1Awa ndi mau amene Mose ananena kwa Israele wonse, tsidya la Yordani m'chipululu, m'chidikha cha pandunji pa Sufu, pakati pa Parani, ndi Tofele, ndi Labani, ndi Hazeroti, ndi Dizahabu.
2Ulendo wake wochokera ku Horebu wofikira ku Kadesi-Baranea, wodzera njira ya phiri la Seiri, ndiwo wa masiku khumi ndi limodzi.
3Ndipo kunali, chaka cha makumi anai, mwezi wakhumi ndi umodzi, tsiku loyamba la mweziwo, Mose ananena ndi ana a Israele, monga mwa zonse Yehova adamlamulira awauze;
4Num. 21.24atakantha Sihoni mfumu ya Aamori, wakukhala m'Hesiboni, ndi Ogi mfumu ya Basani, wakukhala m'Asitaroti, ku Ederei.
5Tsidya lija la Yordani, m'dziko la Mowabu, Mose anayamba kufotokozera chilamulo ichi, ndi kuti,
6Num. 10.11Yehova Mulungu wathu ananena ndi ife m'Horebu, ndi kuti Yakwanira nthawi yokhala inu m'phiri muno;
7bwererani, yendani ulendo wanu ndi kumuka ku mapiri a Aamori, ndi koyandikizana nao, kuchidikha, kumapiri, ndi kunsi ndi kumwera, ndi kumphepete kwa nyanja, dziko la Akanani, ndi Lebanoni, kufikira mtsinje waukulu wa Yufurate.
8Taonani, ndakupatsani dzikoli pamaso panu, lowani landirani dziko limene Yehova analumbirira makolo anu, Abrahamu, Isaki, ndi Yakobo, kuti ili ndidzawapatsa iwo ndi mbeu zao pambuyo pao.
9Num. 11.14Ndipo muja ndinanena ndi inu, ndi kuti, Sinditha ine kukunyamulani ndekha;
10Yehova Mulungu wanu anakuchulukitsani, ndipo taonani, lero muchuluka ngati nyenyezi za kumwamba.
112Sam. 24.3Yehova Mulungu wa makolo anu, achulukitsire chiwerengero chanu chalero ndi chikwi chimodzi, nakudalitseni monga Iye ananena nanu!
121Maf. 3.8-9Ndikasenza bwanji ndekha kupsinya kwanu, ndi katundu wanu, ndi kulimbana kwanu?
13Dzifunireni amuna anzeru, ndi ozindikira bwino, ndi odziwika mwa mafuko anu, ndipo ndidzawaika akhale akulu anu.
14Pamenepo munandiyankha ndi kuti, Mau mwanenawa ndi abwino kuwachita.
15Potero ndinatenga akulu a mafuko anu, amuna anzeru, ndi odziwika, ndi kuwaika akhale akulu anu, atsogoleri a zikwi, ndi atsogoleri a mazana, ndi atsogoleri a makumi, ndi akapitao, a mafuko anu.
16Yoh. 7.24Ndipo ndinauza oweruza anu muja, ndi kuti, Mverani milandu ya pakati pa abale anu, ndi kuweruza kolungama pakati pa munthu ndi mbale wake, ndi mlendo wokhala naye.
17Miy. 24.23; Yak. 2.1, 9Musamasamalira munthu poweruza mlandu; ang'ono ndi akulu muwamvere chimodzimodzi; musamaopa nkhope ya munthu; popeza chiweruzo ncha Mulungu; ndipo mlandu ukakukanikani mubwere nao kwa ine, ndidzaumva.
18Ndipo ndinakuuzani muja zonse muyenera kuzichita.
19 Num. 10.12; 13.26 Pamenepo tinayenda ulendo kuchokera ku Horebu, ndi kubzola m'chipululu chachikulu ndi choopsa chija chonse munachionachi, pa njira ya ku mapiri a Aamori, monga Yehova Mulungu wathu anatiuza; ndipo tinadza ku Kadesi-Baranea.
20Ndipo ndinati kwa inu, Mwafikira mapiri a Aamori, amene Yehova Mulungu wathu atipatsa.
21Yos. 1.9Taonani, Yehova Mulungu wanu wapatsa dzikoli pamaso panu; kwerakoni, landirani, monga Yehova Mulungu wa makolo anu, wanena ndi inu; musamachita mantha, musamatenga nkhawa.
22Ndipo munayandikiza kwa ine inu nonse, ndi kuti, Titumize amuna atitsogolere, kuti akatizondere dziko ndi kutibwezera mau akunena za njira ya kukwera nayo ife pomka komwemo, ndi za midzi yoti tidzafikako.
23Num. 13.3Ndipo chinandikomera chinthu ichi; ndipo ndinatenga amuna khumi ndi awiri a inu, fuko limodzi mwamuna mmodzi;
24amenewa anatembenuka nakwera kumapiri nalowa ku chigwa cha Esikolo, nachizonda.
25Ndipo anatengako zipatso za dzikoli m'manja mwao, natsikira nazo kwa ife, natibwezera mau ndi kuti, Dzikoli Yehova Mulungu wathu atipatsa ndi labwino.
26Koma simunafuna kukwerako, ndipo munapikisana nao mau a Yehova Mulungu wanu.
27Num. 14Ndipo munadandaula m'mahema mwanu, ndi kuti, Popeza anatida Yehova, Iye anatitulutsa m'dziko la Ejipito, kutipereka m'manja mwa Aamori, ationonge.
28Tikwere kuti? Abale athu atimyukitsa mitima yathu, ndi kuti, Anthuwo ndiwo akulu ndi atali akuposa ife; midzi ndi yaikulu ndi ya malinga ofikira m'mwamba: tinaonakonso ana a Anaki.
29Pamenepo ndinati kwa inu, Musamaopsedwa, musamachita mantha nao.
30Neh. 4.20Yehova Mulungu wanu wakutsogolera inu, Iye adzathirira inu nkhondo, monga mwa zonse anakuchitirani m'Ejipito pamaso panu;
31Deut. 32.11-12; Yes. 63.9ndi kuchipululu, kumene munapenya kuti Yehova Mulungu wanu anakunyamulani, monga anyamula mwana wake wamwamuna, m'njira monse munayendamo, kufikira mutalowa m'malo muno.
32Koma m'chinthu ichi simunakhulupirira Yehova Mulungu wanu,
33amene anakutsogolerani m'njira, kukufunirani malo akumanga mahema anu ndi moto usiku, kukuonetserani njira yoyendamo inu, ndi mumtambo usana.
34Ndipo Yehova anamva mau a kunena kwanu, nakwiya, nalumbira, ndi kuti,
35Num. 14Palibe mmodzi wa anthu awa a mbadwo uno woipa adzaona dziko lokomalo ndinalumbira kupatsa makolo anuli.
36Koma Kalebe mwana wa Yefune, iye adzaliona; ndidzampatsa iye dziko limene anapondapo, ndi ana ake; popeza analimbika ndi kutsata Yehova.
37Num. 20.12Yehova anakwiya ndi inenso chifukwa cha inu, ndi kuti, Iwenso sudzalowamo.
38Num. 27.18-20Yoswa mwana wa Nuni, wakuima pamaso pako, iye adzalowamo; umlimbitse mtima; popeza iye adzalandiritsa Israele.
39Ndipo ana anu amene mudanena, Adzakhala ogulidwa, ndi ana anu osadziwa chabwino kapena choipa ndi pano, iwo adzalowamo, ndidzawapatsa iwo ili, adzalilandira ndi iwo.
40Koma inu, bwererani, mukani ulendo wanu kuchipululu, njira ya ku Nyanja Yofiira.
41Num. 14.40Pamenepo munayankha ndi kunena ndi ine, Tachimwira Yehova, tidzakwera ndi kuthira nkhondo monga mwa zonse Yehova Mulungu wathu atiuza. Ndipo munadzimangira munthu yense zida zake za nkhondo, nimunakonzeka kukwera kunka kumapiri.
42Koma Yehova anati kwa ine, Nena nao, Musakwerako, kapena kuthira nkhondo; popeza sindili pakati panu; angakukantheni adani anu.
43Pamene ndinanena ndi inu simunamvera; koma munatsutsana nao mau a Yehova ndi kuchita modzikuza, nimunakwera kunka kumapiri.
44Ndipo Aamori, akukhala m'mapiri muja, anatuluka kukomana ndi inu, nakupirikitsani, monga zimachita njuchi, nakukanthani m'Seiri, kufikira ku Horoma.
45Ndipo munabwerera ndi kulira pamaso pa Yehova; koma Yehova sanamvere mau anu, kapena kukutcherani khutu.
46Potero munakhala m'Kadesi masiku ambiri, monga mwa masiku munakhalako.
Who We AreWhat We EelieveWhat We Do
2025 by iamachristian.org,Inc All rights reserved.