MASALIMO 21 - Buku Lopatulika Bible 2014

Davide ayamika Mulungu pa kugonjetsa adaniKwa Mkulu wa Nyimbo. Salimo la Davide.

1 Mas. 20.5-6; 119.133; Aro. 6.12, 14 Yehova, adzasekera mfumu mu mphamvu yanu;

adzakondwera kwakukulu m'chipulumutso chanu!

2 Mas. 120.4-5 Mwampatsa iye chikhumbo cha mtima wake,

ndipo simunakana pempho la milomo yake.

3Pakuti mufika kwa iye ndi madalitso okoma;

muika korona wa golide woyengetsa pamutu pake.

4 Mas. 61.5-6; 2Sam. 7.19 Anakupemphani moyo, mwampatsa iye;

mwamtalikitsira masiku kunthawi za nthawi.

5Ulemerero wake ngwaukulu mwa chipulumutso chanu;

mumchitira iye ulemu ndi ukulu.

6 Mac. 2.28 Pakuti mumuikira madalitso kunthawi zonse;

mumkondweretsa ndi chimwemwe pankhope panu.

7Pakuti mfumu akhulupirira Yehova,

ndipo mwa chifundo cha Wam'mwambamwamba sadzagwedezeka iye.

8Dzanja lanu lidzapeza adani anu onse,

dzanja lanu lamanja lidzapeza iwo akuda Inu.

9Mudzawaika ngati ng'anjo yamoto pa nyengo ya mkwiyo wanu.

Yehova adzawatha m'kukwiya kwake,

ndipo moto udzawanyeketsa.

10 Yob. 18.16-17, 19; Yes. 14.20 Mudzaziononga zobala zao kuzichotsa pa dziko lapansi,

ndi mbeu zao mwa ana a anthu.

11Pakuti anakupangirani choipa,

anapangana chiwembu, osakhoza kuchichita.

12Pakuti mudzawabweza m'mbuyo,

popiringidza m'nsinga zanu pankhope pao.

13Kwezekani, Yehova, mu mphamvu yanu;

potero tidzaimba ndi kulemekeza chilimbiko chanu.

Blog
About Us
Message
Site Map

Who We AreWhat We EelieveWhat We Do

Terms of UsePrivacy Notice

2025 by iamachristian.org,Inc All rights reserved.

Home
Gospel
Question
Blog
Help