OWERUZA 9 - Buku Lopatulika Bible 2014

Abimeleki awapha abale ake

1 Ower. 8.31 Koma Abimeleki mwana wa Yerubaala anamuka ku Sekemu kwa abale a amai wake, nanena nao, ndi kwa banja lonse la nyumba ya atate wa amai wake, ndi kuti,

2Nenanitu m'makutu mwa eni ake onse a ku Sekemu, Chokomera inu nchiti, akulamulireni ana amuna onse a Yerubaala ndiwo amuna makumi asanu ndi awiri, kapena akulamulireni mwamuna mmodzi? Mukumbukirenso kuti ine ndine wa fuko lanu ndi nyama yanu.

3Pamenepo abale a amake anamnenera mau awa onse m'makutu a eni ake onse a Sekemu; ndi mitima yao inalunjika kutsata Abimeleki; pakuti anati, Ndiye mbale wathu.

42Mbi. 13.7; Miy. 12.11; Mac. 17.5Ndipo anampatsa ndalama makumi asanu ndi awiri za m'nyumba ya Baala-Beriti; ndipo Abimeleki analembera nazo anthu opanda pake ndi opepuka amene anamtsata.

5Ndipo anamuka kunyumba ya atate wake ku Ofura, nawapha abale ake ana a Yerubaala, ndiwo amuna makumi asanu ndi awiri, pa thanthwe limodzi; koma Yotamu mwana wamng'ono wa Yerubaala anatsalako; pakuti anabisala.

6Pamenepo anasonkhana eni ake onse a ku Sekemu, ndi nyumba yonse ya Milo, namuka namlonga Abimeleki ufumu pa thundu wa choimiritsa chili m'Sekemu.

Fanizo la Yotamu

7Ndipo atamuuza Yotamu, anamuka iye naimirira pamutu pa phiri la Gerizimu, nakweza mau ake, nafuula, nanena nao, Mundimvere ine, eni ake a ku Sekemu inu, kuti Mulungu amvere inu.

82Maf. 14.9Kumuka inamuka mitengo kudzidzozera mfumu; niti kwa mtengo wa azitona, Ukhale iwe mfumu yathu.

9Koma mtengo wa azitona unati kwa iwo, Ngati ndidzasiya kunona kwanga kumene alemekeza nako Mulungu ndi anthu kukalenga pa mitengo?

10Pamenepo mitengo inati kwa mkuyu. Tiye iwe, ukhale mfumu yathu.

11Koma mkuyu unanena nao, Ngati ndidzasiya kuzuna kwanga, ndi zipatso zanga zokoma kukalenga pa mitengo?

12Pamenepo mitengo inati kwa mpesa, Tiye iwe, ukhale mfumu yathu.

13Koma mpesa unanena nao, Ngati ndidzasiya vinyo wanga wakusekeretsa Mulungu ndi anthu, kukalenga pa mitengo?

14Pamenepo mitengo yonse inati kwa nkandankhuku, Tiye iwe, ukhale mfumu yathu.

15Ndipo nkandankhuku unati kwa mitengo, Mukandidzoza mfumu yanu moonadi, tiyeni, thawirani ku mthunzi wanga; mukapanda kutero utuluke moto m'nkandankhuku ndi kunyeketsa mikungudza ya Lebanoni.

16Ower. 8.35; Yes. 3.11Ndipo tsopano, ngati mwachita moona ndi mwangwiro pakulonga Abimeleki ufumu, ngatinso mwamchitira chokoma Yerubaala ndi nyumba yake, ndi kumchitira monga anayenera manja ake;

17pakuti atate wanga anakugwirirani nkhondo, nataya moyo wake, nakupulumutsani m'dzanja la Amidiyani;

18koma mwaukira nyumba ya atate wanga lero lino, ndi kuwapha ana ake, ndiwo amuna makumi asanu ndi awiri, pa thanthwe limodzi; ndipo mwalonga Abimeleki mwana wa mdzakazi wake, akhale mfumu ya pa eni ake a ku Sekemu, chifukwa ali mbale wanu;

19ngati tsono mwachitira Yerubaala ndi nyumba yake zoona ndi zangwiro lero lino, kondwerani naye Abimeleki, nayenso akondwere nanu;

20Ower. 9.15, 56-57koma ngati simunatero, utuluke moto kwa Abimeleki, nunyeketse eni ake a ku Sekemu ndi nyumba ya Milo; nutuluke moto kwa eni ake a ku Sekemu, ndi kunyumba yake ya Milo, nunyeketse Abimeleki.

21Pamenepo Yotamu anafulumira, nathawa, namuka ku Beere, nakhala komweko, chifukwa cha Abimeleki mbale wake.

Mpanduko wa Gaala

22Abimeleki atakhala kalonga wa Israele zaka zitatu,

231Sam. 16.14Mulungu anatumiza mzimu woipa pakati pa Abimeleki ndi eni ake a ku Sekemu; ndi eni ake a ku Sekemu anamchitira Abimeleki mosakhulupirika;

24kuti chiwawa adachitira ana amuna makumi asanu ndi awiri a Yerubaala chimdzere, ndi kuti mwazi wao uikidwe pa mbale wao Abimeleki anawaphayo, ndi pa eni ake a ku Sekemu, amene analimbikitsa manja ake, awaphe abale ake.

25Ndipo eni ake a ku Sekemu anaika omlalira pamwamba pa mapiri; amene anawawanya onse akudzera njirayi; ndipo anamuuza Abimeleki.

26Ndipo Gaala, mwana wa Ebedi anadza ndi abale ake, napita ku Sekemu; ndi eni ake a ku Sekemu anamkhulupirira.

27Ndipo anatuluka kunka kuminda, natchera mphesa m'mindamo, naponda mphesa, napereka nsembe yolemekeza, nalowa m'nyumba ya mulungu wao, nadya, namwa, natemberera Abimeleki.

281Sam. 25.10Pamenepo Gaala, mwana wa Ebedi anati, Abimeleki ndani, ndi Sekemu ndani, kuti timtumikire? Sindiye mwana wa Yerubaala kodi? Ndi Zebuli kazembe wake? Mutumikire amuna a Hamori atate wa Sekemu; koma ameneyo timtumikire chifukwa ninji?

292Sam. 15.4Mwenzi anthu awa akadakhala m'dzanja langa; ndikadamchotsadi Abimeleki. Ndipo anati kwa Abimeleki, Chulukitsa khamu lako, nutuluke.

30Pamene Zebuli woyang'anira mudzi anamva mau a Gaala mwana wa Ebedi, anapsa mtima.

31Natuma mithenga kwa Abimeleki ku Aruma monyenga nati, Taonani Gaala mwana wa Ebedi ndi abale ake afika ku Sekemu; ndipo taonani, akupandukitsirani mudzi.

32Ndipo tsopano, taukani usiku, inu ndi anthu okhala nanu ndi kulalira kuthengo;

33ndipo kukhale kuti m'mawa, pakutuluka dzuwa, muuke mamawa mugwere mudziwo; ndipo taonani, akakutulukirani iye ndi anthu ali naye, uzimchitira monga lidziwa dzanja lako.

34Pamenepo Abimeleki anauka ndi anthu onse anali naye, usiku; nalalira a ku Sekemu, magulu anai.

35Ndipo Gaala mwana wa Ebedi anatuluka, naima polowera pa chipata cha mudzi; naika Abimeleki ndi anthu anali naye m'molalira.

36Ndipo pamene Gaala anapenya anthuwo anati kwa Zebuli, Taona, alikutsika anthu kuchokera pamwamba pa mapiri. Koma Zebuli ananena naye, Uona mthunzi wa mapiri ndi kuyesa anthu.

37Koma Gaala ananenanso, nati, Tapenya alikutsika anthu pakati pa dziko, ndi gulu limodzi lidzera njira ya ku thundu wa alauli.

38Pamenepo Zebuli anati kwa iye, Pakamwa pako mpoti tsopano, muja udanena, Ndani Abimeleki kuti timtumikire? Awa si anthuwo unawapeputsa? Utuluke tsopano, nulimbane nao.

39Ndipo Gaala anatuluka pamaso pao pa eni ake a ku Sekemu, nalimbana ndi Abimeleki.

40Koma Abimeleki anampirikitsa, nathawa iye pamaso pake; nagwa olasidwa ambiri mpaka polowera pa chipata.

41Ndipo Abimeleki anakhala ku Aruma; ndi Zebuli anaingitsa Gaala ndi abale ake kuti asakhale m'Sekemu.

42Ndipo kunali m'mawa mwake, kuti anthu anatuluka kunka kuminda; ndipo anauza Abimeleki.

43Pamenepo anatenga anthu, nawagawa magulu atatu, nalalira m'minda; napenya, ndipo taonani, anthu alimkutuluka m'mudzi; nawaukira iye nawakantha.

44Ndi Abimeleki ndi magulu okhala naye anathamanga naima polowera pa chipata cha mudzi; ndi magulu awiriwo anagwera onse okhala m'munda, nawakantha.

451Maf. 12.25Ndipo Abimeleki analimbana ndi mudzi tsiku lija lonse; nalanda mudzi nawapha anthu anali m'mwemo; napasula mudzi; nawazapo mchere.

46Ndipo pamene eni ake onse a nsanja ya ku Sekemu anachimva, analowa m'ngaka ya nyumba ya Eliberiti.

47Ndipo anauza Abimeleki kuti amuna onse a nsanja ya ku Sekemu asonkhane.

48Pamenepo Abimeleki anakwera kunka kuphiri la Zalimoni, iye ndi anthu onse anali naye; natenga nkhwangwa m'dzanja lake Abimeleki, nadula nthambi kumitengo, nainyamula ndi kuiika paphewa pake, nati kwa anthu okhala naye, Ichi munachiona ndachita, fulumirani, muchite momwemo.

49Ndi anthu onse anadulanso yense nthambi yake, natsata Abimeleki, naziika pangaka, natentha nazo ngakayo ndi moto; motero anthu onse a nsanja ya ku Sekemu anafanso, amuna ndi akazi ngati chikwi chimodzi.

Imfa ya Abimeleki

50Pamenepo Abimeleki anamuka ku Tebezi, naumangira Tebezi misasa, naulanda.

51Koma m'mudzimo munali nsanja yolimba nathawira kumeneko amuna ndi akazi onse, ndi eni ake onse a mudziwo, nadzitsekereza m'mwemo, nakwera patsindwi pa nsanja.

52Ndipo Abimeleki anafika kunsanja, nalimbana nayo nkhondo, nayandikira kukhomo kwa nsanja, aitenthe ndi moto.

532Sam. 11.21Ndipo mkazi wina anaponya mwana wa mphero pamutu pa Abimeleki, naphwanya bade lake.

541Sam. 31.4Pamenepo anaitana msanga mnyamata wake wosenza zida zake, nanena naye, Solola lupanga lako nundiphe, angamanenere anthu, ndi kuti, Anamupha ndi mkazi. Nampyoza mnyamata wake, nafa iye.

55Pamene amuna a Israele anaona kuti adafa Abimeleki anamuka yense kumalo kwake.

56Ower. 9.24; Yob. 31.3; Miy. 5.22Momwemo Mulungu anambwezera Abimeleki choipacho anachitira atate wake ndi kuwapha abale ake makumi asanu ndi awiri.

57Ower. 8.20Ndipo Mulungu anawabwezera choipa chonse cha amuna a ku Sekemu pamitu pao, ndipo linawagwera temberero la Yotamu mwana wa Yerubaala.

Blog
About Us
Message
Site Map

Who We AreWhat We EelieveWhat We Do

Terms of UsePrivacy Notice

2025 by iamachristian.org,Inc All rights reserved.

Home
Gospel
Question
Blog
Help