1Ndidzakukwezani, Yehova; pakuti mwandinyamutsa,
ndipo simunandikondwetsera adani anga.
2 Mas. 103.3 Yehova, Mulungu wanga,
ndinafuulira kwa Inu, ndipo munandichiritsa.
3Yehova munabweza moyo wanga kumanda,
munandisunga ndi moyo, kuti ndingatsikire kudzenje.
4 1Mbi. 16.4-5 Imbirani Yehova, inu okondedwa ake,
ndipo yamikani pokumbukira chiyero chake.
5 Yes. 54.7-8; 2Ako. 4.17 Pakuti mkwiyo wake ukhala kanthawi kokha;
koma kuyanja kwake moyo wonse.
Kulira kuchezera,
koma mamawa kuli kufuula kokondwera.
6Ndipo ine, ndinanena m'phindu langa,
sindidzagwedezeka nthawi zonse.
7 Mas. 104.29 Inu, Yehova, munakhazikitsa phiri langa ndi kuyanja kwanu;
munabisa nkhope yanu; ndinaopa.
8Ndinafuulira kwa Inu, Yehova;
kwa Yehova ndinapemba,
9 Mas. 88.11; Yes. 38.18 M'mwazi mwanga muli phindu lanji,
potsikira ine kudzenje?
Ngati fumbi lidzayamika Inu?
Ngati lidzalalikira choonadi chanu?
10Mverani, Yehova, ndipo ndichitireni chifundo,
Yehova, mundithandize ndi Inu.
11 Yes. 61.3 Munasanduliza kulira kwanga kukhale kusekera;
munandivula chiguduli changa, ndipo munandiveka chikondwero,
12kuti ulemu wanga uimbire Inu, wosakhala chete.
Yehova Mulungu wanga, ndidzakuyamikani nthawi zonse.
Who We AreWhat We EelieveWhat We Do
2025 by iamachristian.org,Inc All rights reserved.