LEVITIKO 4 - Buku Lopatulika Bible 2014

Za nsembe yauchimo pochimwa wansembe

1Ndipo Yehova ananena ndi Mose, nati,

21Sam. 14.27; Mas. 19.12Lankhula ndi ana a Israele, ndi kuti, Munthu akachimwa, osati dala, pa china cha zinthu zilizonse aziletsa Yehova, nakachitapo kanthu;

3Aheb. 7.26-28akalakwa wansembe wodzozedwa ndi kupalamulira anthu; pamenepo azibwera nayo kwa Yehova ng'ombe yamphongo, yopanda chilema, chifukwa cha kuchimwa kwake adakuchita, ikhale nsembe yauchimo.

4Ndipo adze nayo ng'ombeyo ku khomo la chihema chokomanako pamaso pa Yehova; naike dzanja lake pamutu pa ng'ombeyo, naiphe ng'ombeyo pamaso pa Yehova.

5Num. 19.4Ndipo wansembe wodzozedwayo atengeko mwazi wa ng'ombeyo, nabwere nao ku chihema chokomanako;

6ndipo wansembeyo aviike chala chake m'mwazimo, nawaze mwaziwo kasanu ndi kawiri pamaso pa Yehova chakuno cha nsalu yotchinga, ya malo opatulika.

7Ndipo wansembeyo atengeko mwazi, nauike pa nyanga za guwa la nsembe la chofukiza cha fungo lokoma, lokhala m'chihema chokomanako pamaso pa Yehova; nathire mwazi wonse wa ng'ombeyo patsinde pa guwa la nsembe yopsereza, lokhala pa khomo la chihema chokomanako.

8Ndipo achotse mafuta onse a ng'ombe ya nsembe yauchimo, achotse mafuta akukuta matumbo, ndi mafuta onse akukhala pamatumbo,

9ndi impso ziwiri ndi mafuta ali pomwepo, okhala m'chuuno, ndi chokuta cha mphafa chofikira kuimpso,

10umo azikachotsera pa ng'ombe ya nsembe yoyamika; ndipo wansembe azitenthe pa guwa la nsembe yopsereza.

11Natulutse chikopa cha ng'ombeyo, ndi nyama yake yonse, pamodzi ndi mutu wake, ndi miyendo yake, ndi matumbo ake, ndi chipwidza chake,

12Eks. 29.14; Aheb. 13.11-12inde ng'ombe yonse, kunja kwa chigono, kunka nayo kumalo koyera, kumene atayako mapulusa, naitenthe pankhuni ndi moto; aitenthe potayira mapulusa.

Za nsembe yauchimo pochimwa mtundu wonse wa Israele

13Ndipo khamu lonse la Israele likalakwa osati dala, ndipo chikabisika chinthuchi pamaso pa msonkhano, litachita china cha zinthu zilizonse aziletsa Yehova, ndi kupalamula;

14kukadziwika kuchimwa adachimwako, pamenepo msonkhano uzibwera nayo ng'ombe yamphongo, ikhale nsembe yauchimo, ndipo udze nayo ku khomo la chihema chokomanako.

15Ndipo akulu a khamulo aike manja ao pamutu pa ng'ombeyo, pamaso pa Yehova; naiphe ng'ombeyo pamaso pa Yehova.

16Aheb. 9.12-14Ndipo wansembe wodzozedwayo adze nao mwazi wina wa ng'ombeyo ku chihema chokomanako;

17naviike chala chake m'mwazi wa nsembewo, nauwaze kasanu ndi kawiri pamaso pa Yehova, chakuno cha nsalu yotchinga.

18Naike mwazi wina pa nyanga za guwa la nsembe, lokhala pamaso pa Yehova, lokhala m'chihema chokomanako; nathire mwazi wonse patsinde pa guwa la nsembe yopsereza, lokhala pa khomo la chihema chokomanako.

19Ndipo achotse mafuta ake onse, nawatenthe pa guwa la nsembe.

20Aheb. 2.17Atero nayo ng'ombeyo; monga umo anachitira ng'ombe ya nsembe yauchimo; ndipo wansembe awachitire chowatetezera, ndipo adzakhululukidwa.

21Ndipo atulutse ng'ombeyo kunja kwa chigono, ndi kuitentha monga anatenthera ng'ombe yoyamba ija; ndiyo nsembe yauchimo ya kwa msonkhano.

Za nsembe yauchimo pochimwa mkulu

22Akachimwa mkulu, osati dala, pa china cha zinthu zilizonse aziletsa Yehova Mulungu wake, napalamula;

23akamdziwitsa kuchimwa kwake adachimwako, azidza nacho chopereka chake, ndicho tonde wopanda chilema;

24naike dzanja lake pamutu pa mbuziyo, naiphe pamalo pophera nsembe yopsereza pamaso pa Yehova; ndiyo nsembe yauchimo.

25Ndipo wansembe atengeko mwazi wa nsembe yauchimo ndi chala chake, nauike pa nyanga za guwa la nsembe yopsereza, ndi kuthira mwazi wake patsinde pa guwa la nsembe yopsereza.

26Ndipo atenthe mafuta ake onse pa guwa la nsembe, monga mafuta a nsembe yoyamika; ndipo wansembe amchitire chomtetezera, ndipo adzakhululukidwa.

Za nsembe yauchimo pochimwa munthu yekha

27Ndipo akachimwa wina wa anthu a m'dziko, osati dala, pa china cha zinthu zilizonse aziletsa Yehova, napalamula;

28akamdziwitsa kuchimwa kwake adachimwako, azidza nacho chopereka chake mbuzi yaikazi, yopanda chilema, chifukwa cha kuchimwa kwake adakuchita.

29Aike dzanja lake pamutu pa nsembe yauchimo, naiphe nsembe yauchimo pamalo pa nsembe yopsereza.

30Ndipo wansembe atengeko mwazi ndi chala chake, nauike pa nyanga za guwa la nsembe yopsereza, ndi kuthira mwazi wake wonse patsinde pa guwa la nsembe.

31Nachotse mafuta ake onse, monga umo amachotsera mafuta pa nsembe yoyamika; ndipo wansembeyo awatenthe pa guwa la nsembe akhale fungo lokoma la kwa Yehova; ndi wansembe amchitire chomtetezera, ndipo adzakhululukidwa.

32Ndipo akadza nayo nkhosa, ndiyo chopereka chake, ikhale nsembe yauchimo, azidza nayo yaikazi, yopanda chilema.

33Naike dzanja lake pa mutu wa nsembe yauchimo, ndi kuipha ikhale nsembe yauchimo pamalo pophera nsembe yopsereza.

34Ndipo wansembe atengeko mwazi wa nsembe yauchimo ndi chala chake, nauike pa nyanga za guwa la nsembe yopsereza, ndi kuthira mwazi wake wonse patsinde pa guwa la nsembe;

35nawachotse mafuta ake onse, monga umo amachotsera mafuta a nkhosa pa nsembe yoyamika; ndipo wansembeyo atenthe awa pa guwa la nsembe, monga umo amachitira nsembe zamoto za Yehova; ndipo wansembeyo amchitire chomtetezera pa kuchimwa kwake adakuchimwira, ndipo adzakhululukidwa.

Blog
About Us
Message
Site Map

Who We AreWhat We EelieveWhat We Do

Terms of UsePrivacy Notice

2025 by iamachristian.org,Inc All rights reserved.

Home
Gospel
Question
Blog
Help