DEUTERONOMO 16 - Buku Lopatulika Bible 2014

Zikondwerero za Paska, za Masabata, ndi za Misasa

1 Eks. 12.2-11; 13.4 Samalirani mwezi wa Abibu, kuti muzichitira Yehova Mulungu wanu Paska; popeza m'mwezi wa Abibu Yehova Mulungu wanu anakutulutsani m'dziko la Ejipito usiku.

2Ndipo muziphera Yehova Mulungu wanu nsembe ya Paska, ya nkhosa ndi ya ng'ombe, m'malo amene Yehova adzasankha kukhalitsamo dzina lake.

3Eks. 13.6-7Musamadyera nayo mkate wa chotupitsa; masiku asanu ndi awiri mudyere nayo mkate wopanda chotupitsa, ndiwo mkate wa chizunziko popeza munatuluka m'dziko la Ejipito mofulumira; kuti mukumbukire tsiku lotuluka inu m'dziko la Ejipito masiku onse a moyo wanu.

4Ndipo m'malire mwanu monse musaoneke chotupitsa masiku asanu ndi awiri; nyama yomwe muiphere nsembe tsiku loyamba madzulo, isatsaleko usiku wonse kufikira m'mawa.

5Simuyenera kuphera nsembe ya Paska m'midzi yanu iliyonse, imene Yehova Mulungu wanu akupatsani;

6koma pamalo pamene Yehova Mulungu wanu adzasankha kukhalitsapo dzina lake, pamenepo muphere nsembe ya Paska, madzulo, polowa dzuwa, nyengo ya kutuluka inu m'Ejipito.

7Ndipo muiphike ndi kuidya m'malo amene Yehova Mulungu wanu adzasankha; koma m'mawa mwake mubwerere kunka ku mahema anu.

8Masiku asanu ndi limodzi muzidya mkate wopanda chotupitsa; ndipo tsiku lachisanu ndi chiwiri ndilo loletsa, la Yehova Mulungu wanu; musamagwira ntchito pamenepo.

9 Mac. 2.1 Mudziwerengere masabata asanu ndi awiri; muyambe kuwerenga masabata asanu ndi awiri poyambira kusenga tirigu wachilili.

101Ako. 16.2Ndipo muchitire Yehova Mulungu wanu chikondwerero cha Masabata, ndiwo msonkho waufulu wa dzanja lanu, umene mupereke monga Yehova Mulungu wanu akudalitsani.

11Ndipo mukondwere pamaso pa Yehova Mulungu wanu, inu ndi ana anu amuna, ndi ana anu akazi, ndi antchito anu amuna, ndi antchito anu akazi, ndi Mlevi wokhala m'mudzi mwanu, ndi mlendo, ndi mwana wamasiye, ndi mkazi wamasiye, okhala pakati pa inu, m'malo amene Yehova Mulungu wanu adzasankha kukhalitsako dzina lake.

12Ndipo mukumbukire kuti munali akapolo m'Ejipito; musamalire kuchita malemba awa.

13Mudzichitire chikondwerero cha Misasa masiku asanu ndi awiri, mutasunga za padwale ndi za mopondera mphesa;

14Neh. 8.9-12nimukondwere m'madyerero mwanu, inu, ndi ana anu amuna, ndi ana anu akazi, ndi antchito anu amuna, ndi antchito anu akazi, ndi Mlevi, ndi mlendo, ndi mwana wamasiye, ndi mkazi wamasiye okhala m'mudzi mwanu.

15Masiku asanu ndi awiri muchitire Yehova Mulungu wanu madyerero m'malo amene Yehova adzasankha; popeza Yehova Mulungu wanu adzakudalitsani m'zipatso zanu zonse, ndi m'ntchito zonse za manja anu; nimukondwere monsemo.

16Eks. 23.14-17Amuna onse azioneka pamaso pa Yehova Mulungu wanu m'malo amene Iye adzasankha, katatu m'chaka; pa chikondwerero cha Mkate wopanda chotupitsa, pa chikondwerero cha masabata, ndi pa chikondwerero cha Misasa; ndipo asaoneke pamaso pa Yehova opanda kanthu;

172Ako. 8.12apereke yense monga mwa mphatso ya m'dzanja lake, monga mwa mdalitso wa Yehova Mulungu wanu anakupatsani.

Za oweruza milandu

18Mudziikire oweruza ndi akapitao m'midzi yanu yonse imene Yehova Mulungu wanu akupatsani, monga mwa mafuko anu; ndipo aweruze anthu ndi chiweruzo cholungama.

19Miy. 17.23; 24.23Musamapotoza chiweruzo, musamasamalira munthu, kapena kulandira chokometsera mlandu; popeza chokometsera mlandu chidetsa maso a anzeru, nichiipsa mau a olungama.

20Chilungamo, chilungamo ndicho muzichitsata, kuti mukhale ndi moyo ndi kulandira dziko limene Yehova Mulungu wanu akupatsani.

21Musazike zifanizo zilizonse pafupi pa guwa la nsembe la Yehova Mulungu wanu, limene mwadzimangira.

22Ndipo musamadziutsira choimiritsa chilichonse chimene Yehova Mulungu wanu adana nacho.

Blog
About Us
Message
Site Map

Who We AreWhat We EelieveWhat We Do

Terms of UsePrivacy Notice

2025 by iamachristian.org,Inc All rights reserved.

Home
Gospel
Question
Blog
Help