AEFESO 1 - Buku Lopatulika Bible 2014

1 2Ako. 1.1 Paulo, mtumwi wa Khristu Yesu, mwa chifuniro cha Mulungu, kwa oyera mtima amene ali m'Efeso, ndi kwa iwo okhulupirika mwa Khristu Yesu:

2Chisomo kwa inu, ndi mtendere wochokera kwa Mulungu Atate wathu, ndi Ambuye Yesu Khristu.

Madalitso a Mulungu mwa Yesu Khristu, Mpulumutsi wathu ndi mutu wa Mpingo

3 1Pet. 1.3 Wolemekezeka Mulungu ndi Atate wa Ambuye wathu Yesu Khristu, amene anatidalitsa ife ndi dalitso lonse la mzimu m'zakumwamba mwa Khristu;

4Aro. 8.28; Akol. 1.22; 1Pet. 1.2, 20monga anatisankha ife mwa Iye, lisanakhazikike dziko lapansi, tikhale ife oyera mtima, ndi opanda chilema pamaso pake m'chikondi.

5Aro. 8.29-30; Agal. 4.5Anatikonzeratu tilandiridwe ngati ana a Iye yekha mwa Yesu Khristu, monga umo kunakomera chifuniro chake,

6Aro. 3.24kuti uyamikidwe ulemerero wa chisomo chake, chimene anatichitira ife kwaufulu mwa Wokondedwayo.

7Aro. 2.4; Akol. 1.14Tili ndi maomboledwe mwa mwazi wake, chikhululukiro cha zochimwa, monga mwa kulemera kwa chisomo chake,

8chimene anatichulukitsira ife m'nzeru zonse, ndi chisamaliro.

9Akol. 1.26Anatizindikiritsa ife chinsinsi cha chifuniro chake, monga kunamkomera ndi monga anatsimikiza mtima kale mwa Iye,

10Agal. 4.4; Aef. 2.15; Afi. 2.9-10kuti pa makonzedwe a makwaniridwe a nyengozo, akasonkhanitse pamodzi zonse mwa Khristu, za kumwamba, ndi za padziko.

11Mac. 20.32; Aef. 1.5Mwa Iye tinayesedwa cholowa chake, popeza tinakonzekeratu monga mwa chitsimikizo mtima cha Iye wakuchita zonse monga mwa uphungu wa chifuniro chake;

12Aef. 1.6, 14kuti ife amene tinakhulupirira Khristu kale tikayamikitse ulemerero wake.

13Yoh. 1.17; Aef. 4.30Mwa Iyeyo inunso, mutamva mau a choonadi, Uthenga Wabwino wa chipulumutso chanu, ndi kumkhulupirira Iye, munasindikizidwa chizindikiro ndi Mzimu Woyera wa lonjezano,

14Mac. 20.28; 2Ako. 5.5ndiye chikole cha cholowa chathu, kuti akeake akaomboledwe, ndi kuti ulemerero wake uyamikike.

15Mwa ichi inenso, m'mene ndamva za chikhulupiriro cha mwa Ambuye Yesu chili mwa inu ndi chikondi chanu, chimenenso mufikitsira oyera mtima onse,

16Afi. 1.3-4sindileka kuyamika chifukwa cha inu, ndi kukumbukira inu m'mapemphero anga;

17Akol. 1.9kuti Mulungu wa Ambuye wathu Yesu Khristu, Atate wa ulemerero, akupatseni inu mzimu wa nzeru, ndi wa vumbulutso kuti mukamzindikire Iye;

18Aef. 1.11; 2.12ndiko kunena kuti maso a mitima yanu awalitsike, kuti mukadziwe inu chiyembekezo cha kuitana kwake nchiyani; chiyaninso chuma cha ulemerero wa cholowa chake mwa oyera mtima,

19Aef. 3.7ndi chiyani ukulu woposa wa mphamvu yake ya kwa ife okhulupirira, monga mwa machitidwe a mphamvu yake yolimba,

20Mac. 2.24; 7.55-56imene anachititsa mwa Khristu, m'mene anamuukitsa kwa akufa, namkhazikitsa pa dzanja lake lamanja m'zakumwamba,

21Afi. 2.9-10pamwamba pa ukulu wonse, ndi ulamuliro, ndi mphamvu, ndi ufumu, ndi dzina lililonse lotchedwa, si m'nyengo yino ya pansi pano yokha, komanso mwa iyo ikudza;

22Mas. 8.6; Akol. 1.18ndipo anakonza zonse pansi pa mapazi ake, nampatsa Iye akhale mutu pamtu pa zonse, kwa Mpingo

23Akol. 1.18; 2.14, 20amene ali thupi lake, mdzazidwe wa Iye amene adzaza zonse m'zonse.

Blog
About Us
Message
Site Map

Who We AreWhat We EelieveWhat We Do

Terms of UsePrivacy Notice

2025 by iamachristian.org,Inc All rights reserved.

Home
Gospel
Question
Blog
Help