1 Yes. 55.12 Ombani m'manja, mitundu yonse ya anthu;
fuulirani kwa Mulungu ndi liu la kuimbitsa.
2 Mala. 1.14 Pakuti Yehova Wam'mwambamwamba ndiye woopsa;
ndiye mfumu yaikulu pa dziko lonse lapansi.
3Atigonjetsera anthu,
naika amitundu pansi pa mapazi athu.
4 1Pet. 1.4 Atisankhira cholowa chathu,
chokometsetsa cha Yakobo amene anamkonda.
5Mulungu wakwera ndi mfuu,
Yehova ndi liu la lipenga.
6Imbirani Mulungu, imbirani;
imbirani mfumu yathu, imbirani.
7 Zek. 14.9 Pakuti Mulungu ndiye mfumu ya dziko lonse lapansi;
imbirani ndi chilangizo.
8 Mas. 22.28; Chiv. 19.6 Mulungu ndiye mfumu ya amitundu,
Mulungu akhala pa mpando wachifumu wake woyera.
9 Aro. 4.11-12 Akulu a anthu asonkhana
akhale anthu a Mulungu wa Abrahamu,
pakuti zikopa za dziko lapansi nza Mulungu;
akwezeka kwakukulu Iyeyo.
Who We AreWhat We EelieveWhat We Do
2025 by iamachristian.org,Inc All rights reserved.