1 SAMUELE Mau Oyamba - Buku Lopatulika Bible 2014

Mau OyambaBukuli likukamba za kusintha kwa zinthu m'dziko la Aisraele, kuchokera pa nthawi ya Oweruza kufikira pa nthawi yokhazikitsa ufumu. Nkhani yonse yagona pa anthu atatuwa: Samuele mweruzi omaliza, Saulo mfumu yoyamba, ndiponso Davide ndi zochita zake pa unyamata wake asanalowe ufumu.Phunziro lopezeka m'bukuli monganso m'mabuku ena osimba mbiri ya Aisraele ndi lakuti, kukhala okhulupirika kwa Mulungu kumabweretsa mtendere ndi madalitso, koma kusamvera ndi kupandukira Mulungu kumadzetsa zoipa. Awa ndi mau amene Yehova adawauza wansembe Eli, “Popeza amene andilemekeza Ine, Inenso ndidzawalemekeza iwowa, ndipo akundipeputsa Ine, adzapeputsidwa.” (2.30).Mau ena opezeka m'bukumu aonetsa kuti si Aisraele onse ankafuna kukhala ndi mfumu yowalamulira. Paja Yehova yekha anali ngati mfumu yao yeniyeni; koma chifukwa cha pempho laolo, Yehova adawasankhirabe mfumu. Chinthu chofunika chinali chakuti mfumuyo pamodzi ndi Aisraele onse amvere ulamuliro wa Mulungu ndi kutsata mau ake (2.7-10); akamatero, onse adzakhala pabwino, anthu olemera ndi osauka omwe.Za mkatimuSamuele pa ntchito yake yoweruza Aisraele 1.1—7.17

Saulo alowa ufumu 8.10—10.27

Zaka zoyamba za ufumu wa Saulo 11.1—15.35

Saulo ndi Davide 16.1—30.31

Imfa ya Saulo ndi ana ake 31.1-13

Blog
About Us
Message
Site Map

Who We AreWhat We EelieveWhat We Do

Terms of UsePrivacy Notice

2025 by iamachristian.org,Inc All rights reserved.

Home
Gospel
Question
Blog
Help