1 AKORINTO 5 - Buku Lopatulika Bible 2014

Za chigololo mu Mpingo wa ku Korinto. Awadzudzulapo

1 Lev. 18.8 Kwamveka ndithu kuti kuli chigololo pakati pa inu, ndipo chigololo chotere chonga sichimveka mwa amitundu, kuti wina ali naye mkazi wa atate wake.

2Ndipo mukhala odzitukumula, kosati makamaka mwachita chisoni, kuti achotsedwe pakati pa inu iye amene anachita ntchito iyi.

3Akol. 2.5Pakuti inedi, thupi langa kulibe, koma mzimu wanga ulipo, ndaweruza kale, monga ngati ndilipo,

4m'dzina la Ambuye wathu Yesu, posonkhana pamodzi inu ndi mzimu wanga, ndi mphamvu ya Ambuye wathu Yesu,

51Tim. 1.20kumpereka iye wochita chotere kwa Satana, kuti lionongeke thupi, kuti mzimu upulumutsidwe m'tsiku la Ambuye Yesu.

61Ako. 15.33Kudzitamanda kwanu sikuli bwino. Kodi simudziwa kuti chotupitsa pang'ono chitupitsa mtanda wonse?

7Yes. 53.7; 1Pet. 1.19Tsukani chotupitsa chakale, kuti mukakhale mtanda watsopano, monga muli osatupa. Pakutinso Paska wathu waphedwa, ndiye Khristu;

8Mat. 16.6, 12chifukwa chake tichita phwando, si ndi chotupitsa chakale, kapena ndi chotupitsa cha dumbo, ndi kuipa mtima, koma ndi mkate wosatupa wa kuona mtima, ndi choonadi.

9 1Ako. 5.1-2 Ndinalembera inu m'kalata uja, kuti musayanjane ndi achigololo;

101Ako. 10.27si konsekonse ndi achigololo a dziko lino lapansi, kapena ndi osirira, ndi okwatula, kapena ndi opembedza mafano; pakuti nkutero mukatuluke m'dziko lapansi;

11Mat. 18.17; 2Ate. 3.6, 14koma tsopano ndalembera inu kuti musayanjane naye, ngati wina wotchedwa mbale ali wachigololo, kapena wosirira, kapena wopembedza mafano, kapena wolalatira, kapena woledzera, kapena wolanda, kungakhale kukadya naye wotere, iai.

121Ako. 6.1-4Pakuti nditani nao akunja kukaweruza iwo? Kodi amene ali m'katimo simuwaweruza ndi inu,

13Aro. 6.5, 8koma akunja awaweruza Mulungu? Chotsani woipayo pakati pa inu nokha.

Blog
About Us
Message
Site Map

Who We AreWhat We EelieveWhat We Do

Terms of UsePrivacy Notice

2025 by iamachristian.org,Inc All rights reserved.

Home
Gospel
Question
Blog
Help