CHIVUMBULUTSO 7 - Buku Lopatulika Bible 2014

Aisraele okhulupirika alanditsidwa

1 Dan. 7.2 Zitatha izi ndinaona angelo anai alinkuimirira pangodya zinai za dziko, akugwira mphepo zinai za dziko, kuti ingaombe mphepo padziko, kapena panyanja, kapena pa mtengo uliwonse.

2Ndipo ndinaona mngelo wina, anakwera kuchokera potuluka dzuwa, ali nacho chizindikiro cha Mulungu wamoyo: ndipo anafuula ndi mau akulu kuitana angelo anai, amene adalandira mphamvu kuipsa dziko ndi nyanja,

3Ezk. 9.4; Chiv. 9.4nanena, Musaipse dziko, kapena nyanja, kapena mitengo, kufikira tidasindikiza chizindikiro akapolo a Mulungu wathu, pamphumi pao.

4Ndipo ndinamva chiwerengo cha iwo osindikizidwa chizindikiro, zikwi makumi khumi ndi makumi anai mphambu anai, osindikizidwa chizindikiro mwa mafuko onse a ana a Israele.

5Mwa fuko la Yuda anasindikizidwa chizindikiro

zikwi khumi ndi ziwiri.

Mwa fuko la Rubeni zikwi khumi ndi ziwiri.

Mwa fuko la Gadi zikwi khumi ndi ziwiri.

6Mwa fuko la Asere zikwi khumi ndi ziwiri.

Mwa fuko la Nafutali zikwi khumi ndi ziwiri.

Mwa fuko la Manase zikwi khumi ndi ziwiri.

7Mwa fuko la Simeoni zikwi khumi ndi ziwiri.

Mwa fuko Levi zikwi khumi ndi ziwiri.

Mwa fuko la Isakara zikwi khumi ndi ziwiri.

8Mwa fuko la Zebuloni zikwi khumi ndi ziwiri.

Mwa fuko la Yosefe zikwi khumi ndi ziwiri.

Mwa fuko la Benjamini anasindikizidwa chizindikiro

zikwi khumi ndi ziwiri.

Maonekedwe m'ulemerero a iwo amene anaphedwa chifukwa cha Khristu

9 Aro. 11.25; Chiv. 3.5, 18; 5.9 Zitatha izi ndinapenya, taonani, khamu lalikulu, loti palibe munthu anakhoza kuliwerenga, ochokera mwa mtundu uliwonse, ndi mafuko ndi anthu ndi manenedwe, akuimirira kumpando wachifumu ndi pamaso pa Mwanawankhosa, atavala zovala zoyera, ndi makhwatha a kanjedza m'manja mwao;

10Yes. 43.11ndipo afuula ndi mau akulu, nanena, Chipulumutso kwa Mulungu wathu wakukhala pa mpando wachifumu, ndi kwa Mwanawankhosa.

11Ndipo angelo onse anaimirira pozinga mpando wachifumu, ndi akulu, ndi zamoyozo zinai; ndipo anagwa nkhope yao pansi kumpando wachifumu, nalambira Mulungu,

12Chiv. 5.13-14ndi kunena, Amen: Thamo ndi ulemerero, ndi nzeru, ndi chiyamiko, ndi ulemu, ndi chilimbiko, ndi mphamvu zikhale kwa Mulungu wathu kufikira nthawi za nthawi. Amen.

13Chiv. 7.9Ndipo mmodzi wa akulu anayankha, nanena ndi ine, Iwo ovala zovala zoyera ndiwo ayani, ndipo achokera kuti?

14Yes. 1.18; 1Yoh. 1.7; Chiv. 6.9Ndipo ndinati kwa iye, Mbuye wanga, mudziwa ndinu. Ndipo anati kwa ine, Iwo ndiwo akutuluka m'chisautso chachikulu; ndipo anatsuka zovala zao, naziyeretsa m'mwazi wa Mwanawankhosa.

15Chifukwa chake ali kumpando wachifumu wa Mulungu; ndipo amtumikira Iye usana ndi usiku m'Kachisi mwake; ndipo Iye wakukhala pa mpando wachifumu adzawachitira mthunzi,

16Mas. 121.6; Yes. 49.10sadzamvanso njala, kapena ludzu, kapena silidzawatentha dzuwa, kapena chitungu chilichonse;

17Mas. 23.1-2; Yes. 25.8chifukwa Mwanawankhosa wakukhala pakati pa mpando wachifumu adzawaweta, nadzawatsogolera ku akasupe a madzi amoyo, ndipo Mulungu adzawapukutira misozi yonse pamaso pao.

Blog
About Us
Message
Site Map

Who We AreWhat We EelieveWhat We Do

Terms of UsePrivacy Notice

2025 by iamachristian.org,Inc All rights reserved.

Home
Gospel
Question
Blog
Help