2 MBIRI 13 - Buku Lopatulika Bible 2014

Abiya ndi Yerobowamu agwirana nkhondo, Israele akanthidwa

1Ndipo chaka chakhumi mphambu zisanu ndi zitatu cha Yerobowamu, Abiya analowa ufumu wa Yuda.

2Anakhala mfumu m'Yerusalemu zaka zitatu; ndi dzina la make ndiye Mikaya mwana wamkazi wa Uriyele wa ku Gibea. Ndipo panali nkhondo pakati pa Abiya ndi Yerobowamu.

3Ndipo Abiya anayambana nkhondo ali ndi khamu la ngwazi za nkhondo, amuna osankhika zikwi mazana anai; Yerobowamu atandandalitsa nkhondo yake ilimbane naye ndi amuna osankhika zikwi mazana asanu ndi atatu, ndiwo ngwazi zamphamvu.

4Ndipo Abiya anaimirira pa phiri la Zemaraimu, ndilo ku mapiri a Efuremu, nati, Mundimvere Yerobowamu ndi Aisraele onse;

5Num. 18.19; 2Sam. 7.12-13, 16simudziwa kodi kuti Yehova Mulungu wa Israele anapereka chiperekere ufumu wa Israele kwa Davide, kwa iye ndi ana ake, ndi pangano lamchere?

61Maf. 11.26Koma Yerobowamu mwana wa Nebati mnyamata wa Solomoni mwana wa Davide anauka, napandukana ndi mbuye wake.

7Ndipo anamsonkhanira amuna achabe, anthu opanda pake, ndiwo anadzilimbikitsa kutsutsana naye Rehobowamu mwana wa Solomoni, muja Rehobowamu anali mnyamata ndi woolowa mtima, wosakhoza kuwalaka.

81Maf. 12.28Ndipo tsopano, mukuti mudzilimbikitse kutsutsana nao ufumu wa Yehova m'dzanja la ana a Davide; ndinu aunyinji ambiri, ndi pamodzi nanu anaang'ombe agolide adawapanga Yerobowamu akhale milungu yanu.

9Simunapirikitsa kodi ansembe a Yehova, ana a Aroni, ndi Alevi, ndi kudziikira ansembe monga amachita anthu a m'maiko ena? Kuti aliyense wakudza kudzipatulira ndi mwanawang'ombe, ndi nkhosa zamphongo zisanu ndi ziwiri, yemweyo ndiye wansembe wa iyo yosati milungu.

10Koma ife, Yehova ndiye Mulungu wathu, sitinamsiya Iye; ndi ansembe tili nao akutumikira Yehova ana a Aroni, ndi Alevi, m'ntchito mwao,

11nafukizira Yehova nsembe zopsereza m'mawa ndi m'mawa, ndi madzulo onse, ndi zonunkhira za fungo lokoma, nakonza mkate woonekera pa gome lopatulika, ndi choikapo nyali chagolide ndi nyali zake, ziyake madzulo onse; pakuti tisunga chilangizo cha Yehova Mulungu wathu, koma inu mwamsiya Iye.

12Ndipo taonani, Mulungu ali nafe, wotitsogolera ndi ansembe ake, ndi malipenga oliza nao chokweza, kukulizirani inu chokweza. Ana a Israele inu, musalimbane naye Yehova Mulungu wa makolo anu; pakuti simudzapindula nako.

13Koma Yerobowamu anazunguliritsa owalalira, awadzere kumbuyo; momwemo iwowa anali kumaso kwa Yuda, ndi owalalira anali kumbuyo kwao.

14Ndipo pocheuka Yuda, taonani, nkhondo inayambana nao kumaso ndi kumbuyo; nafuulira iwo kwa Yehova, ndi ansembe analiza malipenga.

15Pamenepo amuna a Yuda anafuula chokweza; ndipo pofuula amuna a Yuda, kunachitika kuti Mulungu anakantha Yerobowamu ndi Aisraele onse pamaso pa Abiya ndi Yuda.

16Ndipo ana a Israele anathawa pamaso pa Yuda, nawapereka Mulungu m'dzanja lao.

17Ndipo Abiya ndi anthu ake anawakantha makanthidwe akulu; nagwa, nafa amuna osankhika zikwi mazana asanu a Israele.

18Momwemo anachepetsedwa ana a Israele nthawi ija, nalakika ana a Yuda; popeza anatama Yehova Mulungu wa makolo ao.

19Ndipo Abiya analondola Yerobowamu, namlanda midzi yake, Betele ndi milaga yake, ndi Yesana ndi milaga yake, ndi Efuroni ndi milaga yake.

20Ndi Yerobowamu sanaonenso mphamvu m'masiku a Abiya, namkantha Yehova, nafa iye.

21Koma Abiya anakula mphamvu, nadzitengera akazi khumi ndi anai, nabala ana amuna makumi awiri mphambu awiri, ndi ana akazi khumi mphamvu asanu ndi mmodzi.

22Machitidwe ena tsono a Abiya, ndi mayendedwe ake, ndi mau ake, alembedwa m'buku lomasulira la mneneri Ido.

Blog
About Us
Message
Site Map

Who We AreWhat We EelieveWhat We Do

Terms of UsePrivacy Notice

2025 by iamachristian.org,Inc All rights reserved.

Home
Gospel
Question
Blog
Help