NUMERI Mau Oyamba - Buku Lopatulika Bible 2014
Mau OyambaBuku la Numeri likukamba za moyo wa ana a Israele pa zaka pafupi makumi anai, kuyambira pamene anachoka ku phiri la Sinai mpaka pamene anafika pafupi ndi Kanani chakum'mawa. Bukuli likutchedwa Numeri, kutanthauza “Kuwerengera”, chifukwa Mose adachita kalembera wa ana a Israele, asanachoke ku phiri la Sinai, nachitanso kalembera wina ku dziko la Mowabu pafupi ndi Yordani, patapita zaka ngati makumi anai.Bukuli likuonetsa kuti Aisraele anali anthu amantha ndi otaya mtima msanga akakumana ndi zovuta, ndipo kawirikawiri adapandukira Mulungu naukiranso Mose amene Mulunguyo anamusankha kuti aziwatsogolera. Bukuli liwonetseranso kuleza mtima kwa Yehova ndi chifundo chake chosasinthika posamala anthu ake, ngakhale iwowo ankachirachimwira. Moseyo anali munthu woleza mtima, adakhala wokhulupirika kwa Mulungu ndi kwa anthu ake, nasenza udindo wake wofatsa ndi molimba mtima.Za mkatimuAisraele asanachoke ku phiri la Sinai 1.1—9.23a. Kalembera woyamba 1.1—4.9 b. Malangizo ndi malamulo osiyanasiyana 5.1—8.26 c. Paska wachiwiri 9.1-23Ulendo wao kuchokera ku Sinai mpaka ku Mowabu 10.1—32.42a. Afika ku malire a dziko la Kanani nakhala ku Kadesi 10.1—20.21b. Atachoka ku Kadesi afika ku Mowabu 20.22—21.35c. Zochitika zina ndi zina ku dziko la Mowabu 22.1—32.42 Mbiri mwachidule ya ulendo wao kuchokera ku Ejipito mpaka ku Mowabu 33.1-49Awapatsa malangizo asanaoloke Yordani 33.50—36.13