1Ndipo Yehosafati mfumu ya Yuda anabwerera kunyumba yake ku Yerusalemu mumtendere.
2Mas. 139.21Natuluka Yehu mwana wa Hanani mlauli kukomana naye, nati kwa mfumu Yehosafati, Muyenera kodi kuthandiza zoipa, ndi kukonda amene adana ndi Yehova? Chifukwa cha ichi ukugwerani mkwiyo wochokera kwa Yehova.
3Koma zapezeka zokoma mwa inu, popeza mwazichotsa zifanizo m'dzikomo, mwalunjikitsanso mtima wanu kufuna Mulungu.
4Ndipo Yehosafati anakhala ku Yerusalemu, natulukiranso mwa anthu kuyambira ku Beereseba kufikira ku mapiri a Efuremu; nawabweza atsatenso Yehova Mulungu wa makolo ao.
5Naika oweruza m'dziko, m'midzi yonse yamalinga ya m'Yuda, mudzi ndi mudzi;
6Deut. 1.17nati kwa oweruza, Khalani maso umo muchitira; pakuti simuweruzira anthu koma Yehova; ndipo ali nanu Iyeyu pakuweruza mlandu.
7Deut. 10.17; Mac. 10.34; Aro. 2.11; 9.14; Agal. 2.6Ndipo tsono, kuopa Yehova kukhale pa inu, musamalire ndi kuchita; pakuti palibe chosalungama kwa Yehova Mulungu wathu, kapena kusamalira monga mwa nkhope ya munthu, kapena kulandira mphatso.
8Yehosafati anaikanso m'Yerusalemu Alevi, ndi ansembe ena, ndi akulu a nyumba za makolo m'Israele, aweruzire Yehova, nanena milandu. Ndipo anabwerera kudza ku Yerusalemu.
9Ndipo anawalangiza, ndi kuti, Muzitero ndi kuopa Yehova mokhulupirika ndi mtima wangwiro.
10Deut. 17.8-9Ndipo ukakudzerani mlandu uliwonse wochokera kwa abale anu okhala m'midzi mwao, kusiyanitsa pakati pa mwazi ndi mwazi, pakati pa chilamulo ndi chiuzo, malemba ndi maweruzo, muwachenjeze kuti asapalamule kwa Yehova, angafikitsire inu nokha ndi abale anu mkwiyo; muzitero, ndipo simudzapalamula.
111Mbi. 26.30; 2Mbi. 15.2Ndipo taonani, Amariya wansembe wamkulu, ndiye mkulu wanu m'milandu yonse ya Yehova; ndi Zebadiya mwana wa Ismaele, wolamulira nyumba ya Yuda, m'milandu yonse ya mfumu; ndi Alevi akhale akapitao pamaso panu. Chitani molimbika mtima, ndipo Yehova akhale ndi abwino.
Who We AreWhat We EelieveWhat We Do
2025 by iamachristian.org,Inc All rights reserved.