NUMERI 6 - Buku Lopatulika Bible 2014

Za chowinda cha Mnaziri

1Ndipo Yehova ananena ndi Mose, nati,

2Ower. 13.5; Aro. 1.1Nena ndi ana a Israele, nuti nao, Mwamuna kapena mkazi akadzipatulira kulonjeza chowinda cha Mnaziri, kudzipatulira kwa Yehova;

3Amo. 2.12; Luk. 1.15azisala vinyo ndi kachasu; asamwe vinyo wosasa, kapena kachasu wosasa, kapena chakumwa chonse cha mphesa, asamwe; asadye mphesa zaziwisi kapena zouma.

4Masiku onse a kusala kwake asadye kanthu kopangika ndi mphesa, kuyambira nthanga zake kufikira khungu lake.

5Ower. 16.17Masiku onse a chowinda chake chakusala, lumo lisapite pamutu pake; kufikira adatha masikuwo adadzipatulira kwa Yehova, azikhala wopatulika; aleke nzera za tsitsi lake zimeretu.

6Masiku onse akudzipatulira kwa Yehova asayandikize mtembo.

7Asadzidetse ndi atate wake, kapena mai wake, mbale wake, kapena mlongo wake, akafa iwowa; popeza chowindira Mulungu wake chili pamutu pake.

8Masiku onse a kusala kwake akhala wopatulikira kwa Yehova.

9Mac. 18.18Munthu akafa chikomo pali iye, ndipo akadetsa mutu wake wowinda; pamenepo azimeta mutu wake tsiku la kumyeretsa kwake, tsiku lachisanu ndi chiwiri aumete.

10Ndipo tsiku lachisanu ndi chitatu adze nazo njiwa ziwiri, kapena maunda awiri, kwa wansembe;

11ndipo wansembe akonze imodzi nsembe yauchimo, ndi ina nsembe yopsereza, namtetezere popeza anachimwa nao mtembowo; ndipo apatulire mutu wake tsiku lomwelo.

12Ndipo awapatulire Yehova masiku a kusala kwake, nadze nayo nkhosa yamphongo ya chaka chimodzi ikhale nsembe yopalamula; koma masiku adapitawa azikhala chabe, popeza anadetsa kusala kwake.

13 Mac. 21.26 Ndipo chilamulo cha Mnaziri, atatha masiku a kusala kwake ndi ichi: azidza naye ku khomo la chihema chokomanako;

14pamenepo abwere nacho chopereka chake kwa Yehova, nkhosa yamphongo ya chaka chimodzi yopanda chilema, ikhale nsembe yopsereza, ndi nkhosa yaikazi yopanda chilema ikhale nsembe yauchimo, ndi nkhosa yamphongo yopanda chilema ikhale nsembe yoyamika;

15ndi dengu la mkate wopanda chotupitsa, timitanda ta ufa wosalala tosanganiza ndi mafuta, ndi timitanda taphanthi todzoza ndi mafuta, ndi nsembe yao yaufa, ndi nsembe zao zothira.

16Ndipo wansembe azibwera nazo pamaso pa Yehova, nakonze nsembe yake yauchimo, ndi nsembe yake yopsereza;

17naphe nkhosa yamphongo yoyamika ya Yehova, pamodzi ndi dengu la mkate wopanda chotupitsa; wansembe akonzenso nsembe yake yaufa, ndi nsembe yake yothira.

18Pamenepo Mnaziriyo amete mutu wake wa kusala kwake pa khomo la chihema chokomanako, natenge tsitsi la pa mutu wake wa kusala, naliike pamoto wokhala pansi pa nsembe yoyamika.

19Ndipo wansembe atenge mwendo wamwamba wophika wa nkhosa yamphongo, ndi kamtanda kamodzi kopanda chotupitsa ka m'dengu, ndi kamtanda kaphanthi kopanda chotupitsa kamodzi, ndi kuziika m'manja mwa Mnaziri, atameta kusala kwake;

20ndipo wansembe aziweyula nsembe yoweyula pamaso pa Yehova; ichi nchopatulikira wansembe, pamodzi ndi nganga ya nsembe yoweyula, pamodzi ndi mwendo wa nsembe yokweza; ndipo atatero Mnaziri amwe vinyo.

21Ichi ndi chilamulo cha Mnaziri wakuwinda, ndi cha chopereka chake cha Yehova chifukwa cha kusala kwake, pamodzi nacho chimene dzanja lake likachipeza; azichita monga mwa chowinda chake anachiwinda, mwa chilamulo cha kusala.

Mau a mdalitso

22Ndipo Yehova ananena ndi Mose, ndi kuti,

23Nena ndi Aroni ndi ana ake, ndi kuti, Uzidalitsa ana a Israele motero; uziti nao,

24 Mas. 121.3-8 Yehova akudalitse iwe, nakusunge;

25 Mas. 31.16 Yehova awalitse nkhope yake pa iwe, nakuchitire chisomo;

26 Mas. 4.6; Yoh. 14.27 Yehova akweze nkhope yake pa iwe, nakupatse mtendere.

27 Mas. 115.12; Yes. 43.7; Dan. 9.19 Potero aike dzina langa pa ana a Israele; ndipo ndidzawadalitsa.

Blog
About Us
Message
Site Map

Who We AreWhat We EelieveWhat We Do

Terms of UsePrivacy Notice

2025 by iamachristian.org,Inc All rights reserved.

Home
Gospel
Question
Blog
Help