NUMERI 16 - Buku Lopatulika Bible 2014

Kora, Datani, ndi Abiramu aukira Mose

1 Yud. 11; 1Sam. 2.28 Koma Kora, mwana wa Izihara, mwana wa Kohati, mwana wa Levi, anatenga Datani ndi Abiramu, ana a Eliyabu, ndi Oni mwana wa Peleti, ana a Rubeni;

2ndipo anauka pamaso pa Mose, pamodzi ndi amuna mazana awiri mphambu makumi asanu a ana a Israele, ndiwo akalonga a khamulo, oitanidwa a msonkhano, amuna omveka.

3Ndipo anasonkhana motsutsana pa Mose ndi Aroni, nanena nao, Mukula mphamvu inu, pakuti khamu lonse nlopatulika, onsewa, ndipo Yehova ali pakati pao; mudzikuza bwanji pa msonkhano wa Yehova?

4Pamene Mose anamva ichi anagwa nkhope yake pansi;

5nanena ndi Kora ndi khamu lake lonse, ndi kuti, M'mawa Yehova adzatizindikiritsa anthu ake ndi ayani, wopatulika ndani, amene adzamsendeza pafupi pa Iye; ndi iye amene anamsankha adzamsendeza pafupi pa Iye.

6Chitani ichi; dzitengereni mbale za zofukiza, Kora, ndi khamu lake lonse;

7nimuikemo moto, muikenso chofukiza pamenepo, pamaso pa Yehova, mawa; ndipo kudzali kuti amene Yehova amsankha, wopatulika ndiye; mwakula mphamvu, inu ana a Levi.

8Ndipo Mose ananena ndi Kora, Tamvani tsono, inu ana a Levi;

9Yes. 7.13kodi muchiyesa chinthu chaching'ono, kuti Mulungu wa Israele anakusiyanitsani ku khamu la Israele, kukusendezani pafupi pa Iye, kuchita ntchito ya Kachisi wa Yehova, ndi kuima pamaso pa khamu kuwatumikira;

10ndi kuti anakusendeza iwe, ndi abale ako onse, ana a Levi, pamodzi ndi iwe? Ndipo kodi mufunanso ntchito ya nsembe?

111Ako. 3.5Chifukwa chake, iwe ndi khamu lonse mwasonkhana kutsutsana ndi Yehova; ndipo Aroniyo ndani, kuti mudandaule pa iye?

12Ndipo Mose anatuma kukaitaniza Datani ndi Abiramu, ana a Eliyabu; koma anati, Sitifikako:

13kodi ndi chinthu chaching'ono kuti watikweza kutichotsa m'dziko moyenda mkaka ndi uchi ngati madzi, kutipha m'chipululu; koma udziyesanso ndithu kalonga wa ife?

14Ndiponso sunatilowetsa m'dziko moyenda mkaka ndi uchi ngati madzi, kapena kutipatsa cholowa cha minda, ndi minda yamphesa; kodi udzakolowola amuna awa maso ao: Sitifikako.

151Sam. 12.3; Mac. 20.33Pamenepo Mose adapsa mtima, ndipo anati kwa Yehova, Musasamalira chopereka chao; sindinalanda bulu wao mmodzi, kapena kuchitira choipa mmodzi wa iwowa.

16Ndipo Mose anati kwa Kora, Iwe ndi khamu lako lonse mukhale pamaso pa Yehova mawa, iwe ndi iwowa, ndi Aroni;

17nimutenge munthu yense mbale yake yofukizamo, nimuike chofukiza m'mwemo, nimubwere nazo, yense mbale yake yofukizamo pamaso pa Yehova, mbale zofukizamo mazana awiri ndi makumi asanu; ndi iwe, ndi Aroni, yense mbale yake yofukizamo.

18Potero munthu yense anatenga mbale yake yofukizamo, naikamo moto, naikapo chofukiza, naima pa khomo la chihema chokomanako pamodzi ndi Mose ndi Aroni.

19Ndipo Kora anasonkhanitsa khamu lonse mopikisana nao ku khomo la chihema chokomanako; ndipo ulemerero wa Yehova unaoneka kwa khamu lonse.

Alangidwa oukirawo

20Ndipo Yehova ananena ndi Mose ndi Aroni, nati,

21Yer. 51.6; Mac. 2.40; Chiv. 18.4Dzipatuleni pakati pa khamu lino, kuti ndiwathe m'kamphindi.

22Gen. 18.23; 2Sam. 24.17Ndipo anagwa nkhope zao pansi, nati, Mulungu, ndinu Mulungu wa mizimu ya anthu onse, walakwa munthu mmodzi, ndipo kodi mukwiya nalo khamu lonse?

23Ndipo Yehova ananena ndi Mose, nati,

24Nena ndi khamulo, ndi kuti, Kwerani kuchoka pozungulira mahema a Kora, Datani, ndi Abiramu.

25Ndipo Mose anauka namuka kwa Datani ndi Abiramu; ndi akulu a Israele anamtsata.

26Num. 16.21Ndipo ananena ndi khamulo, nati, Chokanitu ku mahema a anthu awa oipa, musamakhudza kanthu kao kalikonse, mungaonongeke m'zochimwa zao zonse.

27Potero anakwera kuchokera pozungulira mahema a Kora, Datani, ndi Abiramu, ndipo Datani ndi Abiramu anatuluka, naima pakhomo pa mahema ao, ndi akazi ao, ndi ana ao amuna, ndi makanda ao.

28Zek. 2.9; Yoh. 5.36Ndipo Mose anati, Ndi ichi mudzadziwa kuti Yehova wanditumiza ine kuchita ntchito izi zonse, ndi kuti sizifuma m'mtima mwangamwanga.

29Akafa anthu awa monga amafa anthu onse, kapena akasungika monga amasungika anthu onse, Yehova sananditumize ine.

30Koma Yehova akalenga chinthu chatsopano, ndi nthaka ikayasama pakamwa pake, nikawameza ndi zonse ali nazo, nakatsikira iwo kumanda ali ndi moyo; pamenepo mudzadziwa kuti anthu awa anyoza Mulungu.

31Ndipo kunali, pakutha iye kunena mau awa onse, nthaka inang'ambika pansi pao;

32ndi dziko linayasama pakamwa pake ndi kuwameza, iwo ndi mabanja ao, ndi amuna ao onse akutsata Kora, ndi akatundu ao onse.

33Chomwecho iwowa, ndi onse anali nao, anatsikira kumanda ali ndi moyo, ndi dziko linasunama pa iwo, ndipo anaonongeka pakati pa msonkhano.

34Ndipo Aisraele onse akukhala pozinga pao anathawa pakumva kufuula kwao; pakuti anati, Lingatimeze dziko ifenso.

35Lev. 10.2Ndipo moto unatuluka kwa Yehova, ndi kunyeketsa amuna mazana awiri ndi makumi asanu aja akubwera nacho chofukiza.

Alanditsa mbale zofukiza za oukirawo

36Ndipo Yehova ananena ndi Mose, nati,

37Nena ndi Eleazara mwana wa Aroni wansembe, kuti aphule mbale zofukiza pakati pa moto, nutaye makalawo uko kutali: pakuti zili zopatulika;

38mbale zofukizazo za iwo amene adachimwira moyo waowao, ndipo azisule zaphanthiphanthi, zikhale chivundikiro cha guwa la nsembe; popeza anabwera nazo pamaso pa Yehova, chifukwa chake zikhala zopatulika; ndipo zidzakhala chizindikiro kwa ana a Israele.

39Ndipo Eleazara wansembe anatenga mbale zofukiza zamkuwa, zimene anthu opsererawo adabwera nazo; ndipo anazisula zaphanthiphanthi zikhale chivundikiro cha guwa la nsembe;

402Mbi. 26.18-19chikhale chikumbutso kwa ana a Israele, kuti mlendo, wosati wa mbeu ya Aroni, asasendere kuchita chofukiza pamaso pa Yehova; angakhale monga Kora ndi khamu lake; monga Yehova adanena naye ndi dzanja la Mose.

Anthu adandaula, mliri uwaononga

41Koma m'mawa mwake khamu lonse la ana a Israele anadandaula pa Mose ndi Aroni, nati, Mwapha anthu a Yehova, inu.

42Num. 16.19Ndipo kunali, posonkhanidwa khamulo kutsutsana nao Mose ndi Aroni, kuti anacheukira chihema chokomanako; taonani, mtambo unachiphimba, ndi ulemerero wa Yehova unaoneka.

43Ndipo Mose ndi Aroni anadza kukhomo kwa chihema chokomanako.

44Ndipo Yehova ananena ndi Mose, nati,

45Kwerani kuchoka pakati pa khamu lino, kuti ndiwathe m'kamphindi. Pamenepo adagwa nkhope zao pansi.

46Ndipo Mose anati kwa Aroni, Tenga mbale yako yofukiza, nuikemo moto wa ku guwa la nsembe, nuikepo chofukiza, nufulumire kumuka ku khamulo, nuwachitire chowatetezera; pakuti watuluka mkwiyo pamaso pa Yehova; wayamba mliri.

47Ndipo Aroni anatenga monga Mose adanena, nathamanga kulowa pakati pa msonkhano; ndipo taonani, udayamba mliri pakati pa anthu; ndipo anaikapo chofukiza nawachitira anthu chowatetezera.

48Eks. 20.19Ndipo anaima pakati pa akufa ndi amoyo; ndi mliri unaleka.

49Koma akufa nao mliri ndiwo zikwi khumi ndi zinai mphambu mazana asanu ndi awiri, osawerenga aja adafera chija cha Kora.

50Ndipo Aroni anabwera kwa Mose ku khomo la chihema chokomanako; ndi mliri unaleka.

Blog
About Us
Message
Site Map

Who We AreWhat We EelieveWhat We Do

Terms of UsePrivacy Notice

2025 by iamachristian.org,Inc All rights reserved.

Home
Gospel
Question
Blog
Help