MASALIMO 45 - Buku Lopatulika Bible 2014

Nyimbo yoimbira ukwati wa mfumuKwa Mkulu wa Nyimbo, pa Syosyanimu. Chilangizo cha kwa ana a Kora. Nyimbo ya chikondi.

1Mtima wanga usefukira nacho chinthu chokoma.

Ndinena zopeka ine za mfumu,

lilime langa ndilo peni yofulumiza kulemba.

2 Luk. 4.22 Inu ndinu wokongola ndithu koposa ana a anthu;

anakutsanulirani chisomo pa milomo yanu,

chifukwa chake Mulungu anakudalitsani kosatha.

3 Yes. 9.6 Dzimangireni lupanga lanu m'chuuno mwanu,

wamphamvu inu,

ndi ulemerero wanu ndi ukulu wanu.

4 Chiv. 6.2 Ndipo pindulani, m'ukulu wanu yendani,

kaamba ka choonadi ndi chifatso ndi chilungamo;

ndipo dzanja lanu lidzakuphunzitsani zoopsa.

5Mivi yanu njakuthwa;

mitundu ya anthu igwa pansi pa inu;

iwalasa mumtima adani a mfumu.

6 Aheb. 1.8-9 Mpando wachifumu wanu,

Mulungu, ukhala nthawi zonse zomka muyaya.

Ndodo yachifumu ya ufumu wanu ndiyo ndodo yolunjika.

7Mukonda chilungamo, ndipo mudana nacho choipa,

chifukwa chake Mulungu, ndiye Mulungu wanu, wadzoza inu

ndi mafuta a chikondwerero koposa anzanu.

8Zovala zanu zonse nza mure, ndi khonje, ndi kasiya;

m'zinyumba za mfumu zomanga ndi minyanga ya njovu

mwatuluka zoimba za zingwe zokukondweretsani.

9 Chiv. 21.9 Mwa omveka anu muli ana akazi a mafumu;

ku dzanja lanu lamanja aima mkazi wa mfumu

wovala golide wa ku Ofiri.

10Tamvera, mwana wamkaziwe, taona, tatchera khutu lako;

uiwalenso mtundu wako ndi nyumba ya atate wako;

11 Yes. 54.5 potero mfumuyo adzakhumba kukoma kwako,

pakuti ndiye mbuye wako; ndipo iwe umgwadire iye.

12 Yes. 49.23 Ndipo mwana wamkazi wa Tiro adzafika nayo mphatso;

achuma a mwa anthu adzapempha kudziwika nanu.

13Mwana wamkazi wa mfumu

ngwa ulemerero wonse m'kati mwa nyumba,

zovala zake nza malukidwe agolide.

14Adzamtsogolera kwa mfumu wovala zamawangamawanga,

anamwali anzake omtsata adzafika nao kwa inu.

15Adzawatsogolera ndi chimwemwe ndi kusekerera,

adzalowa m'nyumba ya mfumu.

16M'malo mwa makolo ako mudzakhala ana ako,

udzawaika akhale mafumu m'dziko lonse lapansi.

17 Mala. 1.11 Ndidzawakumbutsa dzina lanu m'mibadwomibadwo;

chifukwa chake mitundu ya anthu idzayamika Inu

kunthawi za nthawi.

Blog
About Us
Message
Site Map

Who We AreWhat We EelieveWhat We Do

Terms of UsePrivacy Notice

2025 by iamachristian.org,Inc All rights reserved.

Home
Gospel
Question
Blog
Help