1Ndipo munthu akabwera nacho chopereka ndicho nsembe yaufa ya kwa Yehova, chopereka chake chizikhala cha ufa wosalala; ndipo athirepo mafuta, ndi kuikapo lubani.
2Ndipo abwere nayo kwa ana a Aroni, ansembewo; natengeko ufa, ndi mafuta odzala manja, ndi lubani wake wonse; ndipo wansembeyo aitenthe chikumbutso chake pa guwa la nsembe, ndiyo nsembe yamoto, ya fungo lokoma la kwa Yehova.
3Ndipo chotsalira cha nsembe yaufa chikhale cha Aroni ndi ana ake; ndicho chopatulika kwambiri cha nsembe zamoto za Yehova.
4Ndipo ukabwera nacho chopereka ndicho nsembe yaufa, yophika mumchembo, chizikhala cha timitanda ta ufa wosalala topanda chotupitsa tosanganiza ndi mafuta, kapena timitanda taphanthi topanda chotupitsa todzoza ndi mafuta.
5Ndipo nsembe yaufa yako ikakhala yokazinga m'chiwaya, ikhale ya ufa wosalala wopanda chotupitsa, wosanganiza ndi mafuta.
6Uphwanye, nuthirepo mafuta; ndiyo nsembe yaufa.
7Ndipo chopereka chako chikakhala nsembe yaufa ya mumphika, chikhale cha ufa wosalala ndi mafuta.
8Ndipo ubwere nayo nsembe yaufa yopangika ndi izi kwa Yehova; ndipo atabwera nacho kwa wansembe, iyeyo apite nacho ku guwa la nsembe.
9Ndipo wansembeyo atengeko chikumbutso pa nsembe yaufa, nachitenthe pa guwa la nsembe; ndicho nsembe yamoto ya fungo lokoma la kwa Yehova.
10Ndipo chotsalira cha nsembe yaufa chikhale cha Aroni ndi ana ake; ndicho chopatulika kwambiri cha nsembe zamoto za Yehova.
11Mat. 16.12; 1Ako. 5.8; Agal. 5.9Nsembe iliyonse yaufa, imene mubwera nayo kwa Yehova, isapangike ndi chotupitsa, pakuti musamatenthera Yehova nsembe yamoto yachotupitsa, kapena yauchi.
12Monga chopereka cha zipatso zoyamba muzipereka izi kwa Yehova: koma asazifukize pa guwa la nsembe zichite fungo lokoma.
132Mbi. 13.5; Mrk. 9.49Ndipo chopereka chako chilichonse cha nsembe yaufa uzichikoleretsa ndi mchere; usasowe mchere wa chipangano cha Mulungu wako pa nsembe yako yaufa; pa zopereka zako zonse uzipereka mchere.
14Ndipo ukabwera nayo nsembe yaufa ya zipatso zoyamba kwa Yehova, uzibwera nayo nsembe yako ya zipatso zoyamba ikhale ya ngala zoyamba kucha, zoumika pamoto, zokonola.
15Ndipo uthirepo mafuta, ndi kuikapo lubani; ndiyo nsembe yaufa.
16Ndipo wansembe atenthe chikumbutso chake, atatapa pa tirigu wake wokonola, ndi pa mafuta ake, ndi kutenga lubani lake lonse; ndiyo nsembe yamoto ya kwa Yehova.
Who We AreWhat We EelieveWhat We Do
2025 by iamachristian.org,Inc All rights reserved.