MASALIMO 97 - Buku Lopatulika Bible 2014

Ulemerero wa ufumu wa Mulungu

1 Mas. 96.10 Yehova achita ufumu; dziko lapansi likondwere;

zisumbu zambiri zikondwerere.

2 1Maf. 8.12; Mas. 89.14 Pomzinga pali mitambo ndi mdima;

chilungamo ndi chiweruzo ndizo zolimbitsa

mpando wachifumu wake.

3 Luk. 1.5, 55, 72 Moto umtsogolera,

nupsereza otsutsana naye pozungulirapo.

4Mphezi zake zinaunikira dziko lokhalamo anthu;

dziko lapansi linaona nilinagwedezeka.

5 Nah. 1.5 Mapiri anasungunuka ngati sera pamaso pa Yehova,

pamaso pa Ambuye wa dziko lonse lapansi.

6 Mas. 19.1 Kumwamba kulalikira chilungamo chake,

ndipo mitundu yonse ya anthu ipenya ulemerero wake.

7 Yes. 42.17 Onse akutumikira fano losema,

akudzitamandira nao mafano, achite manyazi:

Mgwadireni Iye, milungu yonse inu.

8 Ziyoni anamva nakondwera,

nasekerera ana akazi a Yuda;

chifukwa cha maweruzo anu, Yehova.

9 Eks. 18.11 Pakuti Inu, Yehova, ndinu Wam'mwambamwamba pa dziko lonse lapansi,

ndinu wokwezeka kwakukulu pamwamba pa milungu yonse ina.

10 Mas. 37.28; Amo. 5.15 Inu okonda Yehova, danani nacho choipa:

Iye asunga moyo wa okondedwa ake;

awalanditsa m'manja mwa oipa.

11 Miy. 4.18 Kuunika kufesekera wolungama,

ndi chikondwerero oongoka mtima.

12 Mas. 30.4; 32.11 Kondwerani mwa Yehova, olungama inu;

ndipo yamikani pokumbukira chiyero chake.

Blog
About Us
Message
Site Map

Who We AreWhat We EelieveWhat We Do

Terms of UsePrivacy Notice

2025 by iamachristian.org,Inc All rights reserved.

Home
Gospel
Question
Blog
Help