1 Mas. 72; Zek. 9.9 Taonani mfumu idzalamulira m'chilungamo, ndi akalonga adzalamulira m'chiweruzo.
2Ndipo munthu adzakhala monga pobisalira mphepo, ndi pousira chimphepo; monga mitsinje yamadzi m'malo ouma, monga mthunzi wa thanthwe lalikulu m'dziko lotopetsa.
3Ndipo maso a iwo amene aona sadzatsinzina, ndi makutu a iwo amene amva adzamvera.
4Mtimanso wansontho udzadziwa nzeru, ndi lilime la achibwibwi lidzalankhula zomveka msanga.
5Wopusa sadzayesedwanso woolowa manja, ngakhale wouma manja sadzayesedwa mfulu.
6Pakuti wopusa adzanena zopusa, ndi mtima wake udzachita mphulupulu, kuchita zoipitsa, ndi kunena za Yehova molakwira, kusowetsa konse mtima wanjala, ndi kulepheretsa chakumwa cha waludzu.
7Zipangizonso za womana zili zoipa; iye apangira ziwembu zakuononga waumphawi ndi mau onama, ngakhale pamene wosowa alankhula zoona.
8Koma mfulu aganizira zaufulu, nakhazikika m'zaufulu zomwe.
Chilangizo cha kwa akazi9 Amo. 6.1 Ukani, akazi inu, amene mulinkukhala phee, mumve mau anga; inu ana akazi osasamalira, tcherani makutu pa kulankhula kwanga.
10Pakutha chaka, kudza masiku ena inu mudzavutidwa, inu akazi osasamalira; pakuti masika a mphesa adzasoweka, sadzatuta konse.
11Nthunthumirani, inu akazi, amene mulinkukhalaphe; vutidwani, inu osasamalira, vulani mukhale maliseche, nimumange chiguduli m'chuuno mwanu.
12Iwo adzadzimenya pazifuwa chifukwa cha minda yabwino, chifukwa cha mpesa wobalitsa.
13Hos. 9.6Pa dziko la anthu anga padzafika minga ndi lunguzi; inde pa nyumba zonse zokondwa, m'mudzi wokondwerera;
14pakuti nyumba ya mfumu idzasiyidwa; mudzi wa anthu ambiri udzakhala bwinja; chitunda ndi nsanja zidzakhala nkhwimba kunthawi zonse, pokondwera mbidzi podyera zoweta;
15Yow. 2.28kufikira mzimu udzathiridwa pa ife kuchokera kumwamba, ndi chipululu chidzasanduka munda wobalitsa, ndi munda wobalitsa udzayesedwa nkhalango.
16Pamenepo chiweruzo chidzakhala m'chipululu, ndi chilungamo chidzakhala m'munda wobalitsa.
17Yak. 3.18Ndi ntchito ya chilungamo idzakhala mtendere; ndi zotsata chilungamo zidzakhala mtendere, ndi kukhulupirika kunthawi zonse.
18Ndipo anthu anga adzakhala m'malo a mtendere, ndi mokhala mokhulupirika ndi mopuma mwa phee.
19Koma kudzagwa matalala m'kugwa kwake kwa nkhalango; ndipo mudzi udzagwetsedwa ndithu.
20Mlal. 11.1Odala muli inu, amene mubzala m'mbali mwa madzi monse, amene muyendetsa mapazi a ng'ombe ndi bulu.
Who We AreWhat We EelieveWhat We Do
2025 by iamachristian.org,Inc All rights reserved.