1 Mas. 95.1 Fuulirani kwa Yehova, inu, dziko lonse lapansi.
2Tumikirani Yehova ndi chikondwerero:
Idzani pamaso pake ndi kumuimbira mokondwera.
3 Gen. 1.26; Mas. 95.7; Ezk. 34.30-31; Aef. 2.10 Dziwani kuti Yehova ndiye Mulungu;
Iyeyu anatilenga, ndipo ife ndife ake;
ndife anthu ake ndi nkhosa zapabusa pake.
4 Mas. 66.13 Lowani kuzipata zake ndi chiyamiko,
ndi kumabwalo ake ndi chilemekezo:
Myamikeni; lilemekezeni dzina lake.
5 Mas. 136.1-26 Pakuti Yehova ndiye wabwino;
chifundo chake chimanka muyaya;
ndi chikhulupiriko chake ku mibadwomibadwo.
Who We AreWhat We EelieveWhat We Do
2025 by iamachristian.org,Inc All rights reserved.