehova ali ndi inu.
18Ndipo Yehosafati anawerama mutu wake, nkhope yake pansi; ndi Ayuda onse, ndi okhala m'Yerusalemu anagwa pansi pamaso pa Yehova, nalambira Yehova.
19Ndipo Alevi, a ana a Akohati, ndi a ana a Kora, anauka kulemekeza Yehova Mulungu wa Israele ndi mau omveketsa.
Amowabu ndi Aamoni akanthidwa20 Yes. 7.9 Nalawira mamawa, natuluka kunka kuchipululu cha Tekowa; ndipo potuluka iwo, Yehosafati anakhala chilili, nati, Mundimvere ine, Ayuda inu, ndi inu okhala m'Yerusalemu, limbikani mwa Yehova Mulungu wanu, ndipo mudzakhazikika; khulupirirani aneneri ake, ndipo mudzalemerera.
211Mbi. 16.29, 34, 41Ndipo atafunsana ndi anthu, anaika oimbira Yehova, ndi kulemekeza chiyero chokometsetsa, pakutuluka iwo kutsogolera khamu la nkhondo, ndi kuti, Yamikani Yehova, pakuti chifundo chake chikhala chosatha.
22Ndipo poyamba iwo kuimba, ndi kulemekeza Yehova, anaika olalira alalire Aamoni, Amowabu, ndi a m'phiri la Seiri, akudzera Ayuda; ndipo anawakantha.
23Pakuti ana a Amoni, ndi a Mowabu, anaukira okhala m'phiri la Seiri, kuwapha ndi kuwaononga psiti; ndipo atatha okhala m'Seiri, anasandulikirana kuonongana.
24Ndipo pofika Ayuda ku dindiro la kuchipululu, anapenyera aunyinjiwo; taonani, mitembo ili ngundangunda, wosapulumuka ndi mmodzi yense.
25Ndipo pofika Yehosafati ndi anthu ake kutenga zofunkha zao, anapezako chuma chambiri, ndi mitembo yambiri ndi zipangizo zofunika, nadzifunkhira, osakhoza kuzisenza zonse; nalimkutenga zofunkhazo masiku atatu, popeza zinachuluka.
26Ndi tsiku lachinai anasonkhana m'chigwa cha Beraka; pakuti pamenepo analemekeza Yehova; chifukwa chake anatcha dzina lake la malowo, Chigwa cha Beraka, mpaka lero lino.
27Neh. 12.43Pamenepo anabwerera amuna onse a Yuda, ndi a ku Yerusalemu, nawatsogolera ndi Yehosafati, kubwerera kunka ku Yerusalemu ndi chimwemwe; pakuti Yehova anawakondweretsa pa adani ao.
28Ndipo anafika ku Yerusalemu ndi zisakasa, ndi azeze, ndi malipenga, kunyumba ya Yehova.
292Mbi. 17.10Ndipo kuopsa kwa Mulungu kunagwera maufumu onse a m'maiko, pamene anamva kuti Yehova adayambana ndi adani a Israele.
302Mbi. 15.15Nuchita bata ufumu wa Yehosafati; pakuti Mulungu wake anampumulitsira pozungulirapo.
31Momwemo Yehosafati anakhala mfumu ya Yuda; anali wa zaka makumi atatu mphambu zisanu polowa ufumu wake, nakhala mfumu m'Yerusalemu zaka makumi awiri; ndi dzina la make ndiye Azuba mwana wa Sili.
32Ndipo anayenda m'njira ya Asa atate wake osapatukamo, nachita zoongoka pamaso pa Yehova.
33Komatu misanje siinachotsedwa; popeza pamenepo anthu sadakonzere mitima yao kwa Mulungu wa makolo ao.
34Machitidwe ena tsono adazichita Yehosafati, zoyamba ndi zotsiriza, taonani, zilembedwa m'buku la mau a Yehu mwana wa Hanani, wotchulidwa m'buku la mafumu a Israele.
35 1Maf. 22.48-49 Zitatha izi, Yehosafati mfumu ya Yuda anaphatikana ndi Ahaziya mfumu ya Israele, yemweyo anachita moipitsitsa;
36naphatikana naye kupanga zombo zomuka ku Tarisisi, nazipanga zombozo m'Eziyoni-Gebere.
37Pamenepo Eliyezere mwana wa Dodavahu wa Maresa ananenera kumtsutsa Yehosafati, ndi kuti, Popeza waphatikana ndi Ahaziya Yehova wapasula ntchito zako. Ndipo zombo zinasweka zosakhoza kumuka ku Tarisisi.
Who We AreWhat We EelieveWhat We Do
2025 by iamachristian.org,Inc All rights reserved.