YEREMIYA 34 - Buku Lopatulika Bible 2014

Zedekiya adzatengedwa, Yerusalemu adzalandidwa

1 2Maf. 25 Mau amene anadza kwa Yeremiya kuchokera kwa Yehova, pamene Nebukadinezara mfumu ya Babiloni, ndi nkhondo yake yonse, ndi maufumu onse a dziko lapansi amene anagwira mwendo wake, ndi anthu onse, anamenyana ndi Yerusalemu, ndi midzi yake yonse, akuti:

2Yer. 32.28-29Yehova Mulungu wa Israele atero, Pita, nena kwa Zedekiya mfumu ya Yuda, numuuze iye, kuti Yehova atero, Taona, ndidzapereka mudziwu m'dzanja la mfumu ya ku Babiloni, ndipo adzautentha ndi moto;

3Yer. 32.4ndipo iwe sudzapulumuka m'dzanja lake, koma udzagwiridwadi, nudzaperekedwa m'dzanja lake; ndipo maso ako adzaonana nao a mfumu ya ku Babiloni, ndipo iye adzanena nawe pakamwa ndi pakamwa, ndipo udzanka ku Babiloni.

4Koma tamva mau a Yehova, iwe Zedekiya mfumu ya Yuda; Yehova atero za iwe, Sudzafa ndi lupanga;

52Mbi. 16.14udzafa ndi mtendere; ndipo adzawambika iwe monga anawambika makolo ako, mafumu akale usanakhale iwe; ndipo adzakulirira iwe, kuti, Kalanga ine ambuye! Pakuti ndanena mau, ati Yehova.

6Ndipo Yeremiya mneneri ananena mau onsewa kwa Zedekiya mfumu ya Yuda m'Yerusalemu,

72Maf. 18.13pamene nkhondo ya mfumu ya ku Babiloni inamenyana ndi Yerusalemu, ndi midzi yonse ya Yuda imene inatsala, ndi Lakisi ndi Azeka; pakuti midzi ya Yuda yamalinga yotsala ndi imeneyi.

Oyesa abale ao akapolo aopsedwa

8 Eks. 21.2 Mau amene anadza kwa Yeremiya kuchokera kwa Yehova, mfumu Zedekiya atapangana pangano ndi anthu onse amene anali pa Yerusalemu, kuti awalalikire iwo ufulu;

9Neh. 5.11kuti yense ammasule kapolo wake wamwamuna, ndi wamkazi, pokhala iye Muhebri wamwamuna kapena wamkazi, kuti yense asayese Myuda mnzake kapolo wake;

10ndipo akulu onse ndi anthu onse anamvera, amene anapangana mapangano, akuti yense ammasule kapolo wake wamwamuna, kapena wamkazi osawayesanso akapolo; iwo anamvera nawamasula;

11koma pambuyo pake anabwerera, nabweza akapolo ake aamuna ndi aakazi, amene anawamasula, nawagonjetsanso akhale akapolo aamuna ndi aakazi;

12chifukwa chake mau a Yehova anadza kwa Yeremiya kuchokera kwa Yehova, kuti,

13Yehova Mulungu wa Israele atero: Ndinapangana mapangano ndi makolo anu tsiku lija ndinawatulutsa m'dziko la Ejipito, kutuluka m'nyumba ya ukapolo, kuti,

14Deut. 15.12Zitapita zaka zisanu ndi ziwiri mudzaleka amuke yense mbale wake amene ali Muhebri, amene anagulidwa ndi inu, amene anakutumikirani inu zaka zisanu ndi chimodzi, mudzammasule akuchokereni; koma makolo anu sanandimvere Ine, sananditchere Ine khutu.

152Maf. 23.3Ndipo mwabwerera inu tsopano, ndi kuchita chimene chili cholungama pamaso panga, pakulalikira ufulu yense kwa mnzake; ndipo munapangana pangano pamaso panga m'nyumba imene itchedwa dzina langa;

16Lev. 19.12koma mwabwerera ndi kuipitsa dzina langa, ndi kubwezera m'ukapolo yense kapolo wake wamwamuna, ndi wamkazi, amene munammasula akachite zao, ndipo munawagonjetsa, akhale akapolo anu aamuna ndi aakazi.

17Mat. 7.2; Agal. 6.7; Yak. 2.13Chifukwa chake Yehova atero: Simunandimvera Ine, kuti mulalikire ufulu, munthu yense kwa mbale wake, ndi munthu yense kwa mnzake; taonani, ndilalikira kwa inu ufulu, ati Yehova, wa kulupanga, kuchaola, ndi kunjala; ndipo ndidzakuperekani mukhale oopsetsa m'maufumu onse a dziko lapansi.

18Gen. 15.10, 17Ndipo ndidzapereka anthu akulakwira pangano langa, amene sanachite mau a pangano limene anapangana pamaso panga, muja anadula pakati mwanawang'ombe ndi kupita pakati pa mbali zake;

19akulu a Yuda, ndi akulu a Yerusalemu, adindo, ndi ansembe, ndi anthu onse a m'dziko, amene anapita pakati pa mbali za mwanawang'ombe;

20ndidzapereka iwo m'dzanja la adani ao, ndi m'dzanja la iwo akufuna moyo wao; ndipo mitembo yao idzakhala chakudya cha mbalame za mlengalenga, ndi cha zilombo za pa dziko lapansi.

21Ndipo Zedekiya mfumu ya Yuda ndi akulu ake ndidzawapereka m'dzanja la adani ao, ndi m'dzanja la akufuna moyo wao, ndi m'dzanja la nkhondo ya mfumu ya ku Babiloni, imene yakuchokereani.

22Yer. 39.1-2, 8Taonani, ndidzauza, ati Yehova, ndidzabwezera iwo kumudzi uno; ndipo adzamenyana nao, nadzaulanda, nadzautentha ndi moto; ndipo ndidzayesa midzi ya Yuda mabwinja, palibenso wokhalamo.

Blog
About Us
Message
Site Map

Who We AreWhat We EelieveWhat We Do

Terms of UsePrivacy Notice

2025 by iamachristian.org,Inc All rights reserved.

Home
Gospel
Question
Blog
Help