1Ndipo mkulu wa ansembe anati, Zitero izi kodi?
2Ndipo Stefano anati, Amuna inu, abale, ndi atate, tamverani. Mulungu wa ulemerero anaonekera kwa kholo lathu Abrahamu, pokhala iye m'Mesopotamiya, asanayambe kukhala m'Harani;
3
ndi nyenyezi ya mulungu Refani,
zithunzizo mudazipanga kuzilambira;
ndipo ndidzakutengani kunka nanu m'tsogolo mwake mwa Babiloni.
44 Eks. 25.40 Chihema cha umboni chinali ndi makolo athu m'chipululu, monga adalamula Iye wakulankhula ndi Mose, achipange ichi monga mwa chithunzicho adachiona.
45Yos. 3.10, 14; 23.9Chimenenso makolo athu akudza m'mbuyo, analowa nacho ndi Yoswa polandira iwo zao za amitundu, amene Mulungu anawaingitsa pamaso pa makolo athu, kufikira masiku a Davide;
46amene anapeza chisomo pamaso pa Mulungu, napempha kuti apeze mokhalamo Mulungu wa Yakobo.
471Maf. 8.16-19Koma Solomoni anammangira nyumba.
481Maf. 8.27Komatu Wamwambamwambayo sakhala m'nyumba zomangidwa ndi manja; monga mneneri anena,
49 Yes. 66.1-2 Thambo la kumwamba ndilo mpando wachifumu wanga,
ndi dziko lapansi chopondapo mapazi anga.
Mudzandimangira nyumba yotani, ati Ambuye,
kapena malo a mpumulo wanga ndi otani?
50Silinapanga dzanja langa zinthu izi zonse kodi?
51 Yes. 48.4 Ouma khosi ndi osadulidwa mtima ndi makutu inu, mukaniza Mzimu Woyera nthawi zonse; monga anachita makolo anu, momwemo inu.
522Mbi. 36.16; Mat. 21.35Ndiye yani wa aneneri makolo anu sanamzunza? Ndipo anawapha iwo amene anaonetseratu za kudza kwake kwa Wolungamayo; wa Iye amene mwakhala tsopano akumpereka ndi akumupha;
53Eks. 19.3, 17; Agal. 3.19inu amene munalandira chilamulo monga chidaikidwa ndi angelo, ndipo simunachisunga.
54Koma pakumva izi analaswa mtima, namkukutira mano.
55Mac. 6.5Koma iye, pokhala wodzala ndi Mzimu Woyera, anapenyetsetsa Kumwamba, naona ulemerero wa Mulungu, ndi Yesu alikuimirira pa dzanja lamanja la Mulungu,
56Ezk. 1.1; Mat. 3.16; Mac. 10.11nati, Taonani, ndipenya m'Mwamba motseguka, ndi Mwana wa Munthu alikuimirira pa dzanja lamanja la Mulungu.
57Koma anafuula ndi mau akulu, natseka m'makutu mwao, namgumukira iye ndi mtima umodzi;
58Lev. 24.16; Mac. 22.20ndipo anamtaya kunja kwa mudzi, namponya miyala; ndipo mbonizo zinaika zovala zao pa mapazi a mnyamata dzina lake Saulo.
59Luk. 23.34Ndipo anamponya miyala Stefano, alikuitana Ambuye, ndi kunena, Ambuye Yesu, landirani mzimu wanga.
60Luk. 23.34Ndipo m'mene anagwada pansi, anafuula ndi mau akulu, Ambuye, musawaikire iwo tchimo ili. Ndipo m'mene adanena ichi, anagona tulo.
Who We AreWhat We EelieveWhat We Do
2025 by iamachristian.org,Inc All rights reserved.