MIYAMBO 23 - Buku Lopatulika Bible 2014

1Pamene ukhala ulinkudya ndi mkulu,

zikumbukira ameneyo ali pamaso pako;

2nuike mpeni pakhosi pako,

ngati uli wadyera.

3Usakhumbe zolongosoka zake;

pokhala zakudya zonyenga.

4 Aro. 12.16; 1Tim. 6.9-10 Usadzitopetse kuti ulemere;

leka nzeru yakoyako.

5Kodi upenyeranji chimene kulibe?

Pakuti chuma chimera mapiko,

ngati mphungu youluka mumlengalenga.

6 Mas. 141.1 Usadye zakudya zake za wa maso ankhwenzule,

ngakhale kukhumba zolongosoka zake.

7Pakuti monga asinkha m'kati mwake, ali wotere;

ati kwa iwe, Idya numwe;

koma mtima wake suli pa iwe.

8Pakuti nthongo imene unaidya udzaisanza,

ndi kutaya mau ako okondweretsa.

9 Mat. 7.6 Usalankhule m'makutu a wopusa;

pakuti adzapeputsa nzeru ya mau ako.

10 Miy. 22.28 Usasunthe chidziwitso chakale cha m'malire;

ngakhale kulowa m'minda ya amasiye;

11pakuti Mombolo wao walimba;

adzawanenera mlandu wao pa iwe.

12Lozetsa mtima wako kumwambo,

ndi makutu ako ku mau anzeru.

13Usamane mwana chilango;

pakuti ukammenya ndi nthyole safa ai.

14Udzammenya ndi nthyole,

nudzapulumutsa moyo wake kunsi kwa manda.

15Mwananga, mtima wako ukakhala wanzeru,

mtima wanga wa inedi udzakondwa.

16Imso zanga zidzasangalala,

polankhula milomo yako zoongoka.

17 Mas. 73.3 Mtima wako usachitire nsanje akuchimwawo;

koma opabe Yehova tsiku lonse.

18 Luk. 16.25 Pakutitu padzakhala mphotho;

ndipo chiyembekezo chako sichidzalephereka.

19Tamvera tsopano, mwananga, utenge nzeru,

ulunjikitse mtima wako m'njiramo.

20 Yes. 5.22; Aef. 5.18 Usakhale mwa akumwaimwa vinyo,

ndi ankhuli osusuka.

21Pakuti wakumwaimwa ndi wosusukayo adzasauka;

ndipo kusinza kudzaveka munthu nsanza.

22 Mat. 13.44 Tamvera atate wako anakubala,

usapeputse amai ako atakalamba.

23Gula ntheradi, osaigulitsa;

nzeru, ndi mwambo, ndi luntha.

24 Miy. 15.20 Atate wa wolungama adzasekeradi;

wobala mwana wanzeru adzakondwera naye.

25Atate wako ndi amai ako akondwere,

amai ako akukubala asekere.

26Mwananga, undipatse mtima wako,

maso ako akondwere ndi njira zanga.

27Pakuti mkazi wadama ndiye dzenje lakuya;

ndipo mkazi wachiwerewere ndiye mbuna yopapatiza.

28Pakuti abisalira ngati wachifwamba,

nachulukitsa anthu a chiwembu.

29 Yes. 5.11, 22 Ndani ali ndi chisoni? Ndani asauka?

Ndani ali ndi makangano? Ndani ang'ung'udza?

Ndani alasidwa chabe? Ndani afiira maso?

30 Miy. 20.1 Ngamene achedwa pali vinyo,

napita kukafunafuna vinyo wosanganizidwa.

31Usayang'ane pavinyo alikufiira,

alikung'azimira m'chikho,

namweka mosalala.

32Pa chitsiriziro chake aluma ngati njoka,

najompha ngati mamba.

33Maso ako adzaona zachilendo,

mtima wako udzalankhula zokhota.

34Udzafanana ndi wina wogona pakati pa nyanja,

pena wogona pa nsonga ya mlongoti wa ngalawa.

35 Yer. 5.3 Udzati, Anandimenya, osaphwetekedwa ine;

anandikwapula, osamva ine;

ndidzauka nthawi yanji?

Ndidzafunafunanso vinyoyo.

Blog
About Us
Message
Site Map

Who We AreWhat We EelieveWhat We Do

Terms of UsePrivacy Notice

2025 by iamachristian.org,Inc All rights reserved.

Home
Gospel
Question
Blog
Help