YOBU 12 - Buku Lopatulika Bible 2014

Yobu avomerezanso ukulu wa Mulungu, koma mau a abwenziwo ndi opanda pake; nanena za moyo wa munthu ukutha msanga

1Pamenepo Yobu anayankha, nati,

2Zoonadi inu ndinu anthu,

ndi nzeru idzafa pamodzi ndi inu.

3Koma inenso ndili nayo nzeru monga inu.

Sindingakuchepereni;

ndani sadziwa zonga izi?

4 Mas. 91.15 Ndine ngati munthu wosekedwa ndi mnansi wake,

ndinaitana kwa Mulungu, ndipo anandiyankha;

munthu wolungama wangwiro asekedwa.

5Munthu wosatekeseka apeputsa tsoka mumtima mwake,

limlindira woterereka mapazi ake.

6 Mas. 37.35; Yer. 12.1 Mahema a achifwamba akhala mumtendere,

ndi iwo oputa Mulungu alimbika mtima;

amene Mulungu amadzazira dzanja lao.

7Tafunsira tsono kwa nyamazo, zidzakulangiza,

ndi mbalame za m'mlengalenga, zidzakuuza.

8Kapena ulankhule ndi dziko lapansi, lidzakulangiza;

ndi nsomba za kunyanja, zidzakufotokozera.

9Ndaniyo sadziwa nazo izi zonse;

kuti dzanja la Yehova lichita ichi?

10 Num. 16.22; Mac. 17.28 M'dzanja mwake muli mpweya wa zamoyo zonse,

ndi mzimu wa munthu aliyense.

11M'khutumu simuyesa mau,

monga m'kamwa mulawa chakudya chake?

12Kwa okalamba kuli nzeru,

ndi kwa a masiku ochuluka luntha.

13Kwa Iye kuli nzeru ndi mphamvu;

uphungu ndi luntha ali nazo.

14 Yes. 22.22; Chiv. 3.7 Taona, agamula, ndipo palibe kumanganso;

amtsekera munthu, ndipo palibe kumtsegulira.

15 1Maf. 17.1 Taona atsekera madzi, naphwa;

awatsegulira, ndipo akokolola dziko lapansi.

16Kwa Iye kuli mphamvu ndi nzeru.

Wonyengedwa ndi wonyenga yemwe ali ake.

17 2Sam. 15.31 Apita nao maphungu atawafunkhira,

napulukiritsa oweruza milandu.

18Amasula chomangira cha mafumu,

nawamangira nsinga m'chuuno mwao.

19Apita nao, ansembe atawafunkhira,

nagubuduza amphamvu.

20Amchotsera wokhulupirika kunena kwake.

Nalanda luntha la akulu.

21 Mas. 107.40; Dan. 2.21-22 Atsanulira mnyozo pa akalonga,

nawansezera olimba lamba lao.

22Avumbulutsa zozama mumdima,

natulutsa mthunzi wa imfa ukhale poyera;

23 Yes. 9.3 achulukitsa amitundu, nawaononganso;

abalalikitsa amitundu, nawabwezanso.

24 Mas. 107.4, 27, 40 Awachotsera akulu a anthu a padziko mtima wao,

nawasokeretsa m'chipululu chopanda njira.

25Iwo ayambasa mumdima mopanda kuunika,

ndipo awayendetsa dzandidzandi.

Blog
About Us
Message
Site Map

Who We AreWhat We EelieveWhat We Do

Terms of UsePrivacy Notice

2025 by iamachristian.org,Inc All rights reserved.

Home
Gospel
Question
Blog
Help