1Ndipo Yehova ananena ndi Mose ndi Aroni, nati,
2Ngati munthu ali nacho chotupa, kapena nkhanambo, kapena chikanga pa khungu la thupi lake, ndipo isandulika nthenda yakhate pa khungu la thupi lake, azifika kwa Aroni wansembe, kapena kwa mmodzi wa ana ake ansembe;
3ndipo wansembe aione nthenda pa khungu la thupi; ndipo ngati tsitsi la panthenda lasanduka la mbu, ndi nthenda ikaoneka yapitirira khungu la thupi lake, ndiyo nthenda yakhate; ndipo wansembe amuone, namutche wodetsedwa.
4Koma ngati chikanga chikhala chotuwa pa khungu la thupi lake, ndipo chikaoneka chosapitirira khungu, ndi tsitsi lake losasanduka loyera, pamenepo wansembe ambindikiritse wanthendayo masiku asanu ndi awiri;
5ndipo wansembe amuonenso tsiku lachisanu ndi chiwiri; ndipo taonani, monga momwe apenyera iye, nthenda yaima, nthenda siinapitirira pakhungu, pamenepo wansembe ambindikiritsenso masiku asanu ndi awiri ena;
6ndipo wansembe amuonenso tsiku lachisanu ndi chiwiri, ndipo taonani, nthenda yazimba yosapitirira khungu nthendayi, pamenepo wansembe amutche iye woyera, ndiyo nkhanambo chabe; ndipo atsuke zovala zake, ndiye woyera;
7koma nkhanambo ikapitirira khungu, atadzionetsa kwa wansembe kuti atchedwe woyera, adzionetsenso kwa wansembe;
8ndipo wansembe aone, ndipo taonani, ngati nkhanambo yapitirira khungu, wansembe amutche wodetsedwa, ndilo khate.
9Pamene nthenda yakhate ili mwa munthu, azimfikitsa kwa wansembe;
10ndipo wansembe aone, ndipo taonani, ngati pali chotupa choyera pakhungu, ndipo chasanduliza tsitsi likhale loyera, ndipo pachotupa pali mnofu wofiira,
11ndilo khate lakale pa khungu la thupi lake, ndipo wansembe amutche wodetsedwa; asambindikiretse popeza ali wodetsedwa.
12Ndipo ngati khate libukabuka pakhungu, ndi khate lakuta khungu lonse la wanthendayo kuyambira mutu wake kufikira mapazi ake, monga momwe apenyera wansembe;
13pamenepo wansembe aone, ndipo taonani, ngati khate lakuta thupi lake, amutche woyera wanthendayo; patuwa ponsepo; ndiye woyera.
14Koma tsiku lililonse ukaoneka pa iye mnofu wofiira, adzakhala wodetsedwa.
15Ndipo wansembe aone mnofu wofiirawo, namutche wodetsedwa; mnofu wofiira ndiwo wodetsa; ndilo khate.
16Kapena mnofu wofiira ukasandukanso, nusandulika wotuwa, afike kwa wansembe,
17ndi wansembe amuone, ndipo taonani, ngati nthenda yasandulika yotuwa, wansembe amutche woyera wanthendayo; ndiye woyera.
18Ndipo pamene thupi lili ndi chilonda pakhungu pake, ndipo chapola,
19ndipo padali chilonda pali chotupa choyera, kapena chikanga chotuuluka, pamenepo achionetse kwa wansembe; ndipo wansembe aone,
20ndipo taonani, ngati chioneka chakumba kubzola khungu, ndipo tsitsi lake lisanduka lotuwa, pamenepo wansembe amutche wodetsedwa; ndiyo nthenda yakhate yabuka m'chilondamo.
21Koma wansembe akachiona, ndipo taonani, palibe tsitsi loyera pamenepo, ndipo sichinakumba kubzola khungu, koma chazimba, pamenepo wansembe ambindikiritse masiku asanu ndi awiri;
22ndipo ngati chapitirira khungu, wansembe amutche wodetsedwa; ndilo khate.
23Koma ngati chikanga chaima pomwepo, chosakula, ndicho chipsera cha chilonda; ndipo wansembe amutche woyera.
24Kapena pamene thupi lidapsa ndi moto pakhungu pake, ndipo mnofu wofiira wakupsawo usanduka chikanga chotuuluka, kapena chotuwa;
25pamenepo wansembe achione; ndipo taonani, ngati tsitsi la chikanga lasanduka lotuwa, ndipo chioneka chakumba kubzola khungu; pamenepo ndilo khate lobuka m'kupsamo; ndipo wansembe azimutcha wodetsedwa ndi nthenda yakhate.
26Koma akaonapo wansembe, ndipo taonani, mulibe tsitsi loyera m'chikangamo, ndipo sichikumba kubzola khungu, koma chazimba; pamenepo wansembe ambindikiritse masiku asanu ndi awiri;
27ndipo wansembe amuone tsiku lachisanu ndi chiwiri; ngati chakula pakhungu, wansembe amutche wodetsedwa; ndiyo nthenda yakhate.
28Ndipo ngati chikanga chiima pomwepo, chosakula pakhungu koma chazimba; ndicho chotupa chakupsa; ndipo wansembe amutche woyera; pakuti ndicho chipsera chakupsa.
29Ndipo ngati mwamuna kapena mkazi ali ndi nthenda pamutu kapena pandevu,
30wansembe aziona nthenda; ndipo taonani, ngati ioneka yokumba kubzola khungu, ndipo pali tsitsi loyezuka lotetemera; pamenepo wansembe amutche wodetsedwa; ndiyo mfundu, ndilo khate la mutu kapena ndevu.
31Ndipo wansembe akaona nthenda yamfundu, ndipo taonani, ioneka yosakumba kubzola khungu, ndipo palibe tsitsi lakuda pamenepo, wansembe ambindikiritse iye ali ndi mfundu masiku asanu ndi awiri;
32ndipo tsiku lachisanu ndi chiwiri wansembe aone nthendayi; ndipo taonani, ngati mfundu njosakula, ndipo mulibe tsitsi loyezuka, ndipo mfundu ikaoneka yosakumba kubzola khungu,
33pamenepo azimeta, koma osameta pamfundu; ndipo wansembe ambindikiritse iye wamfundu masiku asanu ndi awiri ena;
34ndipo tsiku lachisanu ndi chiwiri aone mfunduyo; ndipo taonani, ngati mfundu njosakula pakhungu, ndipo ioneka yosakula kubzola khungu, wansembe amutche woyera, ndipo iye atsuke zovala zake, nakhala woyera.
35Koma ngati mfundu ikula pakhungu atatchedwa woyera;
36pamenepo wansembe amuone, ndipo taonani, ngati mfundu yakula pakhungu, wansembe asafunefune tsitsi loyezuka, ndiye wodetsedwa.
37Koma monga momwe apenyera iye, ngati mfundu yaima pomwe, ndipo pamera tsitsi lakuda, mfundu yapola, ndiye woyera, ndipo wansembe amutche woyera.
38Ndipo ngati mwamuna kapena mkazi ali ndi zikanga pa khungu la thupi lake, zikanga zoyerayera;
39wansembe aziona; ndipo taonani ngati zikanga zili pa khungu la thupi lao zikhala zotuwatuwa; ndilo thuza labuka pakhungu; ndiye woyera.
40Ndipo ngati tsitsi la munthu lathothoka, ndiye wadazi; koma woyera.
41Ndipo ngati tsitsi lathothoka pamphumi pake ndiye wa masweswe, koma woyera.
42Koma ngati pali nthenda yotuuluka pakati pa dazi lake la pamutu, kapena la pamphumi, ndipo khate lilikubuka pakati pa dazi lake la pamutu, kapena la pamphumi.
43Pamenepo wansembe azimuona, ndipo taonani, ngati chotupa chake cha nthenda chili chotuuluka pa dazi la pa mutu wake, kapena la pamphumi pake, monga maonekedwe a khate pa khungu la thupi;
44ndiye wakhate, ndiye wodetsedwa; wansembe amutchetu wodetsedwa; nthenda yake ili pamutu pake.
45Ndipo azing'amba zovala zake za wakhate ali ndi nthendayo, ndi tsitsi la pamutu pake lizikhala lomasuka, naphimbe iye mlomo wake wa m'mwamba, nafuule, Wodetsedwa, wodetsedwa!
46Masiku onse nthenda ikali pa iye azikhala wodetsedwa; ali wodetsedwa, agone pa yekha pokhala pake pakhale kunja kwa chigono.
47Ndiponso ngati nthenda yakhate ili pa chovala chaubweya, kapena chathonje;
48ngakhale ili pamuyaro, kapena pamtsendero, chathonje, kapena chaubweya, ngakhale ili pa chikopa, kapena pa chinthu chilichonse chopanga ndi chikopa;
49ngati nthenda ili yobiriwira, kapena yofiira pachovala, kapena pachikopa, kapena pamuyaro, kapena pamtsendero, kapena pa chinthu chilichonse chopangika ndi chikopa, ndiyo nthenda yakhate; aziionetsa kwa wansembe;
50ndipo wansembe aone nthendayo, nabindikiritse chija cha nthenda masiku asanu ndi awiri;
51naone nthenda tsiku lachisanu ndi chiwiri; ngati nthenda yakula pachovala, ngakhale pamuyaro, kapena pamtsendero, kapena pachikopa, zilizonse zantchito zopangika ndi chikopa; nthendayo ndiyo khate lofukuta; ndicho chodetsedwa.
52Ndipo atenthe chovalacho ngakhale muyaro wake, ngakhale mtsendero wake, chaubweya kapena chathonje, kapena chilichonse chachikopa chili ndi khate, ndilo khate lofetsa; achitenthe ndi moto.
53Ndipo wansembe akaona, ndipo taonani, nthenda njosakula pachovala, kapena pamuyaro, kapena pamtsendero, kapena pa chinthu chilichonse chopangika ndi chikopa;
54pamenepo wansembe aziuza kuti atsuke chija pali khate, nachibindikiritse masiku asanu ndi awiri ena;
55ndipo wansembe aone nthenda ataitsuka, ndipo taonani, ngati nthendayi siinasandulika maonekedwe ake, yosakulanso nthenda, ndicho chodetsedwa; uchitenthe ndi moto; ndilo funka, kungakhale kuyera kwake kuli patsogolo kapena kumbuyo.
56Ndipo wansembe akaona, ndipo taonani, nthenda yazimba ataitsuka, pamenepo aikadzule pa chovala, kapena chikopa, kapena muyaro, kapena mtsendero;
57ndipo ikaonekabe pachovala, ngakhale pamuyaro, kapena pamtsendero, kapena pa chinthu chilichonse chopangika ndi chikopa, ilikubukanso; uchitenthe ndi moto chija chanthenda.
58Ndipo ukatsuka chovalacho, kapena muyaro, kapena mtsendero, kapena chinthu chilichonse chopangika ndi chikopa, ngati nthenda yalekapo pa chimenecho, achitsukenso kawiri, pamenepo chili choyera.
59Ichi ndi chilamulo cha nthenda yakhate ili pa chovala chaubweya kapena chathonje, ngakhale pamuyaro, kapena pamtsendero, kapena pa chinthu chilichonse chopangika ndi chikopa; kuchitcha choyera kapena kuchitcha chodetsa.
Who We AreWhat We EelieveWhat We Do
2025 by iamachristian.org,Inc All rights reserved.