1 AKORINTO 9 - Buku Lopatulika Bible 2014

Ufulu ndi ulamuliro wa mtumwiyo

1 Mac. 9.15; 22.18; 1Ako. 4.15 Kodi sindine mfulu? Kodi sindine mtumwi? Kodi sindinaona Yesu Ambuye wathu? Kodi simuli inu ntchito yanga mwa Ambuye?

22Ako. 3.2Ngati sindili mtumwi kwa ena, komatu ndili kwa inu; pakuti chizindikiro cha utumwi wanga ndi inu mwa Ambuye.

3Chodzikanira changa kwa iwo amene andifunsa ine ndi ichi:

41Ako. 9.14Kodi tilibe ulamuliro wa kudya ndi kumwa?

5Kodi tilibe ulamuliro wakuyendayenda naye mkazi, ndiye mbale, monganso atumwi ena, ndi abale a Ambuye, ndi Kefa?

62Ate. 3.8-9Kapena kodi ife tokha, Barnabasi ndi ine tilibe ulamuliro wakusagwira ntchito?

7Deut. 20.6Msilikali ndani achita nkhondo, nthawi iliyonse, nadzifunira zake yekha? Aoka mipesa ndani, osadya chipatso chake? Kapena aweta gulu ndani, osadya mkaka wake wa gululo? Kodi ndilankhula izi monga mwa anthu?

8Kapena chilamulo sichinenanso zomwezo?

9Deut. 25.4Pakuti m'chilamulo cha Mose mwalembedwa, Usapunamitsa ng'ombe pakupuntha iyo dzinthu. Kodi Mulungu asamalira ng'ombe?

102Tim. 2.6Kapena achinena ichi konsekonse chifukwa cha ife? Pakuti, chifukwa cha ife kwalembedwa: popeza wolima ayenera kulima mwa chiyembekezo, ndi wopunthayo achita mwa chiyembekezo cha kugawana nao.

11Aro. 15.27Ngati takufeserani inu zauzimu, kodi nchachikulu ngati ife tituta za thupi lanu?

12Mac. 20.33; 1Ako. 9.15, 18; 2Ako. 11.12Ngati ena ali nao ulamuliro umene pa inu, si ife nanga koposa? Koma sitinachita nao ulamuliro umene; koma timalola zonse, kuti tingachite chochedwetsa kwa Uthenga Wabwino wa Khristu.

13Lev. 6.16, 26Kodi simudziwa kuti iwo akutumikira za Kachisi amadya za m'Kachisi, ndi iwo akuimirira guwa la nsembe, agawana nalo guwa la nsembe?

14Agal. 6.6Chomwechonso Ambuye analamulira kuti iwo amene alalikira Uthenga Wabwino akhale ndi moyo ndi Uthenga Wabwino.

Kudzipereka kwa mtumwiyo. Makani a liwiro a mkhristu

15 Mac. 18.3; 1Ako. 9.12; 2Ako. 11.10 Koma ine sindinachita nako kanthu ka izi; ndipo sindilemba izi kuti chikakhale chotero ndi ine; pakuti kundikomera ine kufa, koma wina asayese kwachabe kudzitamanda kwanga.

16Aro. 1.14Pakuti ngati ndilalikira Uthenga Wabwino ndilibe kanthu kakudzitamandira; pakuti chondikakamiza ndigwidwa nacho; pakuti tsoka ine ngati sindilalikira Uthenga Wabwino.

171Ako. 3.8, 14; Akol. 1.25Pakuti ngati ndichita ichi chivomerere, mphotho ndili nayo; koma ngati si chivomerere, anandikhulupirira m'udindo.

181Ako. 10.33Mphotho yanga nchiyani tsono? Kuti pakulalikira Uthenga Wabwino ndiyese Uthenga Wabwino ukhale waulere, kuti ndisaipse ulamuliro wanga wa mu Uthenga Wabwino.

19Agal. 5.13Pakuti pokhala ndinali mfulu kwa onse, ndinadzilowetsa ndekha ukapolo kwa onse, kuti ndipindule ochuluka.

20Mac. 16.3; 18.18Ndipo kwa Ayuda ndinakhala monga Myuda, kuti ndipindule Ayuda; kwa iwo omvera lamulo monga womvera lamulo, ngakhale sindinakhala ndekha womvera lamulo, kuti ndipindule iwo omvera malamulo;

21Aro. 2.12, 14kwa iwo opanda lamulo monga wopanda lamulo, wosati wakukhala ine wopanda lamulo kwa Mulungu, koma womvera lamulo kwa Khristu kuti ndipindule iwo opanda lamulo.

22Aro. 11.14; 15.1Kwa ofooka ndinakhala ngati wofooka, kuti ndipindule ofooka. Ndakhala zonse kwa anthu onse, kuti paliponse ndikapulumutse ena.

23Koma ndichita zonse chifukwa cha Uthenga Wabwino, kuti ndikakhale woyanjana nao.

24Afi. 2.16Kodi simudziwa kuti iwo akuchita makani a liwiro, athamangadi onse, koma mmodzi alandira mfupo? Motero thamangani, kuti mukalandire.

25Yak. 1.12Koma yense wakuyesetsana adzikanizira zonse. Ndipo iwowa atero kuti alandire korona wakuvunda; koma ife wosavunda.

26Chifukwa chake ine ndithamanga chotero, si monga chosinkhasinkha. Ndilimbana chotero, si monga ngati kupanda mlengalenga;

27Aro. 8.13; 2Ako. 13.5-6koma ndipumpuntha thupi langa, ndipo ndiliyesa kapolo; kuti, kapena ngakhale ndalalikira kwa ena, ndingakhale wotayika ndekha.

Blog
About Us
Message
Site Map

Who We AreWhat We EelieveWhat We Do

Terms of UsePrivacy Notice

2025 by iamachristian.org,Inc All rights reserved.

Home
Gospel
Question
Blog
Help