MASALIMO 29 - Buku Lopatulika Bible 2014

Achenjeza akulu alemekeze MulunguSalimo la Davide.

1 1Mbi. 16.28-29 Perekani kwa Yehova, inu ana a amphamvu,

perekani kwa Yehova ulemerero ndi mphamvu.

2Perekani kwa Yehova ulemerero wa dzina lake,

gwadirani Yehova moyera ndi mokometsetsa.

3 Yes. 30.30 Liu la Yehova lili pamadzi;

Mulungu wa ulemerero agunda,

ndiye Yehova pa madzi ambiri.

4Liu la Yehova ndi lamphamvu;

liu la Yehova ndi lalikulukulu.

5Liu la Yehova lithyola mitengo yamkungudza;

inde Yehova athyola mikungudza ya ku Lebanoni.

6Aitumphitsa monga mwanawang'ombe;

Lebanoni ndi Sirioni monga msona wa njati.

7Liu la Yehova ligawa malawi a moto.

8Liu la Yehova ligwedeza chipululu;

Yehova agwedeza chipululu cha Kadesi.

9Liu la Yehova liswetsa nyama zazikazi,

ndipo lipulula nkhalango;

ndipo m'Kachisi mwake zonse zili m'mwemo zimati, Ulemerero.

10 Mas. 10.16 Yehova anakhala pa chigumula,

inde Yehova akhala mfumu kunthawi yonka muyaya.

11 Mas. 28.8 Yehova adzapatsa anthu ake mphamvu,

Yehova adzadalitsa anthu ake ndi mtendere.

Blog
About Us
Message
Site Map

Who We AreWhat We EelieveWhat We Do

Terms of UsePrivacy Notice

2025 by iamachristian.org,Inc All rights reserved.

Home
Gospel
Question
Blog
Help