CHIVUMBULUTSO 18 - Buku Lopatulika Bible 2014

Kupasula kwa Babiloni. Maliro pa dziko lapansi

1 Ezk. 43.2 Zitatha izi ndinaona mngelo wina wakutsika m'Mwamba wakukhala nao ulamuliro waukulu; ndipo dziko linaunikidwa ndi ulemerero wake.

2Yes. 13.19; Chiv. 14.8Ndipo anafuula ndi mau olimba, nanena, Wagwa, wagwa, Babiloni waukulu, nusandulika mokhalamo ziwanda, ndi mosungiramo mizimu yonse yonyansa, ndi mosungiramo mbalame zonse zonyansa ndi zodanidwa.

3Yes. 13.19; Chiv. 14.8Chifukwa ndi vinyo wa mkwiyo wa chigololo chake mitundu yonse idagwa; ndipo mafumu a dziko anachita naye chigololo; ndipo ochita malonda a dziko analemera ndi mphamvu ya kudyerera kwake.

4 Yes. 48.20; 2Ako. 6.17 Ndipo ndinamva mau ena ochokera Kumwamba, nanena, Tulukani m'menemo, anthu anga; kuti mungayanjane ndi machimo ake, ndi kuti mungalandireko ya miliri yake;

5Gen. 18.20-21pakuti machimo ake anaunjikizana kufikira m'Mwamba, ndipo Mulungu anakumbuka zosalungama zake.

6Yon. 1.2; Mas. 137.8Muubwezere, monganso uwu unabwezera, ndipo muwirikize kawiri, monga mwa ntchito zake; m'chikhomo unathiramo, muuthirire chowirikiza.

7Ezk. 28.2-8Monga momwe unadzichitira ulemu, nudyerera, momwemo muuchitire chouzunza ndi chouliritsa maliro: pakuti unena mumtima mwake, Ndikhala ine mfumu, wosati wamasiye ine, wosaona maliro konse ine.

8Yes. 47.8-9; Yer. 50.34Chifukwa chake miliri yake idzadza m'tsiku limodzi, imfa, ndi maliro, ndi njala; ndipo udzapserera ndi moto; chifukwa Ambuye Mulungu wouweruza ndiye wolimba.

9Ezk. 26.16-17Ndipo mafumu a dziko ochita chigololo nadyerera naye, adzalira nadzaulira maliro pamene aona utsi wa kutentha kwake, poima patali,

10Yes. 21.9chifukwa chakuopa chizunzo chake, nanena, Tsoka, tsoka, mudzi waukuluwo, Babiloni, mudzi wolimba! Pakuti m'ora limodzi chafika chiweruziro chanu.

11Ezk. 27.27-36Ndipo ochita malonda a m'dziko adzalira nadzauchitira chifundo, popeza palibe munthu agulanso malonda ao;

12Chiv. 17.4malonda a golide, ndi a siliva, ndi a mwala wa mtengo wake, ndi a ngale, ndi a nsalu yabafuta, ndi a chibakuwa, ndi a yonyezimira, ndi a mlangali; ndi mitengo yonse ya fungo lokoma, ndi chotengera chilichonse cha minyanga ya njovu, ndi chotengera chilichonse chamtengo wa mtengo wake wapatali, ndi chamkuwa ndi chachitsulo, ndi chansangalabwi;

13Ezk. 27.13ndi sinamoni ndi amomo, ndi zofukiza, ndi mure, ndi lubani, ndi vinyo, ndi mafuta, ndi ufa wosalala, ndi tirigu, ndi ng'ombe, ndi nkhosa; ndi malonda a akavalo, ndi a magaleta, ndi a anthu ndi a miyoyo ya anthu.

14Ndipo zokhumbitsa moyo wako zidakuchokera; ndipo zonse zolongosoka, ndi zokometsetsa zakutayikira, ndipo izi sudzazipezanso konse.

15Chiv. 18.3, 11Otsatsa izi, olemezedwa nao, adzaima patali chifukwa cha kuopa chizunzo chake, nadzalira, ndi kuchita chifundo;

16Chiv. 17.4nadzanena, Tsoka, tsoka, mudzi waukulu wovala bafuta ndi chibakuwa, ndi mlangali, wodzikometsera ndi golide ndi mwala wa mtengo wake, ndi ngale!

17Ezk. 27.27-36; Chiv. 18.10Pakuti m'ora limodzi chasanduka bwinja chuma chachikulu chotere. Ndipo watsigiro aliyense, ndi yense wakupita panyanja pakutipakuti, ndi amalinyero, ndi onse amene amachita kunyanja, anaima patali,

18Ezk. 27.27-36nafuula poona utsi wa kutentha kwake, nanena, Mudzi uti ufanana ndi mudzi waukuluwo?

19Yos. 7.6; Chiv. 18.17Ndipo anathira fumbi pamitu pao, nafuula, ndi kulira, ndi kuchita maliro, nanena, Tsoka, tsoka, mudzi waukuluwo, umene analemerezedwa nao onse akukhala nazo zombo panyanja, chifukwa cha kulemera kwake, pakuti m'ora limodzi unasanduka bwinja.

20Yer. 51.48; Luk. 11.49-50Kondwera pa iye, m'mwamba iwe, ndi oyera mtima, ndi atumwi, ndi aneneri inu; chifukwa Mulungu anauweruzira kuweruzidwa kwanu.

21 Yer. 51.63-64 Ndipo mngelo wolimba ananyamula mwala ngati mphero yaikulu, naiponya m'nyanja, nanena, Chotero Babiloni, mudzi waukulu, udzapasulidwa kolimba, ndipo sudzapezedwanso konse.

22Yer. 25.10; 33.11; Ezk. 26.13Ndipo mau a anthu oimba zeze, ndi a oimba, ndi a oliza zitoliro, ndi a oomba malipenga sadzamvekanso konse mwa iwe; ndipo mmisiri aliyense wa machitidwe ali onse sadzapezedwanso konse mwa iwe; ndi mau a mphero sadzamvekanso konse mwa iwe;

23Yer. 25.10; 33.11; Ezk. 26.13; Nah. 3.4ndi kuunika kwa nyali sikudzaunikiranso konse mwa iwe; ndi mau a mkwati ndi a mkwatibwi sadzamvekanso konse mwa iwe; pakuti otsatsa malonda anu anali omveka a m'dziko; pakuti ndi nyanga yako mitundu yonse inasokeretsedwa.

24Chiv. 17.6Ndipo momwemo munapezedwa mwazi wa aneneri ndi oyera mtima, ndi onse amene anaphedwa padziko.

Blog
About Us
Message
Site Map

Who We AreWhat We EelieveWhat We Do

Terms of UsePrivacy Notice

2025 by iamachristian.org,Inc All rights reserved.

Home
Gospel
Question
Blog
Help