EZEKIELE 15 - Buku Lopatulika Bible 2014

Mtengo wopanda pake

1Ndipo anandidzera mau a Yehova, akuti,

2Wobadwa ndi munthu iwe, mtengo wampesa uposeranji mtengo uliwonse wina, nthambi ya mpesa yokhalayo mwa mitengo ya kunkhalango?

3Kodi atengako mtengo kupanga nao ntchito? Atengako chichiri kodi kupachikapo chipangizo chilichonse?

4Yoh. 15.6Taona, auponya kumoto kuuyesa nkhuni, moto unyeketsa nsonga zake zonse ziwiri, nupserera pakati pake, kodi ukomera ntchito iliyonse?

5Taonani, pokhala wamphumphu sunayenera ntchito iliyonse, nanga utanyeketsa moto nupserera udzayeneranso ntchito iliyonse?

6Chifukwa chake atero Ambuye Yehova, Ngati mtengo wampesa pakati pa mitengo ya kunkhalango ndauponya kumoto ukhale nkhuni, momwemo ndidzapereka okhala m'Yerusalemu.

7Yes. 24.18Ndipo ndidzaika nkhope yanga iwatsutse; adzatuluka kumoto, mudzadziwa kuti Ine ndine Yehova, pakuika Ine nkhope yanga iwatsutse.

8Ndipo ndidzasandutsa dziko chipululu; popeza anachita cholakwa, ati Ambuye Yehova.

Blog
About Us
Message
Site Map

Who We AreWhat We EelieveWhat We Do

Terms of UsePrivacy Notice

2025 by iamachristian.org,Inc All rights reserved.

Home
Gospel
Question
Blog
Help