LEVITIKO 6 - Buku Lopatulika Bible 2014

Za nsembe yopalamula pochimwa dala munthu

1Ndipo Yehova ananena ndi Mose, ndi kuti,

2Miy. 24.28; Akol. 3.9Akachimwa munthu nakachita mosakhulupirika pa Yehova nakachita monyenga ndi mnansi wake kunena za choikiza, kapena chikole, kapena chifwamba, kapena anasautsa mnansi wake;

3kapena anapeza chinthu chotayika, nanenapo bodza, nalumbira pabodza; pa chimodzi cha izi zonse amachita munthu, ndi kuchimwapo;

4pamenepo padzali kuti popeza anachimwa, napalamula, azibweza zofunkha zimene analanda mwachifwamba, kapena chinthuchi adachiona ndi kusautsa mnzake, kapena choikiza anamuikiza, kapena chinthu chotayika anachipeza;

5Luk. 19.8kapena chilichonse analumbirapo monama; achibwezere chonsechi, naonjezepo, limodzi la magawo asanu; apereke ichi kwa mwini wake tsiku lotsutsidwa iye.

6Ndipo adze nayo nsembe yake yopalamula kwa Yehova, ndiyo nkhosa yamphongo yopanda chilema ya m'khola mwake, monga umayesa mtengo wake, ikhale nsembe yopalamula, adze nayo kwa wansembe;

7ndipo wansembeyo amchitire chomtetezera pamaso pa Yehova, ndipo adzakhululukidwa; kunena zilizonse akazichita ndi kupalamula nazo.

Chilamulo cha nsembe yopsereza

8Ndipo Yehova analankhula ndi Mose, nati,

9Uza Aroni ndi ana ake, ndi kuti, Chilamulo cha nsembe yopsereza ndi ichi: nsembe yopsereza izikhala pa nkhuni za pa guwa la nsembe usiku wonse kufikira m'mawa; ndipo moto wa pa guwa la nsembe uziyakabe pamenepo.

10Ndipo wansembe avale mwinjiro wake wabafuta, navale pathupi pake zovala za pamiyendo zabafuta; naole phulusa, moto utanyeketsa nsembe yamoto pa guwa la nsembe, nalitaye m'mphepete mwa guwa la nsembe.

11Pamenepo avule zovala zake, navale zovala zina, nachotse phulusa kunka nalo kunja kwa chigono, kumalo koyera.

12Ndipo moto wa pa guwa la nsembe uyakebe pamenepo, wosazima; wansembe ayatsepo nkhuni m'mawa ndi m'mawa; nakonzepo nsembe yopsereza, natenthepo mafuta a nsembe zoyamika.

13Moto uziyakabe pa guwa la nsembe, wosazima.

Chilamulo cha nsembe yaufa

14Ndipo chilamulo cha chopereka chaufa ndicho: ana a Aroni azibwera nacho pamaso pa Yehova ku guwa la nsembe.

15Ndipo atengeko wodzala manja pa ufa wa chopereka cha ufa wosalala, ndi pa mafuta ake, ndi lubani lonse lili pa chopereka chaufa, nazitenthe pa guwa la nsembe, zichite fungo lokoma, ndizo chikumbutso chake cha kwa Yehova.

16Ndipo chotsalira chake adye Aroni ndi ana ake; achidye chopanda chotupitsa m'malo opatulika; pa bwalo la chihema chokomanako achidye.

17Asachiphike ndi chotupitsa. Ndachipereka chikhale gawo lao lochokera pa nsembe zanga zamoto; ndicho chopatulika kwambiri, monga nsembe yauchimo, ndi monga nsembe yopalamula.

18Amuna onse a mwa ana a Aroni adyeko, ndilo lemba losatha la ku mibadwo yanu, chiwachokere ku nsembe zamoto za Yehova; aliyense wakuzikhudza izi adzakhala wopatulika.

Nsembe ya ansembe podzozedwa iwo

19Ndipo Yehova analankhula ndi Mose, nati,

20Chopereka cha Aroni ndi ana ake, chimene azibwera nacho kwa Yehova tsiku la kudzozedwa iye ndi ichi: limodzi la magawo khumi la efa la ufa wosalala, likhale chopereka chaufa kosalekeza, nusu lake m'mawa, nusu lake madzulo.

21Chikonzeke pachiwaya ndi mafuta; udze nacho chokazinga; chopereka chaufa chazidutsu ubwere nacho, chikhale fungo lokoma la kwa Yehova.

22Ndipo wansembe wodzozedwa m'malo mwake, wa mwa ana ake, achite ichi; likhale lemba losatha; achitenthe konse kwa Yehova.

23Ndipo zopereka zaufa zonse za wansembe azitenthe konse; asamazidya.

Chilamulo cha nsembe yauchimo

24Ndipo Yehova analankhula ndi Mose, nati,

25Lankhula ndi Aroni ndi ana ake, ndi kuti, Chilamulo cha nsembe yauchimo ndi ichi: Pamalo pophera nsembe yopsereza ndipo pophera nsembe yauchimo pamaso pa Yehova; ndiyo yopatulika kwambiri.

26Ndipo azidya iyi wansembe amene aipereka chifukwa cha zoipa; aidyere m'malo opatulika, pa bwalo la chihema chokomanako.

27Aliyense akakhudza nyama yake adzakhala wopatulika; ndipo akawaza mwazi wake wina pa chovala chilichonse, utsuke chimene adauwazacho m'malo opatulika.

28Ndipo mphika wadothi umene anaphikamo nyamayi auswe, koma ngati anaiphika mu mphika wamkuwa, atsuke uwu, nautsukuluze ndi madzi.

29Amuna onse a mwa ansembe adyeko; ndiyo yopatulika kwambiri.

30Koma asadye nsembe yauchimo iliyonse, imene amadza nao mwazi wake ku chihema chokomanako kutetezera nao m'malo opatulika; aitenthe ndi moto.

Blog
About Us
Message
Site Map

Who We AreWhat We EelieveWhat We Do

Terms of UsePrivacy Notice

2025 by iamachristian.org,Inc All rights reserved.

Home
Gospel
Question
Blog
Help