1 MBIRI 11 - Buku Lopatulika Bible 2014

Davide atalowa ufumu alanda Yerusalemu

1 2Sam. 5.1-10 Pamenepo Aisraele onse anasonkhana kwa Davide ku Hebroni, ndi kuti, Taonani, ife ndife fupa lanu, ndi mnofu wanu.

2Ngakhale kale lomwe, pokhala mfumu Sauloyo, wotuluka ndi kulowa nao Aisraele ndinu; ndipo Yehova Mulungu wanu anati kwa inu, Uzidyetsa anthu anga Aisraele, nukhale mtsogoleri wa anthu anga Israele.

31Sam. 16.1, 12-13Akulu onse omwe a Israele anadza kwa mfumu ku Hebroni; ndipo Davide anapangana nao pangano ku Hebroni pamaso pa Yehova; ndipo anamdzoza Davide akhale mfumu ya Israele monga mwa mau a Yehova, ndi dzanja la Samuele.

4Namuka Davide ndi Aisraele onse naye ku Yerusalemu, ndiwo Yebusi; ndipo Ayebusi nzika za m'dziko zinali komweko.

5Ndipo nzika za m'Yebusi zinati kwa Davide, Sungalowe muno. Koma Davide analanda linga la Ziyoni, ndiwo mudzi wa Davide.

6Nati Davide, Aliyense woyamba kukantha Ayebusi, yemweyo adzakhala mkulu ndi mtsogoleri. Nayamba kukwerako Yowabu mwana wa Zeruya, nakhala mkulu iyeyu.

7Ndipo Davide anakhala m'lingamo; chifukwa chake analitcha mudzi wa Davide.

8Ndipo anamanga mudzi pozungulira pake, kuyambira ku Milo ndi pozungulira pake; ndi Yowabu anakonzanso potsala pa mudzi.

9Ndipo Davide anakulakulabe, pakuti Yehova wa makamu anali naye.

Amphamvu a Davide

10 2Sam. 23.8-39 Akulu a amphamvu aja Davide anali nao akulimbika pamodzi naye m'ufumu wake, pamodzi ndi Aisraele onse, kumlonga ufumu, monga mwa mau a Yehova akunena za Israele, ndi awa.

11Kuwerenga kwa amphamvu aja Davide anali nao ndi uku: Yasobeamu mwana wa Muhakimoni, mkulu wa makumi atatu aja, anasamulira mazana atatu mkondo wake, nawapha nthawi imodzi.

12Ndi pambuyo pake Eleazara mwana wa Dodo Mwahohi, ndiye mmodzi wa atatu aja amphamvu.

13Anali pamodzi ndi Davide ku Pasidamimu muja; Afilisti anasonkhanako kunkhondo kumene kunali munda wodzala ndi barele; ndipo anthu anathawa pamaso pa Afilisti.

14Koma anadziimika pakati pa munda, naulanditsa, nakantha Afilisti; m'mwemo anawapulumutsa Yehova ndi chipulumutso chachikulu.

152Sam. 23.13-18Ndipo atatu a akulu makumi atatu anatsikira kuthanthwe kwa Davide, ku phanga la Adulamu; ndi nkhondo ya Afilisti idamanga misasa m'chigwa cha Refaimu.

16Pamenepo Davide anali m'linga, ndi boma la asilikali a Afilisti linali ku Betelehemu.

17Ndipo Davide analakalaka, nati, Ha? Mwenzi wina atandimwetsa madzi a m'chitsime cha ku Betelehemu chili kuchipata.

18Napyola atatuwo misasa ya Afilisti natunga madzi ku chitsime cha ku Betelehemu chili kuchipata, nabwera nao kwa Davide; koma Davide anakana kumwako, koma anawathirira kwa Yehova;

19nati, Pali Mulungu wanga, kukhale kutali kwa ine kuchita ichi. Ngati ndidzamwa mwazi wa anthu awa? Akadataya moyo wao, inde akadataya moyo wao, pakukatenga madziwa. M'mwemo sanafune kuwamwa. Izi anazichita atatu amphamvuwa.

202Sam. 23.18Ndipo Abisai mbale wa Yowabu, ndiye wamkulu wa atatuwa; pakuti anasamulira mazana atatu mkondo wake, nawapha, namveka dzina pakati pa atatuwa.

21Mwa atatuwa iye anali waulemu woposa awiriwa, nasanduka mkulu wao; koma sanafike pa atatu oyamba aja.

222Sam. 23.20-23Benaya mwana wa Yehoyada, mwana wa ngwazi ya ku Kabizeeli, wochita zachikulu, anapha ana awiri a Ariyele wa ku Mowabu; anatsikanso, napha mkango m'kati mwa dzenje nyengo ya chipale chofewa.

23Anaphanso Mwejipito munthu wamkulu, msinkhu wake mikono isanu, ndi m'dzanja la Mwejipito munali mkondo ngati mtanda woombera nsalu; ndipo anamtsikira ndi ndodo, nakwatula mkondo m'dzanja la Mwejipito, namupha ndi mkondo wake womwe.

24Izi anazichita Benaya mwana wa Yehoyada, namveka dzina mwa atatu amphamvuwo.

25Taonani, anali wa ulemu woposa makumi atatuwo, koma sanafike pa atatu oyamba aja; ndipo Davide anamuika mkulu wa olindirira ake.

26 2Sam. 23.24 Ndipo amphamvuwo a magulu a nkhondo ndiwo Asahele mbale wa Yowabu, Elihanani mwana wa Dodo wa ku Betelehemu,

27Samoti Muharodi, Helezi Mpeloni,

28Ira mwana wa Ikesi wa ku Tekowa, Abiyezere wa ku Anatoti,

29Sibekai Muhusa, Ilai Mwahohi,

30Maharai Mnetofa, Heledi mwana wa Baana Mnetofa,

31Itai mwana wa Ribai wa Gibea wa ana a Benjamini, Benaya Mpiratoni,

32Hurai wa ku mitsinje ya Gaasi, Abiyele Mwarabati,

33Azimaveti Mbaharumi, Eliyaba Msaaliboni;

34ana a Hasemu Mgizoni; Yonatani mwana wa Sage Muharari,

35Ahiyamu mwana wa Sakara Muharari, Elifala mwana wa Uri,

36Hefere Mmekerati, Ahiya Mpeloni,

37Heziro wa ku Karimele, Naarai mwana wa Ezibai,

38Yowele mbale wa Natani, Mibara mwana wa Hagiri,

39Zeleki Mwamoni, Naharai Mbeeroti wonyamula zida za Yowabu mwana wa Zeruya,

40Ira Mwitiri, Garebu Mwitiri,

41Uriya Muhiti, Zabadi mwana wa Alai,

42Adina mwana wa Siza Mrubeni mkulu wa Arubeni, ndi makumi atatu pamodzi naye,

43Hanani mwana wa Maaka, ndi Yosafati Mmitini,

44Uziya Mwasiterati, Sama ndi Yeiyele ana a Hotamu wa ku Aroere,

45Yediyaele mwana wa Simiri, ndi Yoha mbale wake Mtizi,

46Eliyele Mmahavi, ndi Yeribai ndi Yosaviya ana a Elinaamu, ndi Itima Mmowabu,

47Eliyele, ndi Obedi, ndi Yaasiyele Mmezobai.

Blog
About Us
Message
Site Map

Who We AreWhat We EelieveWhat We Do

Terms of UsePrivacy Notice

2025 by iamachristian.org,Inc All rights reserved.

Home
Gospel
Question
Blog
Help