1 2Maf. 20.1-11 Masiku amenewo Hezekiya anadwala, nafuna kufa. Ndipo Yesaya mneneri, mwana wa Amozi, anadza kwa iye, nati kwa iye, Atero Yehova, Konza nyumba yako, pakuti iwe udzafa, sudzakhala ndi moyo.
2Ndipo Hezekiya analoza nkhope yake kukhoma, napemphera kwa Yehova, nati,
3Kumbukiranitu tsopano, Yehova, kuti ndayenda pamaso panu m'zoonadi ndi mtima wangwiro, ndipo ndachita zabwino pamaso panu. Ndipo Hezekiya analira kolimba.
4Ndipo anafika mau a Yehova kwa Yesaya, ndi kuti,
5Ukanene kwa Hezekiya, Atero Yehova, Mulungu wa Davide, kholo lako, Ndamva kupemphera kwako, ndaona misozi yako; taona, ndidzaonjezera pa masiku ako zaka khumi ndi zisanu.
6Yes. 37.25Ndipo ndidzakupulumutsa iwe ndi mudzi uno m'manja mwa mfumu ya Asiriya, ndipo ndidzatchinjiriza mudzi uno.
7Ndipo ichi chidzakhala chizindikiro kwa iwe chochokera kwa Yehova, kuti Yehova adzachita ichi wanenachi;
8taona, ndidzabweza mthunzi wa pamakwerero, umene watsika pa makwerero a Ahazi ndi dzuwa, ubwerere makwerero khumi. Ndipo dzuwa linabwerera makwerero khumi pamakwerero, pamene udatsika mthunziwo.
9Malemba a Hezekiya mfumu ya Ayuda muja anadwala, atachira nthenda yake.
10Ine ndinati, Pakati pa masiku anga ndidzalowa m'zipata za kunsi kwa manda; Ndazimidwa zaka zanga zotsala.
11Ndinati, Sindidzaona Yehova m'dziko la amoyo; sindidzaonanso munthu pamodzi ndi okhala kunja kuno;
12Pokhala panga pachotsedwa, pandisunthikira monga hema wa mbusa; Ndapindapinda moyo wanga ngati muomba; Iye adzandidula ine poomberapo; Kuyambira usana kufikira usiku mudzanditsiriza ine.
13Ndinadzitonthoza kufikira mamawa; monga mkango, momwemo Iye anathyolathyola mafupa anga onse; Kuyambira usana kufikira usiku mudzanditsiriza ine.
14Yes. 59.11Ndinalankhulalankhula ngati namzeze, pena chumba; Ndinalira maliro ngati nkhunda; maso anga analephera pogadamira kumwamba. Yehova ndasautsidwa, mundiperekere chikoli.
151Maf. 21.27Kodi ndidzanena chiyani? Iye wanena kwa ine, ndiponso Iye mwini wachita ichi; Ine ndidzayenda chete zaka zanga zonse, chifukwa cha zowawa za moyo wanga.
16Ambuye ndi zinthu izi anthu akhala ndi moyo. Ndipo m'menemo monse muli moyo wa mzimu wanga; Chifukwa chake mundichiritse ine, ndi kundikhalitsa ndi moyo.
17Taonani, ndinali ndi zowawa zazikulu, chifukwa cha mtendere wanga; Koma Inu mokonda moyo wanga, munaupulumutsa m'dzanja la chivundi, Pakuti mwaponya m'mbuyo mwanu machimo anga onse.
18Mas. 6.5Pakuti kunsi kwa manda sikungakuyamikeni Inu; imfa singakulemekezeni; Otsikira kudzenje sangaziyembekeze zoona zanu.
19Deut. 4.6Wamoyo, wamoyo, iye adzakuyamikani inu, monga ine lero; Atate adzadziwitsa ana ake zoona zanu.
20Yehova ndiye wondipulumutsa ine; Chifukwa chake tidzaimba nyimbo zanga, ndi zoimba zazingwe Masiku onse a moyo wathu m'nyumba ya Yehova.
21Ndipo Yesaya adati, Atenge m'bulu wankhuyu, auike pafundo, ndipo iye adzachira.
22Hezekiya anatinso, Chizindikiro nchiyani, kuti ndidzakwera kunka kunyumba ya Yehova?
Who We AreWhat We EelieveWhat We Do
2025 by iamachristian.org,Inc All rights reserved.