1 Yes. 43.10; 49.3, 6; 52.13; 53.11; 61.1; Mat. 3.17; 12.18-20; Yoh. 3.34; Afi. 2.7 Taona Mtumiki wanga, amene ndimgwiriziza; Wosankhika wanga, amene moyo wanga ukondwera naye; ndaika mzimu wanga pa Iye; Iye adzatulutsira amitundu chiweruziro.
2Iye sadzafuula, ngakhale kukuwa, pena kumvetsa mau ake m'khwalala.
3Yes. 57.15Bango lophwanyika sadzalithyola, ndi lawi lozilala sadzalizima; adzatulutsa chiweruzo m'zoona.
4Gen. 49.10; Yes. 60.9Iye sadzalephera kapena kudololoka, kufikira atakhazikitsa chiweruzo m'dziko lapansi; ndipo zisumbu zidzalindira chilamulo chake.
5Zek. 12.1Atero Mulungu Yehova, Iye amene analenga thambo, nalifutukula, nayala ponse dziko lapansi, ndi chimene chituluka m'menemo, Iye amene amapatsa anthu a m'menemo mpweya, ndi mzimu kwa iwo amene ayenda m'menemo;
6Luk. 2.32; Mac. 13.47Ine Yehova ndakuitana Iwe m'chilungamo, ndipo ndidzagwira dzanja lako ndi kusunga Iwe, ndi kupatsa Iwe ukhale pangano la anthu, ndi kuunika kwa amitundu;
7Yes. 61.1; Aheb. 2.14-15kuti utsegule maso akhungu, utulutse am'nsinga m'ndende, ndi iwo amene akhala mumdima, atuluke m'nyumba ya kaidi.
8Yes. 48.11Ine ndine Yehova; dzina langa ndi lomweli; ndipo ulemerero wanga Ine sindidzapereka kwa wina, ngakhale kunditamanda kwa mafano osemedwa.
9Taona, zinthu zakale zaoneka, ndipo zatsopano Ine ndizitchula; zisanabuke ndidzakumvetsani.
10 Mas. 33.3; 107.22-23 Imbirani Yehova nyimbo yatsopano, ndi matamando ake kuchokera ku malekezero a dziko lapansi; inu amene mutsikira kunyanja, ndi zonse zili m'menemo, zisumbu ndi okhala mommo.
11Chipululu ndi midzi yake ikweze mau ao, midzi imene Kedara akhalamo; okhala m'Sela aimbe, akuwe kuchokera pamwamba pa mapiri.
12Apereke ulemerero kwa Yehova, anene matamando ake m'zisumbu.
13Yehova adzatuluka ngati munthu wamphamvu; adzautsa nsanje ngati munthu wa nkhondo; Iye adzafuula, inde adzakuwa zolimba; adzachita zamphamvu pa adani ake.
14Ndakhala nthawi yambiri wosalankhula ndakhala chete kudzithungata ndekha; tsopano ndidzafuula ngati mkazi wobala; ndidzapuma modukizadukiza ndi wefuwefu pamodzi.
15Ndidzapasula mapiri ndi zitunda, ndi kuumitsa zitsamba zao zonse; ndi kusandutsa nyanja zisumbu, ndi kuumitsa matamanda.
16Ndipo ndidzayendetsa akhungu m'khwalala, limene iwo salidziwa, m'njira zimene iwo sazidziwa ndidzawatsogolera; ndidzawalitsa mdima m'tsogolo mwao, ndi kulungamitsa malo okhota. Zinthu izi Ine ndidzachita, ndipo sindidzawasiya.
17Mas. 97.7Iwo adzabwezedwa m'mbuyo, adzakhala ndi manyazi ambiri amene akhulupirira mafano osemedwa, nati kwa mafano oyengeka, Inu ndinu milungu yathu.
18Imvani, agonthi inu; yang'anani, akhungu inu, kuti muone.
19Ezk. 12.2Ndani ali wakhungu, koma mtumiki wanga? Pena wagonthi, monga mthenga wanga, amene ndimtumiza? Ndani ali wakhungu monga bwenzi langa, ndi wakhungu monga mtumiki wa Yehova?
20Aro. 2.21Iwe waona zinthu zambiri, koma susamalira konse; makutu ako ali otseguka, koma sumva konse.
21Chinakondweretsa Yehova chifukwa cha chilungamo chake kukuza chilamulo, ndi kuchilemekeza.
22Koma awa ndiwo anthu olandidwa zao ndi kufunkhidwa; iwo onse agwa m'mauna, nabisidwa m'nyumba za akaidi; alandidwa zao, palibe wowapulumutsa; afunkhidwa ndipo palibe woti, Bwezerani.
23Ndani mwa inu adzatchera khutu lake pamenepo? Amene adzamvera ndi kumva nthawi yakudza?
24Ndani anapereka Yakobo, kuti afunkhidwe, ndi Israele, kuti awawanyidwe? Kodi si Yehova? Iye amene tamchimwira, ndi amene iwo anakonda kuyenda m'njira zake, ngakhale kumvera chiphunzitso chake.
25Hos. 7.9Chifukwa chake anatsanulira pa iye mkwiyo wake waukali, ndi mphamvu za nkhondo; ndipo unamyatsira moto kuzungulira kwake, koma iye sanadziwe; ndipo unamtentha, koma iye sanachisunge m'mtima.
Who We AreWhat We EelieveWhat We Do
2025 by iamachristian.org,Inc All rights reserved.