1Ndipo ndinaona pamene Mwanawankhosa anamasula chimodzi cha zizindikiro zisanu ndi ziwiri, ndipo ndinamva chimodzi mwa zamoyo zinai, nichinena, ngati mau a bingu, Idza.
2Zek. 6.3, 11Ndipo ndinapenya, ndipo taonani, kavalo woyera, ndipo womkwerayo anali nao uta; ndipo anampatsa korona; ndipo anatulukira wolakika kuti alakike.
3Ndipo pamene anamasula chizindikiro chachiwiri, ndinamva chamoyo chachiwiri nichinena, Idza.
4Zek. 6.2Ndipo anatuluka kavalo wina, wofiira: ndipo anampatsa iye womkwera mphamvu yakuchotsa mtendere pa dziko ndi kuti aphane; ndipo anampatsa iye lupanga lalikulu.
5 Zek. 6.2 Ndipo pamene anamasula chizindikiro chachitatu, ndinamva chamoyo chachitatu nichinena, Idza. Ndipo ndinapenya, taonani, kavalo wakuda; ndipo iye womkwera anali nao muyeso m'dzanja lake.
6Chiv. 9.4Ndipo ndinamva ngati mau pakati pa zamoyo zinai, nanena, Muyeso wa tirigu wogula rupiya, ndi miyeso itatu ya barele yogula rupiya; ndi mafuta ndi vinyo usaziipse.
7Ndipo pamene anamasula chizindikiro chachinai, ndinamva mau a chamoyo chachinai nichinena, Idza.
8Ezk. 14.21; Zek. 6.3Ndipo ndinapenya, taonani, kavalo wotumbuluka; ndipo iye womkwera, dzina lake ndiye Imfa; ndipo dziko la akufa linatsatana naye; ndipo anawapatsa ulamuliro pa dera lachinai la dziko, kukapha ndi lupanga, ndi njala, ndi imfa, ndi zilombo za padziko.
9 Chiv. 20.4 Ndipo pamene adamasula chizindikiro chachisanu, ndinaona pansi pa guwa la nsembe mizimu ya iwo adaphedwa chifukwa cha mau a Mulungu, ndi chifukwa cha umboni umene anali nao:
10Zek. 1.12; Chiv. 11.18ndipo anafuula ndi mau akulu, ndi kunena, Kufikira liti, Mfumu yoyera ndi yoona, muleka kuweruza ndi kubwezera chilango chifukwa cha mwazi wathu, pa iwo akukhala padziko?
11Aheb. 11.40; Chiv. 3.4-5Ndipo anapatsa yense wa iwo mwinjiro woyera; nanena kwa iwo, kuti apumulebe kanthawi, kufikira atakwaniranso akapolo anzao, ndi abale ao amene adzaphedwa monganso iwo eni.
12 Yow. 3.15; Mat. 24.29; Chiv. 16.18 Ndipo ndinaona pamene anamasula chizindikiro chachisanu ndi chimodzi, ndipo panali chivomezi chachikulu; ndi dzuwa lidada bii longa chiguduli cha ubweya ndi mwezi wonse unakhala ngati mwazi;
13Yow. 3.15; Mat. 24.29ndi nyenyezi zam'mwamba zinagwa padziko, monga mkuyu utaya nkhuyu zake zosapsa, pogwedezeka ndi mphepo yolimba.
14Yes. 34.4; Yer. 4.24Ndipo kumwamba kudachoka monga ngati mpukutu wopindidwa; ndi mapiri onse ndi zisumbu zonse zinatunsidwa kuchoka m'malo mwao.
15Yes. 2.19Ndipo mafumu a dziko, ndi akulu, ndi akazembe, ndi achuma, ndi amphamvu, ndi akapolo onse, ndi mfulu, anabisala kumapanga, ndi matanthwe a mapiri;
16Luk. 23.30nanena kwa mapiri ndi matanthwe, Igwani pa ife, ndipo tibiseni ife kunkhope ya Iye amene akhala pa mpando wachifumu, ndi kumkwiyo wa Mwanawankhosa;
17Zef. 1.14-15chifukwa lafika tsiku lalikulu la mkwiyo wao, ndipo akhoza kuima ndani?
Who We AreWhat We EelieveWhat We Do
2025 by iamachristian.org,Inc All rights reserved.