1Ndipo akachimwa munthu, wakuti adamva mau akuwalumbiritsa, ndiye mboni, kapena wakuona, kapena wakudziwa, koma osawulula, azisenza mphulupulu yake;
22Ako. 6.17kapena munthu akakhudza chilichonse chodetsa kapena mtembo wa nyama yodetsa, kapena mtembo wa choweta chodetsa, kapena mtembo wa chokwawa chodetsa, kungakhale kudambisikira, ali wodetsedwa, ndi wopalamula.
3Kapena akakhudza chodetsa cha munthu, ndicho chodetsa chilichonse akhala wodetsedwa nacho, ndipo chidambisikira; koma pochizindikira akhala wopalamula:
4kapena munthu akalumbira ndi milomo yake osalingirira kuchita choipa, kapena kuchita chabwino, chilichonse munthu akalumbira osalingirira, ndipo chidambisikira; koma pochizindikira akhala wopalamula chimodzi cha izi:
5ndipo kudzali, atapalamula chimodzi cha izi, aziwulula chimene adachimwa nacho;
6nadze nayo nsembe yopalamula kwa Yehova chifukwa cha kulakwa kwake adachimwira, ndiyo nkhosa yaikazi, kapena mbuzi yaikazi, ikhale nsembe yauchimo; ndipo wansembe amchitire chomtetezera chifukwa cha kuchimwa kwake.
7Ndipo chuma chake chikapanda kufikira nkhosa, wochimwayo adze nayo kwa Yehova nsembe yake yopalamula, njiwa ziwiri, kapena maunda awiri; imodzi ikhale ya nsembe yauchimo, ndi ina ya nsembe yopsereza.
8Ndipo adze nazo kwa wansembe, ndiye ayambe kubwera nayo ija ya kwa nsembe yauchimo, napotole mutu wake pakhosi pake, osauchotsa;
9nawazeko mwazi wa nsembe yauchimo pa mbali ya guwa la nsembe; ndi mwazi wotsalira aukamulire patsinde pa guwa la nsembe; ndiyo nsembe yauchimo.
10Ndipo aikonze inzake ikhale nsembe yopsereza, monga mwa lemba lake; ndipo wansembe amchitire chomtetezera chifukwa cha kuchimwa adachimwira, ndipo adzakhululukidwa.
11Koma chuma chake chikapanda kufikira njiwa ziwiri kapena maunda awiri, wochimwayo azidza nacho chopereka chake limodzi la magawo khumi la efa la ufa wosalala, likhale la nsembe yauchimo; asamaikapo mafuta, kapena kuikapo lubani ai; pakuti ndicho nsembe yauchimo.
12Ndipo adze nacho kwa wansembe, ndi wansembeyo atengeko wodzala manja ukhale chikumbutso chake, nachitenthe pa guwa la nsembe monga umo amachitira nsembe zamoto za Yehova; ndiyo nsembe yauchimo.
13Ndipo wansembe amchitire chomtetezera chifukwa cha kuchimwa kwake adachimwira chimodzi cha izi, ndipo adzakhululukidwa; ndipo chotsalira chikhale cha wansembe, monga umo amachitira chopereka chaufacho.
14Ndipo Yehova ananena ndi Mose, nati,
15Munthu akachita mosakhulupirika, nakachimwa osati dala, pa zopatulika za Yehova, azidza nayo nsembe yake yopalamula kwa Yehova, ndiyo nkhosa yamphongo yopanda chilema, ya m'gulu lake, monga umayesa mtengo wake potchula masekeli a siliva, kunena sekeli wa malo opatulika, ikhale nsembe yopalamula;
16ndipo abwezere cholakwira chopatulikacho, naonjezepo limodzi la magawo asanu, napereke kwa wansembe; ndi wansembeyo amchitire chomtetezera ndi nkhosa yamphongo ya nsembe yopalamula; ndipo adzakhululukidwa.
17Ndipo munthu akachimwa, nakachita china cha zinthu zilizonse aziletsa Yehova; angakhale analibe kudziwa, koma wapalamula, azisenza mphulupulu yake.
18Nadze nayo kwa wansembe nkhosa yamphongo yopanda chilema ya m'khola lake, monga umayesa mtengo wake, ikhale nsembe yopalamula; ndipo wansembeyo amchitire chomtetezera chifukwa cha kusachimwa dala kwake, osakudziwa; ndipo adzakhululukidwa.
19Iyo ndiyo nsembe yopalamula; munthuyu anapalamula ndithu pamaso pa Yehova.
Who We AreWhat We EelieveWhat We Do
2025 by iamachristian.org,Inc All rights reserved.