EZEKIELE 33 - Buku Lopatulika Bible 2014

Udindo wa mneneri

1Ndipo anandidzera mau a Yehova, akuti,

22Sam. 18.24-25; Ezk. 3.11; 14.17Wobadwa ndi munthu iwe, Nena ndi ana a anthu a mtundu wako, uziti nao, Ndikafikitsira dziko lililonse lupanga, nakatenga eni dziko munthu wa pakati pao, nakamuika awadikirire,

3nakaona iye lupanga lilikudzera dziko, nakaomba lipenga ndi kuchenjeza anthu;

4ndipo wina, kumva adamva mau a lipenga, koma osalabadira, likadza lupanga, nilimchotsa, wadziphetsa ndi mtima wake.

5Anamva mau a lipenga, osawalabadira, wadziphetsa ndi mtima wake; akadalabadira, akadalanditsa moyo wake.

6Ezk. 3.18Koma mlonda akaona lupanga likudza, osaomba lipenga, osachenjeza anthu, nilidza lupanga, nilichotsa mwa iwo; munthu atengedwadi m'mphulupulu zake, koma mwazi wake ndidzaufunsa pa dzanja la mlonda.

7Ezk. 3.17Iwe tsono, wobadwa ndi munthu, ndakuika mlonda wa nyumba ya Israele, m'mwemo imva mau a pakamwa panga, nundichenjezere iwo.

8Ndikati Ine kwa woipa, Woipawe, udzafa ndithu, osanena iwe kumchenjeza woipayo aleke njira yake, woipa uyo adzafa m'mphulupulu yake, koma mwazi wake ndidzaufunsa pa dzanja lako.

9Koma ukachenjeza woipa za njira yake, aileke; koma iye osaileka njira yake, adzafa m'mphulupulu mwake iye, koma iwe walanditsa moyo wako.

10Ndipo iwe wobadwa ndi munthu, nena kwa nyumba ya Israele, Mumatero inu ndi kuti, Zolakwa zathu ndi zochimwa zathu zitikhalira, ndipo tichita nazo liwondewonde, tidzakhala ndi moyo bwanji?

112Sam. 14.14; Ezk. 18.23, 32Uziti nao, Pali Ine, ati Ambuye Yehova, sindikondwera nayo imfa ya woipa, koma kuti woipa aleke njira yake, nakhale ndi moyo; bwererani, bwererani, kuleka njira zanu zoipa, muferenji inu nyumba ya Israele?

122Mbi. 7.14; Ezk. 3.20; 18.24-27Ndipo iwe wobadwa ndi munthu, unene ndi ana a anthu a mtundu wako, Cholungama cha wolungama sichidzamlanditsa tsiku la kulakwa kwake, ndi kunena za choipa cha woipa, sadzagwa nacho tsiku lakubwerera iye kuleka choipa chake; ndi munthu wolungama sadzakhoza kukhala ndi moyo ndi chilungamo chake tsiku lakuchimwa iye.

13Ezk. 3.20; 18.24-27Ndikanena kwa wolungama kuti adzakhala ndi moyo ndithu, akatama chilungamo chake, akachita chosalungama, sizikumbukika zolungama zake zilizonse; koma m'chosalungama chake anachichita momwemo adzafa.

14Ezk. 3.18; 18.27Ndipo ndikanena kwa woipa, Udzafa ndithu: koma akabwerera iye kuleka tchimo lake, nakachita choyenera ndi cholungama;

15Ezk. 18.7; Luk. 19.5woipayo akabweza chikole, nakabweza icho anachilanda mwachifwamba, nakayenda m'malemba a moyo wosachita chosalungama, adzakhala ndi moyo ndithu, sadzafa.

16Ezk. 18.22Zoipa zake zilizonse anazichita sizidzakumbukika zimtsutse, anachita choyenera ndi cholungama, adzakhala ndi moyo ndithu.

17Ezk. 18.25, 29Koma ana a anthu a mtundu wako akuti, Njira ya Ambuye siiyenera; koma iwowa njira yao siiyenera.

18Ezk. 18.26-27Akabwerera wolungama kuleka chilungamo chake, nakachita chosalungama, adzafa m'mwemo.

19Ndipo woipa akabwerera kuleka choipa chake, nakachita choyenera ndi cholungama, adzakhala ndi moyo nazo.

20Ezk. 33.17Koma munati, Njira ya Ambuye siiyenera. Nyumba ya Israele inu, ndidzakuweruzani, yense monga mwa njira zake.

Kulangidwa kwa Aisraele chifukwa cha zoipa zao

21 2Maf. 25.4 Ndipo kunali chaka chakhumi ndi chiwiri cha undende wathu, mwezi wakhumi, tsiku lachisanu la mweziwo, anandidzera wina wopulumuka ku Yerusalemu, ndi kuti, Wakanthidwa mudzi.

22Ezk. 1.3Koma dzanja la Yehova linandikhalira madzulo, asanandifike wopulumukayo; ndipo ananditsegula pakamwa mpaka anandifika m'mawa, m'mwemo panatseguka pakamwa panga, wosakhalanso wosalankhula.

23Ndipo anandidzera mau a Yehova, akuti,

24Yes. 51.2; Mac. 7.5Wobadwa ndi munthu iwe, iwo okhala kumabwinja a dziko la Israele anena, ndi kuti, Abrahamu anali yekha, nakhala nalo dziko cholowa chake; koma ife ndife ambiri, dzikoli lipatsidwa kwa ife cholowa chathu.

25Gen. 9.4; Deut. 12.16Chifukwa chake unene nao, Atero Ambuye Yehova, Mumadyera kumodzi ndi mwazi, mumakwezera maso anu kumafano anu, ndi kukhetsa mwazi; ndipo kodi mudzakhala nalo dziko cholowa chanu?

26Ezk. 18.6Mumatama lupanga lanu, mumachita chonyansa, mumaipsa yense mkazi wa mnansi wake; ndipo kodi mudzakhala nalo dziko cholowa chanu?

27Uzitero nao, Atero Ambuye Yehova, Pali Ine, iwo okhala kumabwinja adzagwadi ndi lupanga, ndi iye ali kuthengo koyera ndidzampereka kwa zilombo, adyedwe nazo; ndi iwo okhala m'malinga ndi m'mapanga adzafa ndi mliri.

28Ndipo ndidzasanduliza dziko likhale lachipululu ndi lodabwitsa, ndi mphamvu yake yodzikuza idzatha, ndi mapiri a Israele adzakhala achipululu, osapitako munthu.

29Pamenepo adzadziwa kuti Ine ndine Yehova, posanduliza Ine dziko likhale lachipululu ndi lodabwitsa, chifukwa cha zonyansa zao zonse anazichita.

30Ndipo iwe wobadwa ndi munthu, ana a anthu a mtundu wako anena za iwe kumakoma ndi kumakomo a nyumba zao, nanenana yense ndi mbale wake, ndi kuti, Tiyeni tikamve mau ofuma kwa Yehova.

31Yes. 29.13; Mat. 13.22; 1Yoh. 3.18Ndipo akudzera monga amadzera anthu, nakhala pansi pamaso pako ngati anthu anga, namva mau ako, koma osawachita; pakuti pakamwa pao anena mwachikondi, koma mtima wao utsata phindu lao.

32Ndipo taona, akuyesa iwe ngati nyimbo yachikondi ya woimba bwino, woimba limba bwino; pakuti akumva mau ako, koma osawachita.

331Sam. 3.20Ndipo pakuchitika ichi, pakuti chifikadi, pamenepo adzadziwa kuti panali mneneri pakati pao.

Blog
About Us
Message
Site Map

Who We AreWhat We EelieveWhat We Do

Terms of UsePrivacy Notice

2025 by iamachristian.org,Inc All rights reserved.

Home
Gospel
Question
Blog
Help