1 Mas. 25.20 Ndisungeni ine, Mulungu: pakuti ndakhulupirira Inu.
2Ndinati kwa Yehova, Inu ndinu Ambuye wanga,
ndilibe chabwino china choposa Inu.
3Za oyera mtima okhala pa dziko lapansi,
iwo ndiwo omveka mbiri,
mwa iwowo muli chikondwero changa chonse.
4Zidzachuluka zisoni zao za iwo otsata Mulungu wina.
Sindidzathira nsembe zao zamwazi,
ndipo sindidzatchula maina ao pakamwa panga.
5 Mas. 73.26; Mali. 3.24 Yehova ndiye gawo la cholowa changa ndi chikho changa,
ndinu wondigwirira cholandira changa.
6Zingwe zandigwera mondikondweretsa;
inde chosiyira chokoma ndili nacho.
7 2Sam. 5.18-19 Ndidzadalitsa Yehova, amene anandichitira uphungu,
usikunso impso zanga zindilangiza.
8 Mac. 2.25-28 Ndaika Yehova patsogolo panga nthawi zonse;
popeza ali pa dzanja langa lamanja, sindidzagwedezeka.
9Chifukwa chake wasekera mtima wanga,
nukondwera ulemu wanga;
mnofu wanganso udzakhala mokhazikika.
10Pakuti simudzasiya moyo wanga kumanda;
simudzalola wokondedwa wanu avunde.
11 Mat. 5.8; 7.14; 1Ako. 13.12 Mudzandidziwitsa njira ya moyo,
pankhope panu pali chimwemwe chokwanira;
m'dzanja lanu lamanja muli zokondweretsa zomka muyaya.
Who We AreWhat We EelieveWhat We Do
2025 by iamachristian.org,Inc All rights reserved.