LEVITIKO 18 - Buku Lopatulika Bible 2014

Malamulo a pa ulemu

1Ndipo Yehova ananena ndi Mose, nati,

2Nena ndi ana a Israele, nuti nao, Ine ndine Yehova Mulungu wanu.

3Musamachita monga mwa machitidwe a dziko la Ejipito, muja munakhalamo; musamachita monga mwa machitidwe a dziko la Kanani kumene ndipita nanuko, nimusamayenda m'malemba ao.

4Ezk. 20.19Muzichita maweruzo anga, ndi kusunga malemba anga, kumayenda m'mwemo; Ine ndine Yehova Mulungu wanu.

5Aro. 10.5; Agal. 3.12Inde, muzisunga malemba anga, ndi maweruzo anga; amenewo munthu akawachita, adzakhala nao ndi moyo; Ine ndine Yehova.

6Asasendere mmodzi wa inu kwa mbale wake kumvula; Ine ndine Yehova.

7Usamavula atate wako, ndi mai wako; ndiye mai wako, usamamvula.

8Usamavula mkazi wa atate wako; ndiye thupi la atate wako.

9Usamavula mlongo wako, mwana wamkazi wa atate wako, kapena mwana wamkazi wa mai wako, wobadwa kwanu, kapena wobadwa kwina.

10Usamavula mwana wamkazi wa mwana wamwamuna wako, kapena mwana wamkazi wa mwana wamkazi wako; pakuti thupi lao ndi lako.

11Usamavula mwana wamkazi wa mkazi wa atate wako, amene anambala atate wako, ndiye mlongo wako.

12Usamavula mlongo wa atate wako; ndiye wa chibale cha atate wako.

13Usamavula mbale wa mai wako; popeza ndiye mbale wa mai wako.

14Usamavula mbale wa atate wako; usamasendera kwa mkazi wake; ndiye mai wako.

15Usamavula mpongozi wako; ndiye mkazi wa mwana wamwamuna wako; usamamvula.

16Usamavula mkazi wa mbale wako; ndiye thupi la mbale wako.

17Usamavula mkazi ndi mwana wamkazi wake; usamatenga mwana wamkazi wa mwana wamwamuna wake, kapena mwana wamkazi wa mwana wamkazi wake kumvula; ndiwo abale; chochititsa manyazi ichi.

18Usamtenga mkazi kumuonjezera kwa mbale wake, kumvuta, kumvula pamodzi ndi mnzake, akali ndi moyo mnzakeyo.

19Usamasendera kwa mkazi kumvula pokhala ali padera chifukwa cha kudetsedwa kwake.

20Usagona naye mkazi wa mnansi wako, kudetsedwa naye limodzi.

212Maf. 17.17Ndipo usamapereka a mbumba yako kuwapitiriza kumoto chifukwa cha Moleki; usamaipsa dzina la Mulungu wako; Ine ndine Yehova.

22Usamagonana ndi mwamuna, monga amagonana ndi mkazi; chonyansa ichi.

23Ndipo usamagonana ndi nyama iliyonse, kudetsedwa nayo; kapena mkazi asamaima panyama, kugonana nayo; chisokonezo choopsa ichi.

24Musamadzidetsa nacho chimodzi cha izi; pakuti amitundu amene ndiwapirikitsa pamaso panu amadetsedwa nazo zonsezi;

25dziko lomwe lidetsedwa; chifukwa chake ndililanga, ndi dzikoli lisanza okhala m'mwemo.

26Koma inu, muzisunga malemba anga ndi maweruzo anga, osachita chimodzi chonse cha zonyansa izi; ngakhale wa m'dziko ngakhale mlendo wakugonera pakati pa inu.

27(Pakuti eni dziko okhalako, musanafike inu, anazichita zonyansa izi zonse, ndi dziko linadetsedwa)

28lingakusanzeni inunso dzikoli, polidetsa inu, monga linasanza mtundu wa anthu wokhalako musanafike inu.

29Pakuti aliyense akachita chilichonse cha zonyansa izi, inde amene azichita adzasadzidwa pakati pa anthu a mtundu wao.

30Potero muzisunga chilangizo changa, ndi kusachita zilizonse za miyambo yonyansayi anaichita musanafike inu, ndi kusadzidetsa nayo: Ine ndine Yehova Mulungu wako.

Blog
About Us
Message
Site Map

Who We AreWhat We EelieveWhat We Do

Terms of UsePrivacy Notice

2025 by iamachristian.org,Inc All rights reserved.

Home
Gospel
Question
Blog
Help