1 Mali. 3.55; Yon. 2.2 M'mozamamo ndinakufuulirani, Yehova.
2Ambuye, imvani liu langa;
makutu anu akhale chimverere
mau a kupemba kwanga.
3 Aro. 3.20, 23-24 Mukasunga mphulupulu, Yehova,
adzakhala chilili ndani, Ambuye?
4 Eks. 34.7; 1Maf. 8.39-40 Koma kwa Inu kuli chikhululukiro,
kuti akuopeni.
5 Yes. 8.17 Ndilindira Yehova, moyo wanga ulindira,
ndiyembekeza mau ake.
6 Mas. 63.6 Moyo wanga uyang'anira Ambuye,
koposa alonda matanda kucha;
inde koposa alonda matanda kucha.
7 Mas. 131.3; Yes. 55.7 Israele, uyembekezere Yehova;
chifukwa kwa Yehova kuli chifundo,
kwaonso kuchulukira chiombolo.
8 Mat. 1.21 Ndipo adzaombola Israele
ku mphulupulu zake zonse.
Who We AreWhat We EelieveWhat We Do
2025 by iamachristian.org,Inc All rights reserved.