1 Est. 2.23 Usiku uja tulo tidamwazikira mfumu, niti abwere nalo buku la mbiri, naliwerenga pamaso pa mfumu.
2Napeza mudalembedwa kuti Mordekai adawulula za Bigitana ndi Teresi, awiri a adindo a mfumu osunga pakhomo, amene adayesa kumthira manja mfumu Ahasuwero.
3Niti mfumu, Anamchitira Mordekai ulemu ndi ukulu wotani chifukwa cha ichi? Ndipo anyamata a mfumu akuitumikira ananena nayo, Sanamchitire kanthu.
4Niti mfumu, Ali kubwalo ndani? Koma Hamani adalowa m'bwalo lakunja la nyumba ya mfumu kulankhula ndi mfumu za kupachika Mordekai pamtengo adaukonzeratu.
5Ndipo anyamata a mfumu ananena nayo, Taonani, Hamani alikuima pabwalo. Niti mfumu, Alowe.
6Nalowa Hamani. Ndipo mfumu inati kwa iye, Kodi amchitire chiyani munthu amene mfumu ikondwera kumchitira ulemu? Ndipo Hamani anati mumtima mwake, Ndaniyo mfumu ikondwera kumchitira ulemu koposa ine?
7Nati Hamani kwa mfumu, Munthu amene mfumu ikondwera kumchitira ulemu,
81Maf. 1.33amtengere chovala chachifumu amachivala mfumu, ndi kavalo amakwerapo mfumu, naike korona wachifumu pamutu pake,
9Gen. 41.43napereke chovala ndi kavalo m'dzanja la wina womveketsa wa akalonga a mfumu, naveke nacho munthu amene mfumu ikondwera kumchitira ulemu, namuyendetse pa kavaloyo m'khwalala la m'mudzi, nafuule pamaso pake, Azitero naye munthu amene mfumu ikondwera kumchitira ulemu.
10Pamenepo mfumu inati kwa Hamani, Fulumira, tenga chovala ndi kavalo monga umo wanenera, nuchitire chotero Mordekai Myudayo, wokhala pa chipata cha mfumu; kasasowepo kanthu ka zonse wazinena.
11Ndipo Hamani anatenga chovala ndi kavalo, naveka Mordekai, namuyendetsa pa kavalo m'khwalala la m'mudzi, nafuula pamaso pake, Azitero naye munthu amene mfumu ikondwera kumchitira ulemu.
122Mbi. 26.20; 2Sam. 15.30Ndipo Mordekai anabweranso kuchipata cha mfumu. Koma Hamani anafulumira kunka kwao, wachisoni ndi wofunda mutu wake.
13Ndipo Hamani anafotokozera Zeresi mkazi wake, ndi mabwenzi ake onse, zonse zidamgwera. Nanena naye anzeru ake, ndi Zeresi mkazi wake, Mordekai amene wayamba kutsika pamaso pake, akakhala wa mbumba ya Ayuda, sudzamlaka; koma udzagwada pamaso pake.
14Est. 5.8Akali chilankhulire naye, anafika adindo a mfumu, nafulumira kumtenga Hamani kunka naye kumadyerero adawakonzera Estere.
Who We AreWhat We EelieveWhat We Do
2025 by iamachristian.org,Inc All rights reserved.